Ndinalowa Mpikisano Wabwino Kwambiri
Ndinalowa Mpikisano Wabwino Kwambiri
Yosimbidwa ndi Karl-Erik Bergman
Kuthamanga kunkandisangalatsa kwambiri. Komanso popeza ndinali ndi luso lachibadwa, ndinkakonda kwambiri kuthamanga kuposa chinthu china chilichonse pa moyo wanga.
MU 1972, ndili ndi zaka 17, ndinalowa m’gulu linalake la anthu ochita masewera othamanga. Pasanapite nthawi yaitali, ndinazindikira kuti ndili ndi chintchito chachikulu kuti ndifike pokhala katswiri. Luso lachibadwa si lokwanira kuti munthu akhale katswiri wothamanga. Koma ndinali wokonzeka kuchita chilichonse kuti ndikhale katswiri.
Nditakwanitsa zaka 22, ndinayamba kuthamanga mu timu ya dziko la Finland. M’chaka chotsatira ndinachita nawo mpikisano wothamanga mamita 100, ndipo ndinagonjetsa wothamanga aliyense ku Finland. Kenako ndinavulala bondo ndi phazi ndipo zimenezi zinachititsa kuti ndisamachite bwino kwenikweni. Komabe popeza ndinkakonda kwambiri kuthamanga, ndinayamba kuphunzitsa achinyamata amene ankafuna kudzakhala akatswiri othamanga. Mu 1982, ndinakonza zopita ku California, m’dziko la United States, kuti ndikachite maphunziro payunivesite inayake. Ndinkaona kuti pochita maphunziro anga payunivesiteyi, ndikakhala ndi mpata wokwanira wodziwa zambiri zokhudza masewera othamanga. Pokonzekera ulendowu, ndinaguliratu tikiti ya ndege.
Chomwe Chinachititsa Kuti Ndisinthe Maganizo
Tsiku lina madzulo, patangotsala masiku ochepa kuti ndinyamuke, ndinamva kugogoda pakhomo pa nyumba yanga. Nditatsegula chitseko, ndinapeza azimayi awiri a Mboni za Yehova. Iwo anali odekha ndiponso opanda mantha. Zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri chifukwa makhalidwe amenewa ndi ofunika kwambiri kwa munthu wothamanga. Ndinawauza kuti alowe ndipo tinakhala pansi n’kuyamba kukambirana. Tinakambirana mfundo zambiri zimene zinanditsegula m’maso, ndipo anandipatsa buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. * Nditawerenga bukuli mpaka kufika pakati, ndinazindikira kuti zimene ndikuwerengazo ndi choonadi. Azimayi aja atabweranso, ndinawapempha kuti andiuze zimene ndingachite kuti ndikhale wa Mboni za Yehova. Iwo anandiuza kuti ndikufunika kuyamba kuphunzira Baibulo.
Ndinayambadi kuphunzira Baibulo komanso ndinkapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu ya m’tawuni yakwathu, ku Vantaa. Ndinaona kuti zimene ankaphunzitsa pamisonkhanopo zinali zochokera m’Baibulo. Ndipo pang’ono ndi pang’ono, mfundo za choonadi zimene ndinkaphunzira zinayamba kusintha maganizo anga pa nkhani ya kuthamanga, komwe kunali kofunika kwambiri pa moyo wanga. Choncho, ndinapita kukampani
yokonza za maulendo a pa ndege kuti akandibwezere ndalama zomwe ndinagulira tikiti. Ndinapatula ndalama zina n’kugula suti yoti ndizivala popita kumisonkhano komanso chikwama choti ndizinyamulira Baibulo ndi mabuku ena. Mu 1983, ndinabatizidwa pa msonkhano wachigawo wa ku Helsinki, n’kukhala wa Mboni za Yehova.Akatswiri Ena Othamanga Anayambanso Kuphunzira Baibulo
Ndinkayesetsa kwambiri kuuza anzanga mfundo za m’Baibulo zimene ndinkaphunzira. Koma iwo sankandimvetsa, ndipo pankamveka mphekesera yakuti ndapenga. Anzanga anayamba kundithawa mmodzi ndi mmodzi. Nditabatizidwa, ndinkakumanabe ndi akatswiri anzanga othamanga chifukwa ndinkapitabe kumakathamanga n’cholinga chakuti ndilimbitse thupi. Nkhani zimene tinkacheza zinathandiza anzangawa kuona kuti sindinapenge, ngakhale kuti ndinasintha zolinga zanga.
