Ndinasiya Usilikali N’kuyamba Kutumikira Yehova
Ndinasiya Usilikali N’kuyamba Kutumikira Yehova
Yosimbidwa ndi Andrew Hogg
“Ngati tingaphulitse mabomba anyukiliya, ndiye kuti talephera ntchito yathu,” anatero mkulu wa asilikali yemwe ankayang’anira sitima yathu yapamadzi. Zimenezi zinachititsa kuti tiyambe kukambirana ngati kugwiritsa ntchito zida zanyukiliya kunali koyenera. Komano, kodi ndinayamba bwanji usilikali wapamadzi?
NDINABADWA mu 1944, mumzinda wa Philadelphia, ku Pennsylvania, U.S.A. Ndili mwana, bambo, agogo komanso amalume anga ankandilimbikitsa kuti ndidzakhale msilikali, chifukwa chakuti iwonso poyamba anali asilikali ndipo ankaona kuti ntchito imeneyi ndi yabwino kwambiri. Nthawi ina ndili mnyamata, ndinapita kukaona malo osungirako sitima zankhondo ndipo aka kanali koyamba kuona sitima yapamadzi ya asilikali. Kungoyambira nthawi imeneyi, ndinali ndi cholinga choti ndidzakhale msilikali wapamadzi. Ndipo nditatsala pang’ono kumaliza maphunziro anga akusekondale, ndinasankhidwa kupita kusukulu ya asilikali apamadzi ya U.S. Naval Academy. Ndinachita maphunziro a usilikali zaka zinayi ndipo ndinamaliza mu June 1966.
Kenako ndinayamba maphunziro okonza zida zanyukiliya komanso sitima zapamadzi. Ndipo mu April 1967, ndinakwatira Mary Lee Carter, yemwe ndili nayebe mpaka pano. Cholinga changa chokhala msilikali wapamadzi chinakwaniritsidwa mu March 1968, pamene ndinayamba kugwira ntchito mu sitima yotchedwa USS Jack. Chaka chotsatira, mkazi wanga anakhala ndi mwana wamkazi, amene tinam’patsa dzina lakuti Allison.
Mu 1971, ndinayamba kugwira ntchito mu sitima ya USS Andrew Jackson, yomwe inkanyamula zida zanyukiliya. Ndipo ndinali mkulu wa akatswiri okonza sitimayo. Woyendetsa sitimayi ndi amene ananena mawu amene ali kumayambiriro kwa nkhaniyi. Tsiku lina musitimayi munabuka moto. Ngozi ya moto ndi imene imadetsa nkhawa kwambiri asilikali apamadzi. Pakati pa usiku tikupuma, tinamva phokoso ndipo kenako kunalira belu. Posakhalitsa tinamva chenjezo lakuti, “Moto m’chipinda choyamba cha injini!”
Popeza kuti ineyo ndi amene ndinkayang’anira ntchito yokonza sitimayo, ndinathamangirako kuti ndikaone chimene chachitika. Ndinapeza kuti makina ena amene amapanga mpweya woti anthu azipuma m’sitimamo akuyaka. Nthawi yomweyo, ineyo ndi anzanga ena atatu tinavala zodzitetezera ndipo tinayamba kutaya zinthu zonse zomwe zikanatha kuyaka. Mwamwayi, palibe amene anavulala. Ngakhale kuti tinakumana ndi ngoziyi, tinapitirizabe ulendo wathu, ndipo zimenezi zinali umboni wakuti tinaphunzitsidwa bwino.
Ndinayamba Kuwerenga za Yesu
Kuti ntchito yathu tisamaimve kuwawa, mlungu uliwonse tinkalimbikitsidwa kuwerenga zinthu zosiyanasiyana zokhudza chikhalidwe cha anthu. Nthawi zambiri ndinkakonda kuwerenga za asilikali otchuka. Koma panthawiyi ndinayamba kuwerenga za Yesu Khristu, yemwe amadziwika kuti anali munthu wokonda mtendere. Ndinayamba kuwerenga mabuku a Uthenga Wabwino, pogwiritsa ntchito Baibulo limene ndinalandira panthawi imene ndinkamaliza maphunziro anga a usilikali. Zimene ndinkawerenga zinkandichititsa kuti ndizikhala ndi mafunso ambiri. Ndinkafunitsitsa munthu wina atandithandiza.
