Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndisiye Sukulu?

Kodi Ndisiye Sukulu?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndisiye Sukulu?

Kodi mukuganiza kuti muyenera kusiya sukulu mutafika nayo pati?

․․․․․

Kodi makolo anu amafuna kuti mudzasiyire pati?

․․․․․

KODI zimene mwayankha pa funso loyamba ndi lachiwiri zikufanana? Ngakhale kuti mwina zimene inu mumafuna n’zofanana ndi zimene makolo anu amafuna, n’kutheka kuti masiku ena mumalakalaka mutangosiya sukulu. Kodi munayamba mwaganizapo zofanana ndi zimene zili m’munsizi?

“Masiku ena sukulu inkanditopetsa kwambiri moti sindinkafuna kudzuka m’mawa. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi ndimadzivutitsiranji kupita kusukulu n’kumakaphunzira zinthu zoti sindidzazigwiritsa ntchito n’komwe?’”—Anatero Rachel.

“Nthawi zambiri ndinkatopa ndi sukulu ndipo ndinkangofuna nditaisiya n’kumakafufuza ntchito. Ndinkaona kuti sukulu sikundipindulira, ndipo ndikungowononga nthawi yanga.”—Anatero John.

“Masiku ena ndinkakhala ndi homuweki yomwe inkanditengera maola anayi usiku uliwonse kuti ndithane nayo. Tsiku lililonse ndinkakhala ndi zinthu zosiyanasiyana za kusukulu zoti ndichite ndipo zinafika pondikwana moti ndinkaona kuti ndi bwino ndingosiya sukulu.”—Anatero Cindy.

“Kusukulu kwathu kunkachitika zoopsa zambiri. Tsiku lina tinathawa titaopsezedwa kuti wina watchera bomba pasukulupo. Nthawi ina ana a sukulu atatu anayeserapo kudzipha. Ndipo mwana wa sukulu wina anadzipha. Ndiponso ana a sukulu anapanga magulu omwe nthawi zambiri ankamenyana. Chifukwa cha zonsezi, ndinkafuna kungosiya sukulu.”—Anatero Rose.

Kodi nanunso munakumanapo ndi zinthu ngati zimenezi? Kodi inuyo vuto limene limakuchititsani kuganiza zofuna kusiya sukulu ndi lotani?

․․․․․

Mwina panopa mukufunadi kusiya sukulu. Koma kodi mungadziwe bwanji kuti mukufuna kusiya chifukwa chakuti ndi nthawidi yabwino yoti musiye, kapena mwangotopa nayo?

Kodi Ndi Nzeru Kusiya Sukulu?

Kodi mukudziwa kuti m’mayiko ena, mwana amaloledwa kusiya sukulu atangophunzira kwa zaka 5 kapena 8 zokha? M’mayiko enanso, ana amafunika kuphunzira sukulu kwa zaka 10 kapena 12. Choncho, mayiko osiyanasiyana ali ndi malamulo osiyanasiyananso pa nkhani ya zaka zimene mwana amayenera kuphunzira sukulu.

Komanso m’mayiko ena, mwana akhoza kumachitira maphunziro ake ena kapena onse kunyumba, popanda kupita kusukulu. Ana amene amaphunzirira kunyumba movomerezedwa ndi makolo awo, sali m’gulu la ana amene asiya sukulu.

Komabe, ngati mukuganiza zosiya sukulu musanamalize maphunziro anu, kaya mumaphunzirira kunyumba kapena kusukulu, muyenera kudzifunsa kaye mafunso otsatirawa.

Kodi malamulo a boma amati chiyani? Si bwino kusiya sukulu ngati zimenezi zingachititse kuti muphwanye malangizo a m’Baibulo akuti, “munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.”—Aroma 13:1.