M’kupita kwa nthawi, ambiri mwa akatswiri amenewa anayamba kuzindikira kuti zimene ndinkawauza zinali zomveka komanso zofunika kuziganizira bwinobwino. Anaona kuti ndasiya khalidwe langa lotukwana komanso la makani. Ena anayamba kuphunzira Baibulo. Ndinkasangalala kwambiri kuuza anthu kuti Baibulo limayerekezera Akhristu ndi akatswiri othamanga. Nthawi zambiri ndinkawauza kuti tili pa mpikisano womwe mphoto yake ndi moyo wosatha.—2 Timoteyo 2:5; 4:7, 8.
Ndinkawafotokozera kuti chofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi tsogolo labwino komanso wosangalala ndi kuchita zimene Mlengi wathu amasangalala nazo, osati chabe kupambana mipikisano yothamanga. Zimene ndinkakambirana ndi anzangawa zinachititsa kuti ena mwa iwo aunike bwinobwino zolinga zawo pa moyo. Ena anayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo zimene zinasintha moyo wanga zija. N’zosangalatsa kuti ambiri mwa akatswiri amenewa akhala akutumikira Mulungu modzipereka kwambiri ngati mmene ankadziperekera pa masewera othamanga.
Mmodzi wa anthu amenewa ndi Yvonne, yemwe anali katswiri zedi pa mipikisano yothamanga mamita 800. Iye anali mtsikana wothamanga kwambiri kuposa anzake onse ku Finland komanso ku Scandinavia konse. Nthawi zambiri ankapambana akakaimira dziko la Finland pa mipikisano yothamanga ya ku Ulaya. Chifukwa cha zimene tinkakambirana, Yvonne anayamba kuona kuti kukhala wotchuka kwambiri m’dzikoli kulibe phindu. Monga mmene Baibulo limanenera, iye anazindikira kuti dzikoli likupita, ndipo lilowedwa m’malo ndi dziko latsopano la Mulungu.—1 Yohane 2:17.
Pasanapite nthawi yaitali, Yvonne anayamba kuphunzira Baibulo. Pa nthawiyi, iye anali pa chibwenzi ndi Jouko, yemwe anali katswiri wothamanga m’timu ya dziko la Finland. Jouko anaimirapo dziko la Finland pa mipikisano yothamanga ya ku Ulaya komanso ya padziko lonse. M’kupita kwa nthawi, Yvonne ndi Jouko anasamukira ku United States kuti akapitirize masewera othamanga.
Ali kumeneko, Yvonne anapitiriza kuphunzira Baibulo, ndipo kenako Jouko nayenso anayamba kuphunzira nawo. Koma iye anachita zimenezi n’cholinga choti akapeza chinthu cholakwika, amuuze Yvonne kuti zinthu zimene akuphunzirazo si zabwino. Komabe pang’ono ndi pang’ono, choonadi cha m’Baibulo chinayamba kuzika mizu mumtima mwa Jouko. Yvonne ndi Jouko anakwatirana ndipo kenako anadzipereka kwa Mulungu n’kubatizidwa. Panopa awiri onsewa ndi apainiya, kapena kuti alaliki a nthawi zonse a Mboni za Yehova.
