Makolo Ogwirizana
Makolo Ogwirizana
▪ Madera okwera a kumpoto kwa dziko la South Africa ndi ozizira kwambiri. Nthawi zambiri ndikakhala mu ofesi yanga n’kumayang’ana panja, ndimaona mtengo wina wopanda masamba ukugwedera ndi mphepo. Tsiku lina nditayang’ana paphanda la mtengowo, ndinaona njiwa ikusamalira tiana take tiwiri tating’ono.
Mbalame yaikaziyi isanayikire mazira inamanga chisa mothandizana ndi mbalame yaimuna. Yaimuna inkabweretsa timitengo ndipo yaikazi inkamanga chisacho. Chisachi chinali cholimba kwambiri moti ngakhale mphepo yamphamvu imene imaomba nthawi yozizira siingachipasule. Zitamaliza kumanga chisachi, yaikazi inayikira mazira awiri ndipo imagonera mazirawa usiku pamene yaimuna imagonera mazirawa masana. Patatha milungu iwiri inaswa ana. Pasanathe milungu ina iwiri anawa anakula n’kuyamba kuuluka okha.
Yaikaziyi ikamabwera m’mawa, imabwera ikuimba komanso itanyamula zakudya. Ikamaimba imakhala ikudziwitsa ana ake kuti yabweretsa zakudya komanso kudziwitsa yaimuna kuti yafika kudzailandira. Mbalamezi zimasamalirabe anawa ngakhale atayamba kuuluka mpaka pamene adzafike podzipezera okha chakudya.
Ndimachita chidwi ndi kugwirizana kwa mbalamezi ndiponso mmene zimasamalirira ana awo. Mbalamezi zimasamalira bwino ana awo chifukwa chakuti mwachibadwa Mulungu anazipatsa nzeru. Zimenezi zimandikumbutsa mawu a pa Salmo 86:8 akuti: “Palibe wina wonga Inu, Ambuye; ndipo palibe ntchito zonga zanu.”
M’Baibulo, Yehova Mulungu anapereka malangizo odalirika othandiza makolo kulera bwino ana awo ngati mmene zimachitira mbalamezi mwachibadwa. Mwachitsanzo, Baibulo limalimbikitsa amayi “kukonda ana awo.” (Tito 2:4) Ndipo limalimbikitsa abambo kuti: “Musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.” (Aefeso 6:4; 1 Timoteyo 5:8) Kunena zoona, Mulungu amakonda kwambiri makolo amene amachita zimenezi.