Kuchokera kwa Owerenga
Kuchokera kwa Owerenga
Zimene Anthu Akuchita Pofuna Kuthetsa Vuto la Kusowa kwa Madzi (January 2009) Sindinasangalale ndi zimene munanena kumapeto kwa nkhaniyi. M’malo molimbikitsa owerenga anu kuti azithandiza anthu ena kukumba zitsime, kulimbikitsa njira zosamalirira madzi, kapena kufufuza njira zothetsera vutoli, nkhaniyi inanena kuti: “Mulungu yekha ndi amene ali ndi njira yabwino kwambiri yothetsera vuto la kusowa kwa madzi” ndiponso kuti Mulungu ‘adzapanga zinthu zonse kukhala zatsopano.’ (Chivumbulutso 21:5)” Nkhani imeneyi ndi yosangalatsa koma kodi sizingakhale bwino kuyesetsa kuthetsa vutoli panopa? Masiku ano padzikoli pali mavuto ambiri. Ngakhale kuti Mulungu adzathetsa mavutowa m’tsogolo, ndikuona kuti si bwino kungokhala n’kumusiya Mdyerekezi akuwononga dzikoli.
S. S., United States
Yankho la “Galamukani!”: Cholinga cha nkhaniyi sichinali kufotokoza kuti anthu alibe udindo woyesetsa kuchepetsa mavuto a kusowa kwa madzi. Nkhaniyi inafotokoza kuti, “Mulungu anapatsa anthu udindo wosamalira dziko lapansili.” Ndipo takhala tikulemba nkhani zambiri zimene zimalimbikitsa owerenga kusamalira ndiponso kuteteza zinthu zachilengedwe. Koma vuto ndi lakuti anthu akulephera kusamalira zachilengedwe chifukwa chakuti amaika malamulo amene amalimbikitsa ntchito zachuma osati zosamalira chilengedwe. Komanso anthu ambiri amakonda kwambiri chuma ndiponso ndi odzikonda. N’chifukwa chake tinanena kuti “Mulungu yekha ndi amene ali ndi njira yabwino kwambiri yothetsera vuto la kusowa kwa madzi.”
Dzikoli Linapangidwa Kuti Likhale ndi Zamoyo (February 2009) Panopa anthu ambiri amalemba nkhani zochititsa mantha zokhazokha zokhudza kutentha kwa dziko. Koma nditawerenga nkhani zanu mtima wanga unakhala pansi. Ndinasangalalanso kudziwa kuti m’tsogolomu tikuyembekezera zinthu zabwino chifukwa dziko lapansi lidzakhala paradaiso, ndipo anthu adzakhala mwamtendere. Zikomo kwambiri.
M. H., Japan
Sindinabwerere M’mbuyo Ngakhale Kuti Ndili ndi Matenda Olepheretsa Kuwerenga (February 2009) Inenso ndili ndi matenda olepheretsa kuwerenga ndipo poyamba sindinkadziwa kuti vutoli ndi lalikulu bwanji. Ndinazindikira kukula kwa vutoli pamene ineyo ndi mkazi wanga tinatumizidwa kukachita umishonale kudziko lina ndipo ndinkalephera kuphunzira chinenero china. Nkhaniyi yandilimbikitsa kwambiri, makamaka bokosi limene lili patsamba 22, lomwe landithandiza kuti ndilimvetse bwinobwino vutoli. Ndinasangalala kwambiri ndi nkhani ya Michael Henborg, yemwe anali ndi matendawa koma anakwanitsa kuphunzira zinenero zambiri. Zikomo kwambiri.
M. M., Tanzania
Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndingatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzindisangalatsa? (April 2009) Ndili ndi vuto losatha kuona bwinobwino ndipo ndimagwira ntchito pasukulu ya anthu akhungu. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa mabuku anu andithandiza kwambiri. Nthawi zambiri ndisanakagone, ndimamvetsera nkhani zanu pa kaseti kapena pa CD. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizigona tulo tabwino. Ndamvetsera nkhaniyi pafupifupi kasanu ndipo yandithandiza kupeza njira zabwino zowerengera.
S. H., France