Titatsala pang’ono kumaliza ulendowu, mkulu wa asilikali yemwe ankatiyang’anira anatisonkhanitsa n’kutiuza kuti: “Akuluakulu, mnzathuyu wasankhidwa kukagwira ntchito yabwino kwambiri pa ntchito zonse za asilikali apamadzi ku United States kuno. Iye wakwezedwa kukhala mkulu wa akatswiri okonza sitima yoyamba pa sitima zathu zamakono.” Ndinangoona ngati kutulo.
Choncho, ine ndi banja langa tinasamukira ku Newport News, mumzinda wa Virginia, komwe ndinkagwira nawo ntchito yokonza sitima yatsopano yotchedwa USS Los Angeles. Ndinkayang’anira ntchito yoyesa zipangizo za mu sitimayi. Ndinkalembanso mabuku a mmene zipangizozi zimagwirira ntchito komanso mabuku ophunzitsira anthu. Ntchitoyi inali yovuta kwambiri koma inkandisangalatsa. Panthawiyi, mkazi wanga anabereka mwana wina, dzina lake Drew. Tsopano ndinali bambo wa ana awiri, ndipo ndinayambanso kudzifunsa mafunso okhudza Mulungu, monga akuti: ‘Kodi Mulungu amaiona bwanji nkhondo? Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? Kodi anthu oipa adzapsa ndi moto?
Ndinapeza Mayankho a Mafunso Anga
Panthawi imeneyi, mkazi wanga ankakambirana za m’Baibulo ndi anthu awiri a Mboni za Yehova. Tsiku lina nditaimba foni kunyumba, mkazi wanga anandiuza kuti, “Kwabwera azimayi awiri ophunzitsa Baibulo.”
Ndinamufunsa kuti, “Ndi a mpingo wanji?”
Anandiyankha kuti, “Mboni za Yehova.”
Sindinkadziwa zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira, komabe popeza ndinkafuna kudziwa Baibulo ndinamuuza mkazi wangayo kuti, “Uwapemphe kuti adzabwerenso tsiku lina madzulo.” Pasanapite masiku ambiri, mmodzi wa azimayiwo anabwera ndi mwamuna wake, choncho ineyo ndi mkazi wanga tinayamba kuphunzira Baibulo.
Pang’ono ndi pang’ono anayamba kuyankha mafunso amene ndinakhala nawo kwa zaka zambiri. Mwachitsanzo, ndinaphunzira kuti akufa “sadziwa kanthu bi” ndipo, monga mmene Yesu anasonyezera, amakhala ngati akugona. (Mlaliki 9:5; Yohane 11:11-14) Choncho, akufa sakhala kumalo enaake kumene amasangalala kapena kuzunzidwa, koma amakhala ngati akugona ndipo amangodikirira kuukitsidwa.
Kenako Ine ndi mkazi wanga tinayamba kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu. Kumeneko tinapezana ndi anthu a zikhalidwe, maphunziro, ndiponso mitundu yosiyanasiyana. Anthu onsewa ankatumikira Mulungu mogwirizana ndiponso mwamtendere. Ine ndi mkazi wanga tinafika pozindikira kuti Baibulo limathandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino.—Salmo 19:7-10.
Nthawi Yosankha Zochita
Nkhondo ya pakati pa Israel ndi mayiko achiluya itaulika mu 1973, sitima za nkhondo za pamadzi zinatumizidwa kumeneko. Zinthu zinkaoneka Mateyo 6:9, 10) Panopa ndimazindikira kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba limene posachedwapa lidzalamulire dziko lonse lapansi, n’kuchotseratu zinthu zonse zoipa ndi onse amene amazichita.—Danieli 2:44; 7:13, 14.
kuti zifika poipa kwambiri, ndipo panthawiyi ndinazindikira kuti Ufumu wa Mulungu wokha, osati maboma a anthu, ndi umene ungabweretse mtendere weniweni. Ndipotu nthawi imeneyo ndinkapemphera kuti “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano,” koma sindinkadziwa tanthauzo lake. (Lemba lina limene linandikhudza kwambiri ndi 2 Akorinto 10:3, 4. Lembali limanena kuti Akhristu oona ‘samenya nkhondo monga mwa thupi. Pakuti zida za nkhondo yawo sizili za kuthupi, koma zili zamphamvu mwa Mulungu.’ Ndinaphunzira kuti “zida” zimenezi ndi zauzimu, ndipo zikuphatikizapo “lupanga la mzimu,” lomwe ndi Baibulo.—Aefeso 6:17.
