Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
Zinachitikira Kuti?
1. Kodi ndi mumtsinje uti umene Mose akadali khanda anamupeza?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Eksodo 2:1-10.
Pamapu awa lembani mzere wozungulira yankho lanu.
Firate
Yordano
Nile
▪ Kodi ndani amene ankayang’anira Mose ataima chapatali?
․․․․․
▪ Kodi ndani amene anapeza Mose akuyandama mumtsinje?
․․․․․
▪ Kodi ndani anasankhidwa kuti azilera Mose?
․․․․․
KAMBIRANANI:
Kodi mlongo wa Mose anasonyeza makhalidwe otani? Ngati muli ndi m’bale kapena mlongo wanu, kodi mungamutsanzire bwanji mlongo wa Mose?
Kuchokera M’magazini Ino
Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowa.
TSAMBA 8 Kodi munthu aliyense wochenjera amatani? Miyambo 13:․․․․․
TSAMBA 8 Kodi chingachitike n’chiyani mukamakhala panokha? Miyambo 18:․․․․․
TSAMBA 9 Kodi mayi wabwino amatani? Miyambo 31:․․․․․
TSAMBA 9 N’chifukwa chiyani muyenera kuyesetsa kukhala ndi luso la kulingalira? Miyambo 2:․․․․․
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?
Onani zokuthandizani kupeza yankho. Onaninso malembawo. Kenaka lembani mayina olondola pa mizereyi.
2. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Ndinakanthidwa ndi khate chifukwa ndinafuna kupereka nsembe yofukiza paguwa la nsembe la Yehova.
Werengani 2 Mbiri 26:16-19.
3. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Ndinali mfumu yabwino ndipo ndinamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova.
Werengani 2 Mbiri 27:1-4.
4. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Ndinapsereza ana anga nsembe m’Chigwa cha Hinomu.
Werengani 2 Mbiri 28:1, 3, 4.
▪ Mayankho ali pa tsamba 12
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
1. Nile.
▪ Mlongo wa Mose.
▪ Mwana wamkazi wa Farao.
▪ Mayi a Mose.
2. Uziya.—Mateyo 1:8.
3. Yotamu.—Mateyo 1:9.
4. Ahazi.—Mateyo 1:9.