Mfundo 5: Muzilolerana
Mfundo 5: Muzilolerana
“Kulolera kwanu kudziwike.”—Afilipi 4:5.
Mungachite bwanji? Kuti banja liziyenda bwino, mwamuna ndi mkazi wake amafunika kulolerana wina akalakwa. (Aroma 3:23) Pamafunikanso kuti asakhale oumitsa zinthu kwambiri kapenanso olekerera ana awo. Komanso ayenera kuika malamulo angapo oti ana azitsatira panyumba. Ndipo ana ayenera kupatsidwa chilango “pa mlingo woyenera.”—Yeremiya 30:11, NW.
Kufunika kwake. Baibulo limanena kuti ‘nzeru yochokera kumwamba ndi yololera.’ (Yakobe 3:17) Mulungu sayembekezera kuti tizichita zinthu zonse popanda kulakwitsa. Choncho, si bwino kuti mwamuna kapena mkazi aziyembekezera mnzake kuchita chilichonse mosalakwitsa. Ndipotu kumangoona zolakwa za mnzanu kumachititsa kuti muzisungirana chakukhosi. Ndi bwino kuvomereza mfundo yakuti “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.”—Yakobe 3:2.
Makolo abwino amachita zinthu mololera ndi ana awo. Sawalanga mopitirira malire ndipo sakhala “ovuta kuwakondweretsa.” (1 Petulo 2:18) Amapatsa ana awo ufulu wochita zinthu zina paokha ngati anawo akuyesetsa kuchita zinthu bwino, m’malo mongowauza zochita pa chilichonse. Buku lina limati kumangouza mwana wanu zochita pa chilichonse kuli ngati “kulimbikira kuvina n’cholinga choti mvula ibwere. Mvula singabwere ndipo kuchita zimenezi n’kotopetsa.”
Yesani izi. Yankhani mafunso otsatirawa, kuti mudziwe ngati ndinu wololera.
▪ Kodi ndi liti pamene munayamikira mwamuna kapena mkazi wanu?
▪ Kodi ndi liti pamene munakalipira mkazi kapena mwamuna wanu?
Chitani izi. Ngati mwavutika kuyankha funso loyambalo koma simunavutike kuyankha lachiwiri, ganizirani zimene mungachite kuti mukhale munthu wololera.
Mungachite bwino kukambirana ndi mkazi kapena mwamuna wanu zimene mungachite kuti mukhale wololera.
Ganizirani ufulu umene mungapatse mwana wanu akasonyeza kuti ndi wodalirika.
Mungachite bwino kukambirana ndi mwana wanu nthawi imene ayenera kumafika panyumba.
[Chithunzi patsamba 7]
Muyenera kukhala wololera ngati mmene amachitira dalaivala wosamala