“Musade Nkhawa za Tsiku Lotsatira”
“Musade Nkhawa za Tsiku Lotsatira”
Renée anaona kuti zinthu zafika poipa kwambiri moti sangathenso kupirira. Mwamuna wake, Matthew, anali atakhala zaka zoposa zitatu asanapezebe ntchito yodalirika. Renée anati: “Zinthu sizinkandiyendera ngakhale pang’ono. Ndinkakhala wokhumudwa kwambiri chifukwa chosadziwa kuti mawa kugwa chiyani.” Matthew anayesetsa kumukhazika mtima pansi mkazi wake pomukumbutsa kuti nthawi zonse iwo ankapeza zinthu zimene ankafunikiradi pa moyo wawo. Koma Renée anayankha kuti: “Koma simunapezebe ntchito ndipo tikuvutika kupeza ndalama.”
NTCHITO ikatha, munthu amakhala ndi nkhawa. Iye amadzifunsa kuti, ‘Kodi ndikhala lova mpaka liti? Nanga pa nthawi imeneyi, ndizitha bwanji kusamalira banja langa?’
Ngakhale kuti n’zomveka kuti munthu amene sali pa ntchito akhale ndi nkhawa imeneyi, Yesu Khristu anapereka malangizo othandiza. Iye anati: “Musade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”—Mateyo 6:34.
Dziwani Zimene Zikukudetsani Nkhawa
Yesu sankatanthauza kuti tizikhala ngati tilibe mavuto. Iye ankatanthauza kuti kuda nkhawa ndi zimene tikuganiza kuti zichitika mawa, kumangowonjezera mavuto amene tili nawo panopa. Zoona zake n’zakuti sitingathe kusintha zinthu zimene zichitike mawa, kaya zikhale zabwino kapena zoipa. Koma tingathe kuchita zinthu zoti tithane ndi mavuto amene tikukumana nawo panopa.
Komatu nthawi zina zimakhala zophweka kungonena
zimenezi kusiyana ndi kuzichita. Rebekah, amene mwamuna wake anachotsedwa ntchito imene anakhala akugwira kwa zaka 12, anati: “Ukakhala ndi nkhawa kwambiri, zimavuta kuti uganize mwanzeru. Koma sitikanachitira mwina, tinkafunika kuganiza mwanzeru. Chotero, ndinkayesetsa kuti ndisamade nkhawa kwambiri. Nditaona kuti zinthu zimene ndinkaopa kwambiri kuti zichitika, sizinachitike, ndinazindikira kuti kuda nkhawa n’kosathandiza. Titayamba kuganizira za mavuto okhawo amene tikukumana nawo pa nthawiyo, zinatithandiza kuti tichepetse nkhawa pa moyo wathu.”Dzifunseni kuti: ‘Kodi n’chiyani chimene chimandidetsa nkhawa kwambiri? Kodi zinthu zomwe ndikuopazi zingachitikedi? Kodi ndimawononga nthawi yochuluka bwanji ndikudera nkhawa kuti zinthu zinazake zichitika, kapenanso ndikudera nkhawa kuti zinthu zinazake sizichitika?’
Muzikhutira ndi Zimene Muli Nazo
Kuti munthu akhale ndi nkhawa kapena ayi, zimadalira mmene amaonera zinthu. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti: ‘Pokhala ndi chakudya, zovala ndi nyumba, tizikhala okhutira ndi zinthu zimenezi.’ (1 Timoteyo 6:8) Kuti tizikhutira ndi zimene tili nazo, tisamalakelake kwambiri zinthu zosafunikira kwenikweni, ndipo tizikhutira ngati tikupeza zinthu zimene timafunikiradi tsiku ndi tsiku. Kuyesetsa kuti tikhale ndi zinthu zambirimbiri kukhoza kutilepheretsa kukhala ndi moyo wosalira zambiri.—Maliko 4:19.