Panthawiyi ndinafunika kusankha chimodzi: Kupitirizabe ntchito ya usilikali yomwe ndinkaikonda kwambiri, kapena kuyamba kutsatira choonadi cha m’Baibulo pamoyo wanga. Nditapemphera kwa Mulungu za nkhaniyi kuti andithandize, ndinaona kuti ndiyenera kusankha kutumikira Mulungu ngati ndikufunadi kukhala munthu wamtendere.
Mtsogoleri wa Asilikali Watsopano
Ine ndi mkazi wanga tinakambirana nkhaniyi ndipo tinasankha kutumikira mtsogoleri wa asilikali watsopano. Tonse tinaganiza zodzipereka kwa Yehova, ndipo ndinalemba kalata yosiya ntchito. Kenako anandisamutsira ku Norfolk, ku Virginia, kukadikirira kuti andiyankhe. Anzanga ambiri amene ndinkagwira nawo ntchito anadabwa kwambiri kuti ndikufuna kusiya ntchito ndipo ena ankandinyoza. Komabe ena ankaona kuti ndachita bwino kusankha kutsatira zimene Baibulo limanena ndipo ankandilemekeza kwambiri.
Ndinalandira kalata yondilola kusiya ntchito mu 1974. Chaka chomwechi ine ndi mkazi wanga tinabatizidwa posonyeza kuti tadzipereka kwa Mulungu pa Msonkhano Wachigawo wa mutu wakuti “Cholinga cha Mulungu,” womwe unachitikira mumzinda wa Hampton, ku Virginia. (Mateyo 28:19, 20) Chimenechi chinali chiyambi cha moyo wathu watsopano.
Tinakumana ndi Mavuto Ena
Ine ndi mkazi wanga tinali ndi ana awiri ang’ono koma sindinali pantchito ndipo ndalama zomwe tinali nazo zinali zongokwanira kugwiritsa ntchito miyezi yochepa. Ndinatumiza makalata ofunsira ntchito ku makampani ambiri ndipo tinkakhulupirira kuti Mulungu atithandiza. Pasanapite nthawi yaitali, ndinayamba ntchito pakampani ina. Ndinkalandira theka la malipiro amene ndinkalandira ku usilikali, komabe ndalama zimene ndinkapeza zinali zokwanira kutithandiza kukhalabe m’deralo.
Ine ndi mkazi wanga titapita patsogolo mwauzimu, tinaganiza zotumikira Yehova mowonjezereka. Banja linalake la Mboni lomwe tinkadziwana nalo, linasamukira kudera lapakati ku Virginia, komwe kunali anthu ochepa ophunzitsa Baibulo. Banjali linatiitana kuti tikacheze nalo. Ulendo woyamba womwewo unatichititsa kuti tiganize zosamuka kupita kudera limeneli. Ndinalemba kalata ku kampani yathu yopempha kuti ndisamuke n’kumakagwirira ntchito kudera latsopanolo, ndipo ndinasangalala kwambiri atandilola. Anandiuzanso kuti ndakwezedwa ntchito. Kampaniyo inalonjezanso kuti itipatsa ndalama zoti tigwiritse ntchito posamuka. Tinaona kuti Mulungu amasamaliradi anthu amene amayesetsa kuchita chifuniro chake.—Mateyo 6:33.
Popeza kuti pabanja pathu timayesetsa kukhala ndi moyo wosafuna zambiri, ine ndi mkazi wanga takwanitsa kuchita utumiki wa nthawi zonse. Zimenezi zatithandiza kuti tizikhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi ana athu awiri omwe timawakonda kwambiri. Panopa ndife osangalala kwambiri chifukwa ana athu, Allison ndi Drew, “akuyendabe m’choonadi.”—3 Yohane 4; Miyambo 23:24.
N’zoona kuti nthawi zina timakhala ndi nkhawa chifukwa cha mavuto a zachuma, malo okhala, thanzi lathu komanso ukalamba. Komabe Yehova wakhala akutithandiza nthawi yonseyi. Panopa sindidandaula ngakhale pang’ono kuti ndinasiya ntchito ya usilikali. Ineyo ndi mkazi wanga tikaganizira za moyo wathu, timaona kuti palibe ntchito inanso yabwino ndiponso yopindulitsa kuposa kutumikira Yehova.—Mlaliki 12:13.
[Mawu Otsindika patsamba 14]
Tinasankha kutumikira mtsogoleri wa asilikali watsopano
[Chithunzi pamasamba 12, 13]
Sitima ya USS “Los Angeles”
[Mawu a Chithunzi]
U.S. Navy photo
[Chithunzi patsamba 13]
Ndili ndi mkazi wanga, Mary Lee, posachedwapa