Kodi ndakwanitsa zolinga zanga? Kodi zolinga zanu zopitira kusukulu n’zotani? Mukufunika kudziwa zimenezi chifukwa ngati simutero, mungakhale ngati munthu amene wakwera sitima koma sakudziwa kumene akufuna kupita. Choncho, thandizanani ndi makolo anu kudzaza chipepala chakuti  “Zolinga Zanga pa Nkhani ya Sukulu,” chomwe chili patsamba 28. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuika maganizo anu pa maphunziro.—Miyambo 21:5.

Kodi ndikufuna ndisiye sukulu chifukwa chiyani? Samalani kuti musadzinyenge nokha. (Yeremiya 17:9) Anthu amakonda kupeza zifukwa zooneka ngati zomveka akafuna kuchita zinthu zowakomera.—Yakobo 1:22.

Lembani m’munsimu zifukwa zina zosamveka kwenikweni zimene mungafunire kusiya sukulu.

․․․․․

Kodi mwalemba zifukwa zotani? Zifukwa zina zingakhale monga kuopa mayeso kapena kuthawa homuweki. Nkhani yagona poti muyenera kudzifunsa chifukwa chachikulu chimene mukufuna kusiyira sukulu. Ngati mukufuna kusiya pa zifukwa zosamveka, dziwani kuti mudzakhumudwa kwambiri.

Kodi Vuto ndi Chiyani Ngati Nditasiya Sukulu?

Kusiya sukulu kuli ngati kudumpha m’sitima musanafike kumene mukupita. Mwina mungaganize zodumpha m’sitimayo chifukwa chakuti si yawofuwofu komanso anthu amene mwakwera nawo akukusowetsani mtendere. Koma ngati mutachita zimenezi, simungafike kumene mumapita komanso mukhoza kuvulala kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi sukulu. Ngati mutaisiyira pa njira, simungakwanitse zolinga zimene munali nazo, komanso pali mavuto odziwikiratu amene mungakumane nawo, ndi enanso amene mwina simunawaganizire.

Mavuto odziwikiratu Mungavutike kupeza ntchito, ndipo ngati mutaipeza, mukhoza kumalandira ndalama zochepa kwambiri kusiyana n’zimene mukanati muzilandira mukanakhala kuti munamaliza sukulu. Kuti muthe kupeza zofunikira pa moyo wanu, mungafunike kumagwira ntchito kwa maola ambiri komanso m’malo osasangalatsa kuposa mmene kulili kusukulu kwanu panopa.

Mavuto amene mwina simunawaganizire Kafukufuku wasonyeza kuti anthu ambiri amene amasiyira sukulu pa njira amadwaladwala, amabereka ali aang’ono, ndiponso amatha kuyamba kuchita zinthu zimene angathe kumangidwa nazo.

Sikuti munthu amene wamaliza sukulu sangakumane ndi mavuto ngati amenewa. Koma si nzeru kusiyira sukulu pa njira pamene mukudziwa kuti mungathe kudzakumana ndi mavuto ngati amenewa.

Ubwino Womaliza Sukulu

N’zoona kuti ngati mwangolephera kumene mayeso kapena ngati zinthu sizinakuyendereni bwino kusukulu tsiku limenelo, mungaganize zongosiya sukulu. Mungaone ngati mavuto amene tikunenawa ndi ochepa poyerekezera ndi mavuto amene mukukumana nawo panopa. Koma musanaganize zotenga njira yachidule, ganizirani zimene ana a sukulu omwe tawagwira mawu aja ananena za mmene kumaliza sukulu kunawathandizira.

“Ndaphunzira kupirira ndipo zimenezi zandithandiza kuti ndikhale wolimba. Ndaphunziranso kuti ngati munthu ukufuna kuti chinachake chizikusangalatsa, uyenera kuchita khama. Maganizo amenewa andithandiza kuti ndizichita bwino pa phunziro la zojambulajambula, limene lidzandithandize kupeza ntchito mosavuta ndikamaliza sukulu.”—Anatero Rachel.

