Kodi Zinthu Zingayambe Kuyenda Bwino Padzikoli Patakhala Kuti Palibe Zipembedzo?
Kodi Zinthu Zingayambe Kuyenda Bwino Padzikoli Patakhala Kuti Palibe Zipembedzo?
GULU latsopano la anthu okhulupirira zoti kulibe Mulungu limanena kuti zinthu zingayambe kuyenda bwino padzikoli patakhala kuti palibe zipembedzo. Iwo amaganiza kuti kutakhala kuti kulibe zipembedzo, ndiye kuti sikungakhalenso anthu ophulitsa mabomba atinkenawo, nkhondo zachipembedzo ndiponso atsogoleri achipembedzo amene amabera anthu ndalama. Kodi inuyo mukugwirizana ndi maganizo amenewa?
Musanayankhe funso limeneli, dzifunseni kuti, ‘Kodi pali umboni uliwonse wosonyeza kuti zinthu zingamayende bwino ngati anthu onse atamakhulupirira zoti kulibe Mulungu?’ Taganizirani izi: Anthu pafupifupi 1.5 miliyoni anafa ku Cambodia pamene gulu la Khmer Rouge linkafuna kukhazikitsa boma losakhulupirira Mulungu potengera ziphunzitso za Karl Marx. Komanso pa nthawi imene Joseph Stalin ankalamulira dziko la USSR, lomwe linakhazikitsa lamulo loti m’dzikolo musapezeke chipembedzo chilichonse, anthu mamiliyoni ambiri anaphedwa. N’zoona kuti sitinganene kuti kusakhulupirira zoti kuli Mulungu n’kumene kunachititsa kuti anthu onsewa aphedwe. Komabe, zimenezi zikusonyeza kuti ulamuliro wa anthu omwe sakhulupirira zoti kuli Mulungu suchititsa kuti anthu azikhala mwamtendere ndiponso mogwirizana.
Aroma 3:23) Uchimo wobadwa nawo ndi umene umachititsa anthu kukhala odzikonda, onyada, osafuna kuuzidwa zochita komanso achiwawa. (Genesis 8:21) Kubadwa ndi uchimo kumachititsanso kuti anthu azipeputsa zolakwa zawo komanso azikonda zikhulupiriro zimene zimalekerera zinthu zoipa. (Aroma 1:24-27) M’pake kuti Yesu Khristu ananena kuti: “Maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama, za kuba, maumboni onama, ndi zonyoza Mulungu, zimachokera mumtima.”—Mateyu 15:19.
Anthu ambiri angavomereze kuti chipembedzo chachititsa mavuto ambiri. Koma kodi vuto ndi la Mulungu? Ayi. Si bwino kuimba Mulungu mlandu. Kuchita zimenezi kuli ngati kuimba mlandu kampani yopanga magalimoto chifukwa chakuti galimoto ina yachita ngozi pomwe dalaivala wake amaiyendetsa uku akulankhula pafoni yam’manja. Pali zinthu zambiri zimene zikuyambitsa mavuto amene anthu akukumana nawo. Chimodzi mwa zinthu zimenezi sichikukhudzananso n’komwe ndi kukhulupirira kuti kuli Mulungu kapena ayi. Baibulo limanena kuti chinthu chimenechi ndi kupanda ungwiro. Limati: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Tiyenera Kusiyanitsa Chipembedzo Choona ndi Chonyenga
Tisanapite patali, ndi bwino kusiyanitsa chipembedzo choona chimene Mulungu amavomereza, ndi chipembedzo chonyenga. Chipembedzo choona chimathandiza anthu kulimbana ndi makhalidwe oipa amene amachita chifukwa cha kupanda ungwiro. Chimathandizanso anthu kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi chololera kuvutikira ena, mtendere, kukoma mtima, ubwino, kufatsa, kudziletsa, kukhulupirika m’banja komanso kulemekezana. (Agalatiya 5:22, 23) Mosiyana ndi zimenezi, chipembedzo chonyenga chimangophunzitsa zimene anthu ambiri angakonde kumva. Chimalekerera makhalidwe oipa amene Yesu ankadzudzula, ndipo malinga ndi zimene Baibulo limanena, chimangouza anthu zinthu “zowakomera m’khutu.”—2 Timoteyo 4:3.