Renée anayamba kukhutira ndi zimene anali nazo ataonanso bwinobwino mmene zinthu zinalili pa moyo wake. Iye anati: “Sitinakhalepo opanda magetsi kapena kusowa malo ogona. Vuto lalikulu linali lakuti tinali tisanazolowere kukhala moyo wokhala ndi ndalama zochepa. Popeza ineyo ndinkafunabe kuti tizikhala moyo wawofuwofu womwe tinali nawo poyamba, ndinkakhala ndi nkhawa kwambiri.”
Pasanapite nthawi yaitali, Renée anazindikira kuti ankavutika kupirira chifukwa cha mmene ankaonera zinthu, osati chifukwa cha mmene zinthu zinalili pa moyo wake. Iye anati: “Ndinafunika kuyamba kuvomereza kuti umu ndi mmene zinthu zilili, m’malo momangoganizira kuti ndikanakonda zinthu zikanakhala mwakutimwakuti. Nditayamba kukhutira ndi zimene Mulungu ankatipatsa tsiku ndi tsiku, ndinayambanso kusangalala.”
Dzifunseni kuti: ‘Kodi lero ndapeza zinthu zimene ndimafunikira? Ngati ndazipeza, kodi sindingachite bwino kusiya kudera nkhawa za mawa, pokhulupirira kuti zinthu zimene ndidzafunikire mawa ndidzazipezanso?’
Kuona zinthu moyenera ndi chiyambi chabe cha zinthu zimene tingachite kuti tikhale ndi moyo wosalira zambiri. * Koma kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene mungachite ngati mukupeza ndalama movutikira chifukwa chakuti ntchito yakutherani?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 14 Kuti mudziwe zinthu zina zimene zingakuthandizeni kupeza ntchito komanso kukhalitsa pantchito, onani Galamukani! ya July 8, 2005, masamba 3-11.
[Bokosi patsamba 5]
Khama Lipindula
Atayesetsa kufunafuna ntchito kwa milungu yambiri, Fred anayamba kuganiza kuti n’zosathekanso kuipeza. Iye anati: “Ndinkaona ngati ndikudikira munthu winawake pamalo okwerera basi kuti adzanditenge koma sakubwera.” Fred anazindikira kuti pali zinthu zambiri zimene sangathe kuzisintha, koma akhoza kusintha kafufuzidwe kake ka ntchito. Iye anatumiza makalata ofunsira ntchito kumakampani ambirimbiri, ngakhale amene ankaoneka kuti sangakhale ndi ntchito yoyenerana ndi luso lake. Fred ankapita kulikonse kumene amuitana kuti akamufunse mafunso okhudza ntchitoyo. Asanapite ankakonzekera bwino kwambiri, pozindikira kuti “zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu.” (Miyambo 21:5) Iye anati: “Pa nthawi ina, mabwana akuluakulu a kampani ina anandiitana maulendo awiri kukandifunsa mafunso ovuta kwambiri.” Koma khama la Fred linamupindulira chifukwa pamapeto pake analembedwa ntchito.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]
Chinthu Chofunika Kwambiri Kuposa Ndalama
Kodi chofunika kwambiri n’chiyani? Kukhala ndi khalidwe labwino kapena kupeza ndalama zambiri? Taonani malemba awiri a m’buku la Miyambo awa:
“Waumphawi woyenda mwangwiro apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera.”—Miyambo 28:6.
“Kudya masamba, pali chikondano, kuposa ng’ombe yonenepa pali udani.”—Miyambo 15:17.
Apa n’zoonekeratu kuti ngakhale munthu atasauka, amakhalabe wofunika chifukwa cha khalidwe lake labwino. Choncho mwamuna wa Renée atachotsedwa ntchito, Renée anauza ana ake kuti: “Muzinyadira kuti muli ndi bambo abwino kwambiri. Abambo ambiri amathawa ana awo. Koma bambo anu sanakuthaweni. Iwo amakukondani kwambiri ndipo akhala akukuthandizani pa mavuto anu onse.”