N’zotheka Ndithu Kuti Amene Ali Kumanda Adzakhalenso ndi Moyo
N’zotheka Ndithu Kuti Amene Ali Kumanda Adzakhalenso ndi Moyo
ZAKA zambiri zapitazo, m’filimu inayake anasonyeza mnyamata wina ataimirira pafupi ndi manda a munthu amene iye ankamukonda. Mnyamatayu anati: “Mayi ankandiuza kuti moyo ndi wotero, anthufe timabadwa ndi kufa.” Kenako, pamene m’filimuyo anasonyeza pamandapo kwa kanthawi, mnyamatayo anati: “Ndikanakonda kwambiri ngati moyo sunali wotero.”
Maganizo amenewa ndi amenenso ali ndi anthu ambirimbiri omwe achibale awo anamwalira. Imfa ndi mdani woopsa kwambiri. Ngakhale zili choncho, Mulungu walonjeza kuti: “Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.” (1 Akorinto 15:26) Nanga n’chifukwa chiyani anthufe timafa, pamene zikuoneka kuti ubongo wathu unapangidwa moti tikhoza kukhala ndi moyo wamuyaya? Kodi imfa idzawonongedwa bwanji?
N’chifukwa Chiyani Timakalamba ndi Kufa?
Ponena za Mlengi wathu, Yehova Mulungu, Baibulo limati: “Ntchito yake ndi yangwiro.” (Deuteronomo 32:4; Salmo 83:18) Munthu woyamba Adamu analengedwa wangwiro, ndipo akanatha kukhala ndi moyo wosatha mu Edene, munda wa paradaiso umene Mulungu anamuikamo. (Genesis 2:7-9) Kodi chinachitika n’chiyani kuti Adamu asakhalenso m’Paradaiso ameneyu ndiponso kuti akalambe ndi kufa?
Yankho lake ndi losavuta: Adamu sanamvere lamulo lakuti asadye chipatso cha mtengo winawake. Mulungu anali atachenjeza Adamu mosapita m’mbali za chilango cha kusamvera, kuti: ‘Udzafa ndithu.’ (Genesis 2:16, 17) Adamu anatsatira mkazi wake Hava, posamvera lamulolo, choncho Mulungu anawathamangitsa m’munda wa Edene. Pali chifukwa chachikulu chimene Mulungu anachitira zimenezi mwamsanga. Baibulo limati: “Kuti [Adamu] asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo [m’mundamo], ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse.”—Genesis 3:1-6, 22.
Adamu ndi Hava anafa chifukwa cha kusamvera kwawo. Koma nanga n’chifukwa chiyani ife tonse, ana awo, timakalamba ndi kufa? N’chifukwa chakuti tinatengera uchimo kwa Adamu, ndipo chifukwa cha uchimowo, ana ake tonsefe ndi opanda ungwiro ndipo timafa. Baibulo limafotokoza kuti: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo, imfayo nifalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’—Aroma 5:12.
N’zotheka Kudzakhalanso ndi Moyo
Malinga ndi zimene tawerenga poyamba paja, ‘imfa idzawonongedwa,’ inde, idzachotsedwa moti sidzakhalakonso. (1 Akorinto 15:26) Kodi zidzatheka bwanji zimenezi? Baibulo limayankha funso limeneli, kuti: “Mwa kuchita chinthu chimodzi cholungamitsa, anthu kaya akhale a mtundu wotani, akuyesedwa olungama kuti akhale ndi moyo.” (Aroma 5:18) Kodi n’chiyani chimene chimathandiza anthu kuti akhale olungama kwa Mulungu ndi kulandira moyo wosatha?
Ndi zimene Mulungu wachita kuti achotse uchimo umene anthu onse anatengera kwa munthu woyamba, Adamu. Baibulo limati: “Mphatso imene Mulungu amapereka ndiyo moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Ponena za mphatso imeneyi yothandiza anthu kuti ayesedwe olungama n’kukhala ndi moyo, Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko [kutanthauza anthu] mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Mukhoza kuona kuti chikondi cha Mulungu komanso cha Mwana wake Yesu Khristu, yemwe anazunzika kwambiri chifukwa cha ifeyo, n’chachikulu kwambiri. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Agalatiya 2:20) Koma n’chifukwa chiyani Yesu ndiye munthu yekhayo amene ‘akanapereka moyo wake dipo’ m’malo mwa ife, ndi kutipulumutsa ku uchimo ndi mavuto ake onse?—Mateyo 20:28.
