Kodi Alipo Amene Tingamukhulupirire?
Kodi Alipo Amene Tingamukhulupirire?
Dokotala wina ankalemekezedwa kwambiri chifukwa cholemba nkhani zosiyanasiyana zokhudza ubwino wogwiritsa ntchito mankhwala enaake opha ululu. Nkhani zimene iye ankalemba zinkafalitsidwa m’magazini otchuka kwambiri azachipatala. Koma kwa zaka zoposa 10, kuyambira mu 1996, nkhani zambiri zimene dokotalayu ankafalitsa zinali zabodza. Iye ankasintha zotsatira za kafukufuku wake.
NYUZIPEPALA ina inagwira mawu dokotala wina, dzina lake Steven L. Shafer, yemwe anati: “Zikundivuta kumvetsa kuti munthu wabwinobwino angachite bwanji zinthu zachinyengo ngati zimenezi.”—Anesthesiology News.
Kodi n’chiyani chingachititse munthu wodziwa bwino ntchito yake amene anthu amamulemekeza kwambiri kuchita zachinyengo? Ganizirani zinthu zinayi izi:
● Dyera. M’nyuzipepala ya New York Times, Dr. Jerome Kassirer, yemwe anali mkonzi wa magazini inayake ya zachipatala, anati: “Akatswiri ochita kafukufuku akamapeza ndalama zawo zambiri kuchokera ku makampani [opanga mankhwala], nthawi zambiri amasintha zotsatira za kafukufuku wawo n’cholinga choti zikhale zokomera makampaniwo.”
● Kufuna kuti zake ziyende basi. Anthu ena akuti ku Germany, ana a sukulu amene amatenga maphunziro a sayansi ankapatsa aphunzitsi awo ndalama zambirimbiri n’cholinga choti akhoze bwino n’kumadziwika ndi dzina lakuti “Dokotala.” M’dzikolo, munthu akamadziwika ndi dzina limeneli, amalemekezedwa kwambiri. Pa kafukufuku wina amene analembedwa m’nyuzipepala ya New York Times, ofufuza anapeza kuti ophunzira ambiri amene amadutsa njira zamadulira n’cholinga choti ziwayendere, ananena kuti adzayamba “kuyesetsa kuchita zachilungamo” zinthu zikadzawayendera.
● Kusowa kwa anthu achitsanzo chabwino. Ponena za ana a ku sekondale, nyuzipepala ya New York Times inalemba zimene pulofesa wina ananena, kuti: “Tingathamangire kunena kuti anawa
asiya kutsatira mfundo za makhalidwe abwino. . . . Koma mwina tingachite bwino kunena kuti aphunzitsi ndi alangizi awo komanso anthu ena onse sanawathandize ngakhale pang’ono kukhala ndi khalidwe labwino.”● Anthu sakutsatira mfundo zabwino zimene amakhulupirira. Pa kafukufuku wina wokhudza ana 30,000, ana 98 pa 100 alionse ananena kuti amakhulupirira kuti chilungamo n’chofunika. Komabe, ana 80 pa 100 alionse anavomera kuti ananamizapo makolo awo, ndipo ana 64 pa 100 alionse anavomera kuti anabera mayeso chaka chapitacho.
Mfundo Zabwino Kwambiri Zokhudza Makhalidwe
Monga momwe bokosi la patsamba lino likusonyezera, mwachibadwa anthufe timakhulupirirana. Komabe, Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti “maganizo a anthu amakhala oipa kuyambira pa ubwana wawo.” (Genesis 8:21) Kodi tingatani kuti tigonjetse maganizo amenewa n’kupewa moyo wachinyengo umene wafala masiku ano? Mfundo za m’Baibulo zotsatirazi zingatithandize:
● “Usakonze zochitira mnzako choipa, pamene iye akuona kuti akukhala nawe mwamtendere.”—Miyambo 3:29.
Ngati timakonda anthu anzathu, timawachitira zabwino. Anthu amene amatikhulupirira sitiwachitira zachinyengo chifukwa chowapezerera. Kutsatira mfundo imeneyi kungathandize anthu kusiya nkhanza zimene amachitira anzawo chifukwa cha dyera, monga kugulitsa mankhwala achabechabe kumene tatchula m’nkhani yoyambirira ija.
● “Mlomo wa choonadi ndi umene udzakhazikike kwamuyaya, koma lilime lachinyengo lidzangokhalapo kwa kanthawi.”—Miyambo 12:19.
Anthu ambiri masiku ano amaganiza kuti munthu wachilungamo zinthu sizingamuyendere. Koma dzifunseni kuti, ‘Kodi chofunika kwambiri n’chiyani pakati pa kuchita zinthu mwachinyengo kuti ndipeze mwachangu zimene ndikufuna, ndi kuchita zinthu mwachilungamo kuti zidzandiyendere bwino m’tsogolo komanso kuti anthu apitirize kundilemekeza?’ Mwachitsanzo, mwana wa sukulu angabere mayeso, anthu n’kumamuona ngati wanzeru, koma kodi zingadzamuyendere bwanji kuntchito?
● “Munthu wolungama amayenda ndi mtima wosagawanika, ndipo ana ake amakhala odala.”—Miyambo 20:7.
Ngati ndinu kholo, muzipereka chitsanzo chabwino kwa ana anu pokhala ndi “mtima wosagawanika.” Muziwafotokozera zabwino zimene mwakumana nazo pa moyo wanu chifukwa chochita zinthu mwachilungamo. Ana akaona kuti kholo lawo limachita zinthu mwachilungamo, nawonso akhoza kutengera chitsanzo chomwecho.—Miyambo 22:6.
Kodi mfundo za m’Baibulo zomwe zili pamwambazi zimathandizadi? Kodi masiku ano n’zotheka kupeza anthu amene mungawakhulupirire?
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Malinga ndi nyuzipepala ya Le Figaro, masiku ano anthu ambiri ku France “akuganiza kuti anthu amene ali ndi udindo wolemekezeka monga andale, azachuma, ndi akuluakulu ena alibe khalidwe labwino, choncho saona kufunika koti iwowo akhale ndi khalidwe labwino.”
[Bokosi patsamba 5]
KUKHULUPIRIRANA N’KWACHIBADWA
Pulofesa wina wa pa yunivesite ya Frankfurt ku Germany, dzina lake Michael Kosfeld, atachita kafukufuku anapeza kuti “kukhulupirirana kukuoneka kuti ndi mbali ya chibadwa cha anthu.” Kosfeld anapeza kuti anthu awiri akamachita zinthu limodzi, ubongo wawo umatulutsa mankhwala enaake amene amawachititsa kuyamba kukhulupirirana. Iye anati: “Ichi ndi chimodzi mwa zinthu zimene zimasiyanitsa anthu ndi zamoyo zina. Anthu akasiya kukhulupirirana, sakhalanso ngati anthu.”