Mfundo 20 Zothandiza Kuti Muzikhala ndi Nthawi Yokwanira
Dulani N’Kusunga
Mfundo 20 Zothandiza Kuti Muzikhala ndi Nthawi Yokwanira
“Pitirizani kuyenda mwanzeru kwa akunja, ndipo muzidziwombolera nthawi yopezeka.”—Akolose 4:5.
PAMBUYO poti mwadziwa zinthu zimene mukufuna kumawonongerapo nthawi yanu, chatsala n’kuyesetsa kuzichita. Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kukwaniritsa zimenezo.
1 MUZILEMBA ZIMENE MUKUFUNA KUCHITA. Muzilemba mwandondomeko zimene mukufuna kuchita tsiku lililonse, ndipo ntchito imene mukufuna kuchita koyambirira muziilemba koyamba. Sonyezaninso ntchito zimene mufunika kutherapo nthawi yambiri. Mukamaliza ntchitoyo, muziichonga. Ngati ntchito ina yatsala, muziipititsa pa zochita za tsiku lotsatira.
2 MAKALENDALA ANU ONSE AZISONYEZA ZOFANANA. Si bwino kuphonya zimene munapangana ndi munthu wina chifukwa chakuti munalemba zomwe munapanganazo pa kalendala ina yosiyana ndi imene mukugwiritsa ntchito. Ngati muli ndi kalendala pakompyuta yanu ndipo ina pa chipangizo china, onetsetsani kuti makalendala onsewa akusonyeza zofanana.
3 LEMBANI NDONDOMEKO YA MMENE MUGWIRIRE NTCHITO. Muzilemba mwandondomeko zinthu zonse zomwe muchite pogwira ntchito inayake.
4 NTCHITO YOFUNIKA KWAMBIRI IZIKHALA KOYAMBIRIRA. Mukamaliza ntchito yofunika kwambiri, zimakhala zosavuta kupeza nthawi yogwira ntchito zina zosafunika kwenikweni.
5 MUZIKHALA NDI ZOLINGA ZOMWE MUNGATHEDI KUZIKWANIRITSA MOSAVUTA. Mwachitsanzo, cholinga chofuna kuwonjezera luso lanu pa ntchito inayake n’chosavuta kuchikwaniritsa kusiyana ndi cholinga chofuna kukhala bwana wa kampani yanuyo.
6 DZIWANI KUTI N’ZOSATHEKA KUCHITA ZONSE ZOMWE MUNAKONZA. Muzichita zinthu zimene mungapindule nazo kwambiri. Nanga bwanji ntchito yofunika kuichita mwamsanga kapena imene mukuyembekezeredwa kuichita basi? Ngati simungangoisiya kapena kupempha wina kuti aichite, muziigwira msanga. Ntchito zina zosafunika kwenikweni mungazisiye n’kudzazigwira patapita mwezi umodzi kapena kuzisiyiratu. Muzikhala ndi nthawi yokwanira yochita zinthu zimene mukuona kuti n’zofunika kwambiri, mogwirizana ndi zolinga zanu.
7 MUZILEMBA MMENE MUKUGWIRITSIRA NTCHITO NTHAWI YANU. Kuti muzidziwa kumene nthawi yanu imathera, muzilemba nthawi imene mwathera pochita zinazake kwa mlungu umodzi kapena iwiri. Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa ngati mumawonongera nthawi yanu pa zinthu zosafunika kwenikweni. Mungathenso kudziwa ngati munthu winawake amakonda kukusokonezani. Mungadziwenso nthawi imene mumasokonezedwa kwambiri tsiku lililonse kapena mlungu uliwonse. Mukatero, yambani kupewa zinthu zimene zimakuwonongerani nthawiyo.
8 MUSAMAFUNE KUCHITA ZINTHU ZAMBIRI PATSIKU. Ngati patsiku mukufuna kukagula zakudya kumsika, kukonza galimoto, kucheza ndi alendo, kukaonera filimu ndiponso kuwerenga, mungapanikizike kwambiri ndipo simungakhale wosangalala.
9 CHEPETSANI ZODODOMETSA. Muzikhala ndi nthawi patsiku yochita zinthu zina popanda kudodometsedwa. Muzilola kudodometsedwa pakakhala zifukwa zomveka. Ngati n’kotheka, muzithimitsa foni yanu kapena zipangizo zina panthawi imeneyi.
