Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Njati za ku Ulaya Zapulumuka Lokumbakumba

Njati za ku Ulaya Zapulumuka Lokumbakumba

Njati za ku Ulaya Zapulumuka Lokumbakumba

YOLEMBEDWA KU POLAND

Osaka nyama anasangalala kwambiri atapeza mapazi a nyama imene anali kufunafuna. Atapitirizabe kuyenda, mwadzidzidzi anaona nyama imene ankaitsatira itaima cha apo. Ubweya wake unali woderapo ndipo ndevu zake zinali zakuda, nyanga zake zopindikira mkati zitaima pamutu pake. Osaka nyamawo anadziwa kuti anthu amafuna kwambiri nyama yake ndi chikopa, ndipo akaipha apanga ndalama zambiri.

Iwo atawombera koyamba nyamayo, anangoivulaza ndipo inathawira m’nkhalango kukabisala koma sizinathandize. Ataiwomberanso kachiwiri, nyama yolemera makilogalamu 500 imeneyi inagwa pansi kuti phii, n’kuferatu. Osaka nyamawo sanadziwe kuti zimene achitazo zidzapanga mbiri m’tsogolo. Zimenezi zinachitika mu April 1919, ndipo anthuwo anali atapha njati yakutchire, yomwe inali njati ya ku Ulaya yomaliza yokhala m’zigwa za ku Poland. Mwamwayi, panthawiyo n’kuti njati zina zamtunduwu zili m’malo osungirako nyama a boma ndi a anthu.

KALE, njati za ku Ulayazi (Bison bonasus), zimene zimatchedwanso kuti wisent, zinkapezeka zochuluka m’madera ambiri a ku Ulaya. Njati yaikulu yamphongo imatha kulemera makilogalamu 900 ndipo imatha kutalika mamita awiri mbali yakutsogolo. Anthu amanena kuti nyama zazikuluzi ndi mafumu a m’nkhalango.

Maonekedwe a njatiyi ndi ochititsa chidwi. Thupi lake ndi laling’ono kumbuyo poyerekeza ndi kutsogolo kwake. Mapewa ake ndi aakulu kwambiri ndipo ili ndi linunda lalikulu kwambiri. Mbali yakumbuyo imakhala ndi ubweya waufupi, pamene mbali yakutsogolo imakhala ndi ubweya wautali wanyankhalala ndiponso imakhala ndi ndevu.

Zinatsala Pang’ono Kutha

Masiku ano akuti njati za ku Ulaya zomwe zilipo ndi zikwi zowerengeka chabe. Kale ulimi ndi kudula mitengo mwachisawawa zinalanda malo awo okhala, ndipo osaka nyama ankazipha kwambiri. Pofika zaka za m’ma 700, njati za ku Ulayazi zomwe zinali ku Gaul (kumene masiku ano ndi dera la France ndi Belgium) zinali zitatheratu.

M’zaka za m’ma 1500, mafumu a ku Poland anayesetsa kuteteza nyamazi. Mfumu yoyamba kuchita zimenezi inali Sigismund II Augustus, yomwe inalamula kuti aliyense wopha njatizi azilandira chilango cha imfa. Anatero chifukwa chiyani? Dr. Zbigniew Krasiński, wa ku Białowieza National Park, anati: “Cholinga poteteza nyamazo chinali chakuti mafumu ndi nduna zawo azizisaka.” Ngakhale kuti anaika chilango chokhwimachi, sizinathandize poteteza njati zakutchirezi. Ndipo pofika kumapeto kwa zaka za m’ma 1700, njati za ku Ulaya zinkapezeka ku Nkhalango ya Białowieza kum’mawa kwa Poland ndi ku Caucasia basi.

M’zaka za m’ma 1800, zinthu zinayamba kuwongokera. Ufumu wa Russia utalanda Nkhalango ya Białowieza, Mfumu Alexander I inakhazikitsa lamulo loteteza njati za ku Ulaya. Zotsatira zake sizinachedwe kuonekera. Chiwerengero cha njatizi chinayamba kuwonjezereka, ndipo pofika mu 1857, boma linkasamalira njati za ku Ulaya pafupifupi 1,900. Kenako anakonza malo odyetsera njatizi m’nyengo yozizira. Anakonzanso maiwe oti njatizi zizimwako madzi komanso analambula malo oti azilimapo zakudya zake.

