N’zotheka Kusiya Fodya
N’zotheka Kusiya Fodya
TINENE kuti tsopano ‘mwalimba mtima’ kuti musiye kusuta fodya, kodi ndi mfundo ziti zomwe mungatsatire kuti zimenezo zitheke?—1 Mbiri 28:10.
Sankhani tsiku. Dipatimenti ya zaumoyo ku United States inanena kuti munthu akaganiza zosiya kusuta, ayenera kuonetsetsa kuti waziikira malire osiya kusuta mkati mwa milungu iwiri. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti musasinthe maganizo. Lembani tsiku lomwe mwasankhalo pakalendala, dziwitsani anzanu ndipo tsikulo likafika musalisinthe, zivute zitani.
Muziyenda ndi pepala lolembedwa kuti “Ndasiya kusuta.” Papepalapo mungalembe zinthu zomwe zingakuthandizeni kutsatira zomwe mwasankha monga:
● Zifukwa zosiyira.
● Manambala a foni a anthu amene mungawaimbire panthawi yomwe chibaba cha fodya chakubwererani.
● Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni, ngati zomwe zili pa Agalatiya 5:22, 23.
Nthawi zonse muziyenda ndi pepala limene mwalemba kuti “Ndasiya kusuta” kuti lizikukumbutsani zomwe mwasankhazo. Ngakhale mutafika poti mwasiya kusuta, muziyenda nalobe kuti muziliwerenga mukaona kuti chibaba choti musute chayambiranso.
Siyani zinthu zina zimene mumakonda kuchita. Tsiku lomwe mwasankha kusiya kusuta lisanafike, muyenera kusiya kaye zizolowezi zina zimene mumachita. Mwachitsanzo, ngati muli ndi chizolowezi chosuta mukangodzuka m’mawa, yesani kusintha kuti muzitha ola limodzi musanasute. Ngati mumasuta panthawi ya chakudya kapena mukangomaliza kudya, siyani kusuta panthawi imeneyi. Pewani malo amene anthu amakonda kusutirako fodya. Ndipo mukakhala nokha muziyesa kunena mokuwa kuti: “Pepani, ndasiya kusuta.” Zimenezi zingakuthandizeni kwambiri kuti musadzavutike kusiya tsiku limene mwasankha kusiya kusuta likafika. Komanso zimenezi zingakuthandizeni kuona kuti kusuta fodya ikhala mbiri yakale kwa inu.
Konzekani. Tsiku limene mwasankha kuti musiye kusuta likayandikira, pezani zinthu zomwe mungamadye, m’malo mosuta. Mwachitsanzo, mungagule kaloti, chingamu, mtedza ndi zina zotero. Kumbutsani anzanu komanso anthu am’banja lanu za tsiku limene mukufuna kusiya komanso mmene angakuthandizireni. Tsikulo lisanafike, muyenera kutaya zotsalira zonse za fodya, machesi ndi zina zimene zingakukopeni kuti muyambirenso kusuta. Mwachitsanzo, muyenera kutaya ndudu zimene zili m’nyumba, m’galimoto, m’matumba a zovala kapena ku ofesi. Kunena zoona, n’zovuta kwambiri kupempha mnzanu kuti akupatseni fodya kapena kugula paketi ya fodya kusiyana ndi kungopita m’nyumba n’kutenga. Ndiponso, pitirizani kupempha Mulungu kuti akuthandizeni, ndipo muyenera kuyesetsa kwambiri kuchita zimenezi pamene mwasiya kusuta.—Luka 11:13.
Anthu ambiri akwanitsa kusiya kusuta, ndipo inunso mungakwanitse. Dziwani kuti fodya ndi woipa. Kusiya kusuta kungakuthandizeni kukhala ndi thanzi labwino ndiponso kukhala wosangalala kwambiri.
[Chithunzi patsamba 9]
Nthawi zonse muziyenda ndi pepala limene mwalemba kuti, “Ndasiya kusuta” kuti lizikukumbutsani zomwe mwasankhazo