“Tsopano ndadziwa kuti ngati nditalimbikira, ndingakwanitse zolinga zanga. Ndikuchita maphunziro enaake a ku sekondale, amene adzandithandize kupeza ntchito imene ndimafuna yokonza makina osindikizira mabuku.”—Anatero John.

“Sukulu yandithandiza kuti ndiziganiza bwino kwambiri, kaya pa zinthu za kusukulu kapena zinthu zina. Kupeza njira zothetsera mavuto amene ndimakumana nawo kusukulu, amene ndimakumana nawo ndikamachita zinthu zosiyanasiyana ndi anthu, ndiponso mavuto ena pa moyo wanga, kwandithandiza kwambiri kukhwima maganizo.”—Anatero Cindy.

“Sukulu inandithandiza kukonzekera kudzalimbana ndi mavuto akuntchito. Komanso, kusukulu kunkachitika zinthu zambiri zimene zinkandichititsa kuganizira mozama za zinthu zimene ndimakhulupirira. Choncho kukhala pa sukulu kwalimbitsa chikhulupiriro changa.”—Anatero Rose.

Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake, ndipo munthu woleza mtima ndi wabwino kuposa munthu wodzikuza.” (Mlaliki 7:8) Choncho m’malo mongosiya sukulu, lezani mtima ndipo phunzirani kuthana ndi mavuto amene mumakumana nawo kusukulu. Mukatero, mudzaona kuti pa mapeto pake zinthu zidzakuyenderani bwino kwambiri.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.dan124.com.

ZOTI MUGANIZIRE

● Kodi kukhala ndi zolinga zokhudzana ndi maphunziro anu zimene mungazikwanitse pa nthawi yochepa, kungakuthandizeni bwanji?

● Kodi kudziwa ntchito imene mumafuna kudzagwira mukadzamaliza sukulu n’kofunika bwanji?

[Bokosi/Zithunzi patsamba 27]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

Sukulu ndi imene inandiphunzitsa kukonda kuwerenga. Zimasangalatsa kwambiri kumvetsetsa maganizo a munthu wina powerenga zimene iye walemba.

Zimandivuta kugawa bwino nthawi yanga. Koma ndikanati ndisapite kusukulu, zinthu zikanaipa kuposa pamenepa. Sukulu imandithandiza kukhala ndi ndondomeko yochitira zinthu n’kumaitsatira. Zimenezi zimandithandiza kukwanitsa kuchita zinthu zofunika.

[Zithunzi]

Esme

Christopher

[Bokosi patsamba 28]

ZOLINGA ZANGA PA NKHANI YA SUKULU

Cholinga chachikulu cha maphunziro n’choti mudzathe kupeza ntchito imene ingadzakuthandizeni kupeza zinthu zimene mumafunikira pa moyo wanu, komanso kuti mudzathe kusamalira banja ngati mungadzakhale nalo m’tsogolo. (2 Atesalonika 3:10, 12) Kodi munasankha kale ntchito imene mumafuna kudzagwira? Nanga kodi sukulu ingakuthandizeni bwanji kukonzekera ntchito imeneyi? Kuti mudziwe ngati sukulu ikukuthandizani kuti mudzakwanitse zimene mumafuna, yankhani mafunso otsatirawa:

Kodi ndimachita bwino pa zinthu zotani? (Mwachitsanzo, kodi mumacheza bwino ndi anthu? Kodi mumakonda ntchito zamanja, monga kupanga zinthu zatsopano kapena kukonza zinthu zowonongeka? Kodi mumakonda kufufuza nkhani bwinobwino n’kuona mmene mungaithetsere?)

․․․․․

Kodi ndi ntchito zotani zimene zingagwirizane ndi zinthu zimene ndimachita bwino?

․․․․․

  Kodi kudera kwathu kumapezeka ntchito zotani?

․․․․․

Kodi panopa ndikutenga maphunziro otani amene angadzandithandize kupeza ntchito?