10 MUZIGWIRA NTCHITO YOVUTA KWAMBIRI PANTHAWI YOMWE MULI NDI MPHAMVU.
11 NTCHITO YOMWE SIKUKUSANGALATSANI MUZIIGWIRA MWACHANGU. Mukangothana ndi ntchito yotereyi, mumapezanso mphamvu yogwira ntchito zina zosangalatsa.
12 MUZIYEMBEKEZERA KUTI PAKHALA ZINTHU ZINA ZODODOMETSA. Ngati mukuona kuti zikutengerani mphindi 15 kuti mukafike pamalo amene munapangana ndi munthu wina, mungamulonjeze kuti mukafika pamalowo pakatha mphindi 25. Ngati mukuona kuti zimene mukufuna kukachita ndi munthu wina zikakutengerani ola limodzi, muzikonzekera kuti zikhoza kukatenga ola limodzi ndi mphindi 20. Mukamakonza zoti muchite patsiku, muzisiya nthawi ina yapadera.
13 MUKAMADIKIRIRA ZINAZAKE, MUZIGWIRITSA NTCHITO NTHAWI MWANZERU. Mwachitsanzo, pamene mukumetedwa, mungamamvetsere nkhani kapena pulogalamu inayake pa wailesi. Pamene mukuyembekezera sitima kapena pamene muli m’sitimayo, mungamawerenge kapena kupuma. Koma si bwino kungoiwononga n’kumadandaula pambuyo pake.
14 CHITANI ZOFUNIKA ZOKHAZOKHA KUTI MUSUNGE NTHAWI. * Kodi pa zinthu 10 zimene mukufuna kuchita, ziwiri ndi zofunika kwambiri kuposa zinazo? Kodi n’zotheka kumaliza kaye chinthu china chofunika kwambiri pa ntchitoyo n’cholinga chakuti ngati simukhala ndi nthawi yokwanira, pasakhale vuto kwenikweni.
15 NGATI MWATOPA NDI NTCHITO INAYAKE, lembani ntchitoyo papepala. Kenako gawani zimene muyenera kuchita. Mwachitsanzo, mungalembe kuti, “Zoti Ndichite Lero” ndi “Zoti Ndichite Mawa.” Tsiku lotsatiralonso mungachite chimodzimodzi.
16 MUZIKHALA NDI NTHAWI YOPUMA KUTI MUKHALENSO NDI MPHAMVU. Kubwereranso kuntchito pambuyo poti mwapuma kungakuthandizeni kuti muchite zambiri kusiyana ndi kugwira maola ambirimbiri osapuma.
17 LEMBANI MAVUTO NDIPONSO MMENE MUNGAWATHETSERE. Muzilemba papepala vuto limene mukukumana nalo pa ntchito yanu ndiponso njira zosiyanasiyana zothetsera vutolo.
18 MUSAMAYEMBEKEZERE KUTI MUNGAKWANITSE NTCHITO ILIYONSE. Ngati ntchito inayake yakuvutani, mungaisiye n’kuyamba kuchita chinthu china chofunikanso.
19 MUZIGWIRA NTCHITO MONGA MUNTHU WOIDZIWA. Muziyesetsa kugwira ntchito mwakhama ngakhale ngati tsiku limenelo simunadzuke mwantchito.
20 MUKHOZA KUSINTHA. Mfundo zimene takambiranazi ndi malangizo chabe. Yesani kuona zimene zingakuthandizeni ndipo mungazisinthe kuti zigwirizane ndi mmene zinthu zilili pamoyo wanu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 18 Mfundo imeneyi anayambitsa ndi katswiri wina wazachuma wa ku Italy, dzina lake Vilfredo Pareto. Iye ananena kuti nthawi zambiri tingagwire chintchito chachikulu m’kanthawi kochepa. Mfundo imeneyi imagwira ntchito pa zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mukamayeretsa m’nyumba, fumbi lambiri limachokera malo amene anthu amakonda kudutsa ndipo malo amenewa amakhala aang’ono kwambiri. Choncho, kungosesa malo amenewo mumakhala kuti mwagwira ntchito yaikulu kuposa kuwononga nthawi kusesa malo akulu omwe sanade kwenikweni.