Chipembedzo chonyenga chachititsa kuti anthu asamadziwe mfundo zabwino zoyenera kutsatira. Kodi kukhulupirira zoti Mulungu kulibe kungachititsenso zomwezi? Pulofesa wina wazamalamulo, dzina lake Phillip Johnson, ananena kuti anthu akamakhulupirira zoti kulibe Mulungu, saopanso kuimbidwa mlandu ndi Mulunguyo, komanso “sakhala ndi mfundo zilizonse zimene amaona kuti ayenera kutsatira.” Choncho, munthu aliyense amangoyendera mfundo zake pa nkhani ya makhalidwe. Zimenezi n’zimene zimachititsa kuti anthu ena azikopeka ndi chikhulupiriro chakuti kulibe Mulungu.—Salimo 14:1.
Koma chimene tiyenera kudziwa n’chakuti, Mulungu sadzalekerera chinyengo mpaka kalekale, kaya cha zipembedzo kapena cha anthu amene amakhulupirira zoti kulibe Mulungu. * Iye analonjeza kuti: “Owongoka mtima [amene amakhulupirira zoona zokhudza Mulungu komanso amene ali ndi makhalidwe abwino] ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo. Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi ndipo achinyengo adzazulidwamo.” (Miyambo 2:21, 22) Zimenezi zikadzachitika, padziko lonse anthu adzayamba kukhala mwamtendere komanso mosangalala. Palibe munthu aliyense, mfundo zilizonse za anthu, kapena bungwe lililonse la anthu limene lingakwanitse kuchita zimenezi.—Yesaya 11:9.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Mukafuna kudziwa mfundo zomveka bwino za m’Baibulo zofotokoza chifukwa chake Mulungu walola kuti zoipa zizichitika, werengani mutu 11 wa buku lophunzirira Baibulo lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Bokosi patsamba 6]
KODI MULUNGU AMAZIONA BWANJI NKHANZA ZIMENE ZIPEMBEDZO ZIMACHITA?
Dziko limene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli, poyamba linali la Akanani. Akanani ankachita zinthu zachiwerewere zamtundu uliwonse monga kugonana pachibale, kugonana amuna okhaokha, komanso kugonana ndi nyama. Iwo ankaperekanso ana awo nsembe. (Levitiko 18:2-27) Buku lina lofotokoza za zinthu zokumbidwa pansi komanso zotchulidwa m’Chipangano Chakale, linanena kuti akatswiri okumba zinthu zakale “apeza milu yambirimbiri ya phulusa ndi mafupa a tiana m’manda apafupi ndi maguwa a nsembe a milungu yachikunja, zomwe zikusonyeza kuti anthu ambiri [ankawotcha ana awo popereka nsembe].” Buku lina lofotokozera Baibulo linanena kuti Akanani ankachita zachiwerewere polambira milungu yawo ndipo ankaperekanso ana awo oyamba kubadwa kwa milungu yomweyo. Bukuli linanenanso kuti: “Akatswiri amene anafukula zinthu zakale m’mizinda ya ku Kanani amadabwa kuti Mulungu sanawononge anthuwo mwamsanga.”
Kuwonongedwa kwa Akanani kuyenera kutichenjeza kuti Mulungu sadzalekerera mpaka kalekale anthu ochita zonyansa m’dzina lake. Lemba la Machitidwe 17:31 limati: “[Mulungu] wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu.”
[Zithunzi patsamba 7]
Anthu osapembedza ndi opembedza omwe akhala akuchita nkhanza zosaneneka
Zipembedzo zinkathandiza Hitler
Mafupa a anthu amene anaphedwa ndi gulu la Khmer Rouge ku Cambodia
[Mawu a Chithunzi]
AP Photo