Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzina la Mulungu Likulengezedwabe

Dzina la Mulungu Likulengezedwabe

Dzina la Mulungu Likulengezedwabe

● Munthu akamayenda pachilumba chokongola cha Orleans pafupi ndi mzinda wa Quebec City, m’dziko la Canada, salephera kuona kuti anthu oyamba kukhala pachilumbachi anali okonda kupemphera. M’mphepete mwa msewu umene unazungulira chilumba chonsechi mudakali matchalitchi ambiri ndipo dera lililonse lili ndi tchalitchi chake. Munthu akaona matchalitchiwa amatha kukhala ndi chithunzi cha mmene zinthu zinalili kalelo pachilumbachi.

M’tawuni ya Saint-Pierre muli tchalitchi chomwe ndi chakale kwambiri m’chigawo chonse cha Quebec. Tchalitchichi chinamangidwa m’chaka cha 1717. Panopa tchalitchichi anachisandutsa malo oonetserako luso la zopangapanga. Koma mkati mwake muli chinthu chochititsa chidwi kwambiri. Pamwamba pa guwa pali zilembo zinayi zachiheberi zimene zimapanga dzina la Mulungu lakuti Yehova, limene limapezekanso m’Baibulo.

Masiku ano, si kawirikawiri kumva dzina la Mulungu likutchulidwa m’tchalitchi cha Katolika. Ndipo n’zosowa kwambiri kuliona litalembedwa penapake m’tchalitchimo. Izi n’zosadabwitsa chifukwa chikalata cholembedwa kulikulu la tchalitchi cha Katolika ku Vatican mu 2008, chinanena kuti Papa walamula kuti dzina la Mulungu “lisamagwiritsidwe ntchito kapena kutchulidwa” poimba nyimbo, popemphera kapena pamwambo uliwonse wachikatolika. Koma Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Yehova Mulungu amafuna kuti anthu “alalikire dzina [lake] pa dziko lonse lapansi.”—Eksodo 9:16.

Mboni za Yehova zimaona kuti kuchita zimene Mulungu akufuna n’kofunika kwambiri. Choncho zimayesetsa kulengeza dzina la Mulungu mwakhama osati kungolilemba penapake m’nyumba. Choncho, chaka chilichonse Mboni za Yehova padziko lonse zimathera maola oposa 1.5 biliyoni zikuphunzitsa anthu za dzina la Mulungu ndi zolinga zake. Komanso, sizinachotse dzina la Mulungu m’Baibulo lawo. Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Oyera limene Mboni za Yehova zafalitsa, linatsatira kwambiri zilankhulo zoyambirira zimene analembera Baibulo, mmene dzina lakuti Yehova limapezeka nthawi pafupifupi 7,000. Pofika pano, Mabaibulo a Dziko Latsopano amene asindikizidwa, athunthu kapena mbali yake yokha, akwana 165 miliyoni, m’zinenero 83. Choncho pa nkhani ya dzina la Mulungu lakuti Yehova, funso limene tiyenera kudzifunsa ndi lakuti, ‘Kodi n’chifukwa chiyani sitikugwiritsa ntchito dzinali?’ Osati lakuti, ‘Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito dzinali?’

[Chithunzi patsamba 21]

Baibulo la Dziko Latsopano, limene dzina lakuti Yehova limapezekamo nthawi pafupifupi 7,000, lasindikizidwa lathunthu kapena mbali yake yokha m’zinenero 83