Kutonthoza Amene Akulira
Kutonthoza Amene Akulira
▪ Kabuku ka masamba 32 ka zithunzi zokongola kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira kamatonthoza onse amene akulira. Kangathandize anamalira onse kuti athetse nkhawa zimene amakhala nazo munthu amene amamukonda akamwalira. Ndipo mutu wina wa m’kabuku kameneka ukufotokoza zimene anthu ena angachite kuti athandize anthu amene akulira.
Kabukuka kamayankha mafunso ngati akuti: Kodi ndingakhale motani ndi chisoni changa? Kodi pali chiyembekezo chotani kaamba ka anthu akufa? Kakufotokozanso zimene Baibulo limanena zokhudza imfa ndi chimene chimachitika munthu akafa. Ndipo koposa zonse, kakufotokoza za kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu, kudzera mwa Yesu Khristu, lakuti akufa adzauka pa dziko lapansi loyeretsedwa la paradaiso.
Mwinamwake inuyo kapena munthu wina amene mukumudziwa angatonthozedwe atawerenga kabukuka. Tikukupemphani kuti muitanitse kabuku kameneka.
Ngati mukufuna kuitanitsa kabukuka, lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.