Ndinayambanso kuphunzira Baibulo ndi Barbro, yemwe anali katswiri wothamanga kwambiri m’timu ya atsikana othamanga mamita 400 ku Finland. Panthawiyi, n’kuti atangoimira kumene dziko la Finland mu mpikisano wothamanga umene unachitikira ku Ulaya. Barbro ndi mwamuna wake, Jarmo, yemwe anali katswiri wa masewera odumpha m’mwamba pogwiritsa ntchito mtengo, anasamukira ku Sweden. Ali kumeneku, Barbro anapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo kenako Jarmo anayambanso kuphunzira. Awiri onsewa ankafunitsitsa kudziwa cholinga cha moyo, ndipo ataphunzira choonadi, anabatizidwa ku Sweden komweko. M’kupita kwa nthawi, Jarmo anayamba ntchito yophunzitsa anthu kuchita masewera olimbitsa thupi, ndipo iye ndi mkazi wake ndi alaliki akhama. Jarmo ndi mkulu mumpingo.
Ndiye panali mtsikana winanso dzina lake Heidi, yemwe anali ndi zaka pafupifupi 15. Popeza ndinali mphunzitsi wake wa masewera, ndinaona kuti ankachita chidwi ndi zinthu zauzimu. Choncho, tsiku lina ndinamuuza zimene Baibulo limanena zokhudza Ufumu wa Mulungu ndiponso zinthu zabwino zimene ufumuwo udzabweretse padziko lapansi. Ndinamufunsa kuti, “Kodi ukukhulupirira kuti zimenezi zidzachitikadi?”—Salmo 37:11, 29; Mateyo 6:9, 10.
Iye anayankha kuti, “Inde, ndikukhulupirira.” Mtsikanayu ankafunitsitsa kuphunzira Baibulo, choncho ndinakonza zoti mlongo wina azimuphunzitsa. Patapita zaka zingapo, Heidi anadzipereka kwa
Mulungu n’kubatizidwa. Heidi anali mtsikana wokongola kwambiri ndiponso wokonda zinthu zauzimu. Patapita nthawi ine ndi Heidi tinakwatirana. Heidi ndi mkazi wabwino kwambiri. Mpaka pano, iye ndi wodzipereka kwambiri potumikira Mulungu, moti akanakhala kuti akuchitabe masewera othamanga ndi kudzipereka koteroko, akanakhala katswiri wotchuka kwambiri.Mng’ono wanga Peter, yemwenso anali katswiri wa masewera, sanasangalale nditayamba kuphunzira Baibulo. Ndinamupatsa buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi ndipo kenako anandiuza kuti, “Ndayamba kuwerenga bukuli, koma muli zina zimene sindikuzimvetsa. Kodi ungandithandize?” Ndinapempha m’bale wina kuti aziphunzira naye, ndipo ataphunzira kwa miyezi inayi, anabatizidwa. Kenako anakwatira ndipo mkazi wake panopa ndi mpainiya.
Ndikupitirizabe Kuchita Mpikisano
Ngakhale pa nthawi yomwe ndinali ndisanabatizidwe, ndinali ndi cholinga chodzakhala mmishonale. Choncho nditangobatizidwa, ndinayamba upainiya. Ndinkaona kuti ngati munthu ukuchita nawo mpikisano womwe mphoto yake ndi moyo wosatha, uyenera kuchita khama kwambiri kuti upambane. Ine ndi mkazi wanga Heidi tinafunsira kuti tilowe nawo sukulu ya Gileadi ya Mboni za Yehova ku New York, yomwe imaphunzitsa amishonale. Tinaitanidwa kukayamba sukuluyi mu 1994. Titamaliza, tinatumizidwa kukatumikira m’dziko la Latvia, momwe amalankhula chinenero cha Chirasha.
Kutha kwa ulamuliro wa Soviet Union kunachititsa anthu kukhumudwa ndi atsogoleri andale. Poyamba anthu ankaona kuti Baibulo lilibe ntchito ndipo boma linalamula kuti munthu aliyense asapezeke ndi Baibulo. Koma kenako tinaona kuti anthuwo ayamba kufuna kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Zinanditengera nthawi yaitali kuti ndiphunzire Chirasha. Nditakhala zaka 6 ku Latvia, ndinaikidwa kuti ndizigwira ntchito yoyendera ndiponso kulimbikitsa mipingo ya Mboni za Yehova. Mpaka pano, ine ndi mkazi wanga timagwirabe ntchito imeneyi.
