Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupereka Chinthu Chofunika Kwambiri kwa Anthu

Kupereka Chinthu Chofunika Kwambiri kwa Anthu

Kupereka Chinthu Chofunika Kwambiri kwa Anthu

PAMOYO wa munthu, mpweya wabwino, chakudya komanso madzi si zokwanira. Koma kuti anthu akhaledi osangalala amafunikira kupeza zosowa zawo zauzimu. Tiyenera kudziwa cholinga cha Mulungu polenga zamoyo komanso chifukwa chimene anatilengera ifeyo. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyo 5:3.

N’zotheka kupeza zosowa zimenezi chifukwa Mulungu watipatsa Baibulo, lomwe ndi buku lopatulika ndipo limapezeka padziko lonse lapansi m’zilankhulo pafupifupi 2,400. (2 Timoteyo 3:16) Baibulo limatiuza kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse kuphatikizapo zamoyo zonse za padziko pano. (Genesis chaputala 1 ndi 2) Limanenanso kuti anachita zimenezi m’masiku 6. Awa si masiku enieni koma akuimira zigawo za nthawi imene Mulungu analengera zinthu. Ndipo nthawi imeneyi imagwirizana ndi nthawi imene asayansi amatchula akamanena zaka zimene dziko lakhalapo.

Baibulo limanenanso zimene Mulungu akufuna kudzawachitira anthu. Zimenezi zinatchulidwa pa Salmo 37:29. Lembali limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Lembali likusonyeza kuti anthu olungama kapena kuti amene amatsatira mfundo za m’Baibulo adzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi pompano, osati kumwamba. Koma panthawiyo dzikoli lidzakhala litakonzedwa bwino kwambiri. Dziko lonseli lidzakhala paradaiso.—Salmo 104:5; Luka 23:43.

Dziwani Zimene Zingakupezetseni Moyo Wosatha

Dziko likadzakhala paradaiso anthu onse adzakhala pamtendere ndi Mulungu. Lemba la Yesaya 11:9 limati: “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” Kumvetsa mfundo imeneyi kwathandiza Akhristu oona kuti ngakhale panopo azikhala mwamtendere ndiponso mogwirizana. Komanso iwo amagwiritsira ntchito mawu amene Yesu ananena nthawi ina popemphera. Iye anati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”—Yohane 17:3.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhuza malonjezo a Mulungu amene ali m’Baibulo, pezani Mboni za Yehova ndipo zidzakuthandizani kwaulere. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Mungathenso kupeza Mboni za Yehova pogwiritsa ntchito adiresi iyi pa Intaneti: www.dan124.com.