Yesu ndi amene akanatha kupereka moyo wake dipo chifukwa ndi munthu yekhayo amene sanalandire uchimo kuchokera kwa munthu woyamba, Adamu. N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chakuti moyo wa Yesu unasamutsidwa mozizwitsa kuchoka kumwamba n’kuikidwa m’mimba mwa Mariya, yemwe anali namwali. Choncho, mogwirizana ndi zimene mngelo anauza Mariya, mwana wakeyo anali “woyera, Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:34, 35) N’chifukwa chake Yesu amatchedwa “Adamu womalizira” ndiponso n’chifukwa chake sanatengere uchimo kwa “munthu woyambirira, Adamu.” (1 Akorinto 15:45) Pokhala munthu wopanda uchimo, Yesu anatha kudzipereka kukhala “dipo lolinganiza.” Izi zili choncho chifukwa moyo wake unali wolingana kapena kuti wofanana ndi wa munthu woyamba, amene pa nthawi ina anali wangwiro ndi wopanda uchimo.—1 Timoteyo 2:6.
Mwa kupereka dipo limeneli, Mulungu anatipatsa mwayi wakuti ife tilandire moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi, umene Adamu woyambirira anautaya. Komabe kuti anthu ena ambiri adzalandire madalitso amenewa, adzafunika kuukitsidwa. Chimenechi ndi chiyembekezo chabwino kwambiri. Koma kodi zimenezi zingathekedi?
Chifukwa Chake Tiyenera Kukhulupirira
Kodi zimativuta kukhulupirira kuti Yehova Mulungu, amene analenga moyo, ali ndi mphamvu yolenganso munthu amene anamwalira? Taganizirani mphamvu ya kubereka imene Mulungu anapatsa mkazi woyamba. “Mwamunayo [Adamu] anadziwa mkazi wake Hava,” ndipo patatha miyezi 9, kamwana kofanana ndi iwowo, kosaperewera chilichonse, kanabadwa. (Genesis 4:1) Zimene zinkachitika m’mimba mwa Hava pamene ziwalo zonse za mwanayo zinali kulengedwa ndi kuikidwa m’malo mwake ndi chinsinsi komanso ndi zozizwitsa mpaka pano, ndipo palibe munthu amene angazimvetse.—Salmo 139:13-16.
Popeza kuti ana ambirimbiri amabadwa tsiku lililonse, anthu ambiri saona kuti kubereka ndi chinthu chozizwitsa. Ngakhale zili choncho, ambiri amaona kuti n’zosatheka kubwezeretsa moyo wa munthu amene anamwalira. Yesu atauza anthu amene anali kulira pamaliro a kamtsikana kuti asiye kulirako, iwo “anayamba kum’seka monyodola” chifukwa ankadziwa kuti kamtsikanako kamwalira. Koma Yesu ananena kwa kamtsikanako kuti, “‘Dzuka!’ Ndipo nthawi yomweyo buthulo linadzuka ndi kuyamba kuyenda.” Kenako, timawerenga kuti: “Pamenepo [anthu omwe analipo] anasangalala kwadzaoneni.”—Maliko 5:39-43; Luka 8:51-56.
Yesu atalamula kuti anthu atsegule manda a bwenzi lake Lazaro, Marita, mlongo wa Lazaro, anatsutsa ndipo anati: “Pano ayenera kuti wayamba kununkha, pakuti lero ndi tsiku lachinayi chimuikireni m’manda.” Koma zinali zosangalatsa kwambiri Yesu ataukitsa Lazaro n’kukhalanso ndi moyo. (Yohane 11:38-44) Anthu ambiri anadziwa zozizwitsa zimene Yesu anali kuchita. Pamene Yohane Mbatizi anali m’ndende, ophunzira a Yohaneyo anamuuza zomwe Yesu anali kuchita, kuti: “Akufa akuukitsidwa.”—Luka 7:22.
Akufa Adzaukitsidwa N’kukhalanso ndi Moyo
N’chifukwa chiyani Yesu anachita zozizwitsa zimenezi, pamene anthu oukitsidwawo anadwala ndi kumwaliranso? Anachita zimenezi pofuna kusonyeza kuti moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi, umene Adamu woyambirira anautaya, ungabwezeretsedwe ndipo zidzatero kumene. Kuukitsa akufa kumene Yesu anachita kunasonyeza kuti anthu ambirimbiri “adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
Ubwino wake ndi wakuti ifenso tingakhale ndi chiyembekezo chosangalatsa chokhala ndi moyo wosatha ngati tikhala ‘odzipereka kwa Mulungu.’ Baibulo limati kudzipereka kumeneku “kuli ndi lonjezo la moyo uno ndi umene ukubwerawo.” ‘Moyo umene ukubwerawo’ umatchedwanso “moyo weniweniwo.”—1 Timoteyo 4:8; 6:19.
Tsopano tiyeni tione mmene moyo weniweniwo, moyo umene ukubwerawo m’dziko latsopano lolungama, udzakhalira.
[Chithunzi patsamba 6]
“Anthuwo anasangalala kwadzaoneni”