‘Buku Lothandiza Kwambiri’
‘Buku Lothandiza Kwambiri’
Banja lina la ku New Hampshire, m’dziko la United States, linalemba kalata yomwe inati: “Tikufuna kukuthokozani kwambiri chifukwa cha nkhani zosiyanasiyana zimene mumalembera makolofe. Ifeyo tili ndi mwana wamkazi wa zaka zinayi, dzina lake Sophia. Tikamawerenga nkhani zimenezi, timamva ngati tili ndi mlangizi wathuwathu amene akutithandiza kuti tikwanitse kuphunzitsa mwana wathu. Nkhani zimenezi zimatithandiza kuti tibzale mbewu za choonadi m’maganizo ndi mumtima mwake, pa zaka zofunika kwambiri zimenezi za moyo wake.”
Kalatayo inapitiriza kuti: “Buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso ndi lothandiza kwambiri kwa mwana wathu, ngakhalenso kwa ifeyo. Zithunzi zimene zili m’mutu womalizira wa bukuli ndi zokongola kwambiri pa zithunzi zonse za Paradaiso zimene taonapo. Mwana wathu amakonda kwambiri kuona zithunzi zimenezi ndipo amaphunzira zambiri zokhudza zimene Mulungu walonjeza m’Baibulo.”
Mutu womaliza wa buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, wakuti “Ungathe Kukhala M’dziko Latsopano la Mulungu Lamtendere,” uli ndi zithunzi zokongola zokhudza malonjezo a Mulungu amene ali m’Mawu ake, m’Baibulo.
Mukhoza kuitanitsa buku la masamba 256 limeneli. Masamba a bukuli ndi aakulu mofanana ndi a magazini ino. Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.
□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.
[Chithunzi patsamba 32]
Chithunzichi chili patsamba 254 m’bukuli