Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
Zinachitikira Kuti?
1. Kodi zomwe zasonyezedwa pachithunzipa zinachitikira mumzinda uti?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Machitidwe 18:1-3.
Lembani mzere wozungulira yankho lanu pamapu awa.
Roma
Korinto
Efeso
Tariso
▪ Kodi anthu atatuwa akutani?
․․․․․
▪ Kodi mwamuna ndi mkazi wakeyo maina awo ndani? Nanga mnzawoyo dzina lake ndani?
․․․․․
KAMBIRANANI:
Tchulani dzina la munthu winanso amene anathandizidwa ndi banjali?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Machitidwe 18:24-26.
Kodi mukuganiza kuti banjali linkakonda ntchito yotani, ndipo n’chifukwa chiyani mukuganiza choncho?
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
Kuchokera M’magazini Ino
Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.
TSAMBA 3 Kodi munthu amene sasamalira banja lake amakhala woipa kuposa ndani? 1 Timoteyo 5:․․․
TSAMBA 5 Kodi n’chifukwa chiyani awiri amaposa mmodzi? Mlaliki 4:․․․
TSAMBA 11 Kodi ndani amakhala ndi nzeru? Yobu 12:․․․
TSAMBA 29 Kodi tiyenera kupewa chiyani? 1 Atesalonika 4:․․․
Kodi Mukudziwa Chiyani Zokhudza Woweruza Gideoni?
Werengani Oweruza 6:1–7:25. Ndiyeno yankhani mafunso otsatirawa.
2. ․․․․․
Kodi anali wa fuko liti?
3. ․․․․․
Kodi anapulumutsa Aisiraeli ku mtundu uti?
4. ․․․․․
Zoona kapena zonama? Anakhala ndi moyo Mose asanabadwe.
KAMBIRANANI:
Kodi Gideoni anasonyeza khalidwe lotani atasankhidwa ndi Yehova?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Oweruza 6:14-16.
Kodi mukuganiza kuti khalidwe limeneli ndi lofunika? Fotokozani chifukwa chake mukuyankha choncho.
▪ Mayankho ali patsamba 27
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
1. Korinto.
▪ Akupanga hema.
▪ Akula ndi Purisikila, ndiponso Paulo.
2. Manase.—Oweruza 6:15.
3. Midiyani.—Oweruza 6:6.
4. Zonama.