Kwa zaka zambiri, ndakhala ndikuphunzitsa anthu kuti adzapambane pa mpikisano womwe mphoto yake ndi “moyo weniweni” m’dziko latsopano la Mulungu. (1 Timoteyo 6:19) Kuti munthu aphunzitse anthu othamanga n’kukhala akatswiri, amafunika kuwamvetsa. Mphunzitsiyo amafunika kuwathandiza kukulitsa luso lawo ndi kuchepetsa mavuto ena ndi ena amene ali nawo. Amafunikanso kuwalimbikitsa kuti azichita khama mpaka kufika pokhaladi akatswiri.
Zimandichititsa chidwi kwambiri kuona kuti Akhristu amafanana ndi akatswiri othamanga m’njira zambiri, ndipo zimenezi n’zogwirizana ndi zimene mtumwi Paulo ananena m’kalata yake yoyamba yopita kwa Akorinto. Kuti munthu wothamanga zimuyendere bwino, amafunika kuchita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse, ndipo sayembekezera kuti angapambane atangokhala. Iye amakhala ndi zolinga zimene akuona kuti atha kuzikwanitsa, ndipo amachita zinthu zimene zingamuthandize kuti akwanitse zolingazo. Iye amadziwa kuti ngati ataiwala cholinga chake n’kusiya kulimbikira, ndiye kuti zonse zimene wakhala akuchita m’mbuyomu zikhoza kungopita pachabe. Mofanana ndi zimenezi, Mkhristu weniweni nthawi zonse safunika kuiwala cholinga chake.
Katswiri wothamanga amafunikanso kuonetsetsa kuti chakudya chimene akudya n’choyenera. Iye samangodya zilizonse. N’chimodzimodzinso ndi Mkhristu. Mkhristu sayenera kumvetsera ziphunzitso zoipa, kapena kuti kudya pa “tebulo la ziwanda,” monga mmene Paulo ananenera. M’malomwake, amadya chakudya chabwino chauzimu chimene Mulungu amapereka kudzera m’Mawu ake, Baibulo. (1 Akorinto 10:21) Komanso munthu wothamanga akakumana ndi zokhoma, sataya mtima. Amavomereza zinthu zimene analakwitsa n’kuzikonza. Paulo analemba kuti: ‘Sindingothamanga osadziwika kumene ndikulowera. Koma ndipumphuntha thupi langa kuopera kuti ndingakhale wosayenera.’—1 Akorinto 9:24-27.
Ine ndi mkazi wanga timakondabe kuchita masewera olimbitsa thupi kuti tikhalebe ndi mphamvu. Komabe, sitimachita zimenezi mopitirira malire mpaka kutilepheretsa kutumikira Yehova, yemwe analenga anthu modabwitsa kwambiri. (Salmo 139:14) Cholinga chathu n’chakuti tidzalandire mphoto ya “moyo weniweni,” moyo “umene ukubwerawo,” m’dziko latsopano la Mulungu.—1 Timoteyo 4:8.
Atafotokoza za “mtambo wa mboni” umene unakhalako Chikhristu chisanayambe, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti: “Tiyeninso tivule cholemera chilichonse ndi tchimo lija lotikola mosavuta. Ndipo tithamange mopirira mpikisano umene atiikirawu.” (Aheberi 12:1) Palibenso chinthu china chopindulitsa kwambiri m’dzikoli kuposa kuchita nawo mpikisano umenewu, womwe mphoto yake ndi moyo wosatha.—2 Timoteyo 4:7, 8.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma panopa anasiya kulisindikiza.
[Chithunzi patsamba 14]
Cha m’ma 1985, ine ndi mkazi wanga Heidi, Yvonne pamwambapo, ndi Jouko atanyamula mwana wawo pansipo
[Chithunzi patsamba 15]
Ndikulalikira ndi mkazi wanga Heidi posachedwapa
[Chithunzi patsamba 15]
Pamsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova ku Helsinki, mu 2009. Ali kumanzere kwathuwa ndi Yvonne ndi Jouko ndipo ali kumanja kwathuwa ndi Jarmo ndi Barbro
[Mawu a Chithunzi patsamba 12]
Published in Aamulehti 8/21/1979