Koma n’zachisoni kuti mtendere umene njatizi zinapeza sunakhalitse. M’zaka 60 zokha, chiwerengero cha njatizi chinatsika ndi theka. Nkhondo yoyamba ya padziko lonse itaulika, mavuto a njati zakutchire za ku Poland anafika pachimake. Ngakhale kuti boma la Germany linapereka lamulo “loteteza njatizi kuti mibadwo ya m’tsogolo izidzaona chilengedwe chapaderachi,” asilikali a Germany obwerera kwawo pothawa nkhondo, asilikali a Russia omenyana ndi Germany, ndiponso anthu osaka nyama, anasakaza njatizi. Monga tafotokozera poyamba paja, mu 1919 njati ya ku Ulaya yomaliza yokhala m’tchire ku Poland inaphedwa.

Kupulumuka Lokumbakumba

Pofuna kupulumutsa nyamazi, bungwe la International Society for the Protection of the European Bison linakhazikitsidwa mu 1923. Cholinga chake choyamba chinali kupeza chiwerengero cha njati zomwe zinali kusungidwa zosasakanikirana mtundu. * Bungweli linapeza kuti padziko lonse lapansi pali njati za ku Ulaya zoterezi za m’zigwa zokwana 54, zomwe zinali m’malo osungira nyama osiyanasiyana. Koma sikuti zonse zinali zoyenera kubereka. Zina zinali zokalamba, zina zodwala. Pamapeto pake, njati 12 zinasankhidwa kuti zithandize kuwonjezera chiwerengero cha njatizi. Akuti njati zonse za ku Ulaya za m’zigwa zomwe zilipo zinachokera ku zisanu mwa njatizo.

Chakumapeto kwa 1929, panachitika zinthu zosangalatsa kwambiri chifukwa njati ziwiri za ku Ulaya za m’zigwa anazibwezera m’tchire. Izo zinaikidwa m’malo apadera kwambiri mu Nkhalango ya Białowieza. Patadutsa zaka 10, chiwerengero chake chinakwera kufika 16.

Kodi Zapulumutsidwadi?

Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 2000, panali njati za ku Ulaya pafupifupi 2,900 padziko lonse. Ku Poland kunali njati pafupifupi 700. M’zaka zaposachedwapa, mayiko monga Belarus, Kyrgyzstan, Lithuania, Russia ndi Ukraine, akhalanso akusunga nyamazi.

Koma zimenezi sizikutanthauza kuti njati za ku Ulaya zasiya kukumana ndi mavuto. Nyamazi zikukumana ndi mavuto monga tizilombo, matenda, kusowa kwa chakudya ndi madzi komanso anthu opha nyamazi. Vutonso lalikulu ndilo kupunduka chifukwa cha kuchepa kwa majini ena m’thupi la nyamazi. Pazifukwa zimenezi, njati za ku Ulaya zidakali pa mndandanda wa nyama ndi zomera zomwe zatsala pang’ono kutha padziko lonse.

Khama la anthu poteteza nyamazi lathandiza kuti zifike m’nthawi yathu. Ngakhale zili choncho, Dr. Krasiński, amene tamutchula poyamba uja, akutikumbutsa kuti “tsoka la njati za ku Ulaya ndi chitsanzo cha mmene panthawi yochepa chabe, mtundu wa nyama ungatsalire pang’ono kutha kenako n’kudzapulumutsidwa pambuyo pochita khama nthawi yaitali.” Tsogolo la njatizi ndi nyama zina zambiri silikudziwika. Koma panopa, “mafumu a m’nkhalango” amenewa apulumuka lokumbakumba.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Pali mitundu iwiri ya njati za ku Ulaya, ndipo mitunduyi ndi njati za m’zigwa ndiponso njati za ku Caucasia, kapena kuti za m’mapiri. Njati yomaliza ya ku Caucasia inafa mu 1927. Koma m’mbuyomo, njati ina yamphongo yamtundu umenewu anaiika pamodzi ndi njati yaikazi ya m’zigwa, ndipo panabadwa mwana wosakanikirana mtundu. Njati zosakanikirana mtundu za ku Caucasia zimenezi zidakalipo ndithu.

[Zithunzi patsamba 10]

Njati za ku Ulaya ku Białowieza National Park

[Mawu a Chithunzi]

All photos: Białowieski Park Narodowy