․․․․․

Kodi panopa ndingathe kuchita maphunziro otani amene angandithandize kuti ndisadzavutike kukwanitsa zolinga zanga?

․․․․․

Kumbukirani kuti cholinga chanu n’choti mukamadzamaliza sukulu, mudzathe kupeza chochita. Koma musakhalenso ngati anthu amene amangofuna kumangophunzirabe mpaka kalekale, ngati munthu amene sakufuna kutsika sitima, pongofuna kupewa udindo.

[Bokosi patsamba 29]

MAWU KWA MAKOLO

“Aphunzitsi athu amaphunzitsa motopetsa.” “Ndimakhala ndi homuweki yochuluka kwambiri.” “Sindiona chifukwa cholimbikirira sukulu chifukwa ngakhale ndilimbikire chotani, sindimakhoza bwino.” Izi ndi zina mwa zifukwa zimene zimachititsa achinyamata ena kuganiza zongosiyira sukulu pa njira asanaphunzire zinthu zimene zidzawathandize kupeza zinthu zofunikira pa moyo wawo. Ngati mwana wanu akufuna kusiya sukulu, kodi mungatani?

Kodi inuyo sukulu munkaiona bwanji? Kodi munkaona kuti kupita kusukulu ndi kungotaya nthawi kapenanso kuti sukulu ili ngati ndende, yongofunika kuipirira mpaka tsiku limene mudzatulukemo n’kuyamba kuchita zinthu zina zosangalatsa? Ngati munkaiona choncho, ana anu akhozanso kutengera zomwezo. Koma choti mudziwe n’chakuti ngati ana anu ataphunzira mokwanira zingawathandize kuti akhale ndi ‘nzeru zopindulitsa ndiponso kuti aziganiza bwino.’ Zimenezi zingawathandize kuti akadzakula zinthu zidzawayendere bwino.—Miyambo 3:21.

Muzipatsa ana anu zinthu zowathandiza pa maphunziro awo. Ana ena angamakhoze bwino atangodziwa mmene angamawerengere komanso atakhala ndi malo abwino owerengera. Malo abwino owerengera amafunika kukhala owala bwino. Pamafunikanso desiki losakhala ndi zinthu zambirimbiri komanso mabuku okwanira. Mungathandize mwana wanu kuchita bwino pa maphunziro ake komanso pa zinthu zauzimu poonetsetsa kuti ali ndi malo abwino amene angakhale n’kumawerenga ndiponso kuganizira zinthu mozama, komanso pomuthandiza kuchita zimenezi.—1 Timoteyo 4:15.

Muzidziwa bwino zimene mwana wanu akuchita kusukulu. Muziona aphunzitsi a ana anu ngati anzanu, osati adani anu. Muzipita kukakumana nawo ndipo muziwadziwa bwino. Muzikambirana nawo nkhani zokhudza zolinga za mwana wanu komanso za mavuto amene akukumana nawo. Ngati mwana wanu sakukhoza bwino, yesetsani kudziwa chifukwa chake. Mwachitsanzo, kodi mwana wanu akuona kuti akamakhoza bwino m’kalasi anzake azimuvutitsa? Kodi sagwirizana ndi mphunzitsi winawake? Kodi akutenga maphunziro oyenera? Muzionetsetsa kuti mwana wanu sakusankha maphunziro ovuta kwambiri amene angangomugwetsa mphwayi. Fufuzaninso ngati mwana wanu ali ndi vuto linalake monga lokhudza maso kapena matenda enaake amene akumuchititsa kuti asamakhoze bwino m’kalasi.

Mukamayesetsa kudziwa bwino zimene mwana wanu akuchita kusukulu ndiponso pa moyo wake wauzimu, mwana wanuyo adzayamba kuchita bwino.—Miyambo 22:6.

[Chithunzi patsamba 29]

Kusiyira sukulu pa njira kuli ngati kudumpha m’sitima musanafike kumene mukupita