Njinga Yonolera Mipeni
Njinga Yonolera Mipeni
YOLEMBEDWA KU TANZANIA
▪ Kodi mutaona munthu atakwera njinga moyang’ana kumbuyo n’kumapalasa mwamphamvu koma njingayo osayenda mungaganize chiyani? M’madera ena padzikoli, monga kuno kum’mawa kwa Africa anthu amachita zimenezi ponola mipeni kuti azipeza kangachepe.
Onola mipeniwa amatenga njinga n’kuiwonjezera zina ndi zina. Pa keliyala ya njingayo amamangirirapo mwala wozungulira umene amanolera mipeni. Ndiyeno amamangirira chingwe ku chingelengele cha tayala lakumbuyo.
Sizikudziwika bwino kuti luso limeneli linayamba bwanji kuno ku Africa. Munthu wina amene wakhala akunola mipeni m’njira imeneyi kuyambira m’chaka cha 1985, dzina lake Andrea, ananena kuti: “Ndinamva kuti njinga zimenezi zinkapezeka ku Dar es Salaam, likulu la dziko lino la Tanzania, zisanafike kuno ku mzinda wa Moshi. Kunoko zinafika m’chaka cha 1982.”
Kodi munthu ungapeze bwanji njinga zimenezi? Andrea ananena kuti, “Timapititsa njinga yabwinobwino kwa mmisiri, kapena kuti fundi m’Chiswahili, kuti akaisinthe mmene tikufunira.” Zimatenga tsiku limodzi kapena awiri kuti aisinthe.
Ntchito Yokhetsa Thukuta
Andrea amanyamuka pakhomo m’mamawa cha m’ma seveni koloko n’kukwera njinga yake kupita m’madera amene kumakhala anthu ambiri. Akafika, amayamba kuitanira amvekere: “Kunola mipeni! Kunola mipeni!” Amanena zimenezi kwinaku akuimba belu. Posakhalitsa amangomva mayi wina akumuitana kuti: “Onola mipeni! Tabwerani!” Ndipo amam’patsa mipeni ingapo yobuntha kuti awanolere. Kenako amangoonanso amayi ena abweretsa chikwanje, nawonso ometa amam’bweretsera zometera zawo. Andrea amanolanso makasu, zokumbira ndiponso chilichonse chofunika kunoledwa.
Andrea akafuna kugwira ntchito yake amaimika njinga yake pa malo a fulati n’kugwetsa sitandi kuti teyala lakumbuyo la njingayo likhale m’malere. Kenako pa teyalalo amakolekerapo chingwe choti chizizungulitsa mwala wonolerawo, akatero amayamba kupalasa atakhala pa chishalo chimene amachiika kutsogolo kwa njingayo. Akamanola mipeniyi moto umathetheka ndipo iye amangotuluka thukuta kamukamu. Potsirizira pake mipeniyo imathwa ngati malezala. Dzuwa likalowa iye amabwerera kunyumba kwake.
Njinga yonolera mipeniyi ndi njira imodzi imene anthu osauka “akhama” amasonyezera luso lawo kuti apeze kangachepe popanda kubera ena.—Miyambo 13:4.