“Sindinkadziwa Kuti Mulungu Ali ndi Dzina”
“Sindinkadziwa Kuti Mulungu Ali ndi Dzina”
▪ Mayi wina ananena zimenezi atawerenga buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Iye ananenanso kuti: “Koma n’zomveka kuti Mulungu akhale ndi dzina. Nditafufuza dzina la Mulungu m’Baibulo langa, ndinapeza kuti lilimo.” Mayiyu anati: “Ndinali ndisanawerengepo buku lofotokoza Baibulo lothandiza ndi losavuta kumva ngati limeneli.”
Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani silimangosonyeza kuti cholinga cha Mulungu kuchokera pachiyambi ndi chakuti dziko lapansi likhale paradaiso, koma limanenanso momveka bwino mmene iye adzakwaniritsire cholingacho. Bukuli limafotokoza udindo waukulu umene Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, ali nawo pokwaniritsa cholinga chimenechi. Lili ndi mfundo za m’Baibulo zosonyeza chifukwa chake timakalamba ndi kufa, chifukwa chimene Mulungu walolera kuvutika, ndiponso mmene Ufumu wa Mulungu udzathetsere mavuto onse.
Ngakhale kuti pangopita zaka zitatu kuyambira pamene buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani linafalitsidwa, mabuku oposa 79 miliyoni asindikizidwa m’zinenero 220. Ngati mukufuna kuitanitsa bukuli, lembani m’mizere ili pansiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire buku limene lasonyezedwa panoli.
□ Lembani chinenero chimene mukufuna.