Chivomezi cha ku Haiti Chinapereka Mpata Wosonyeza Chikhulupiriro ndi Chikondi
Chivomezi cha ku Haiti Chinapereka Mpata Wosonyeza Chikhulupiriro ndi Chikondi
Lachiwiri, pa January 12, 2010, nthawi ili 4:53 madzulo, Evelyn anamva chiphokoso changati cha ndege yaikulu ndipo nthawi yomweyo nthaka inayamba kugwedezeka. Kenako nyumba zapafupi zinayamba kugwa ndipo kugwa kwa nyumbazi kunachititsanso chiphokoso chachikulu. Kugwedezeka kwa nthakako kutasiya, Evelyn anathawa n’kukaima pamalo okwera kuti aone bwinobwino zimene zikuchitika. Iye ankamva paliponse anthu ambirimbiri akulira. Anaona chifumbi cha nyumba zogumuka chikukwera m’mwamba ngati chimtambo chachikulu. Chifumbicho chinadzaza mumzinda wonse wa Port-au-Prince, womwe ndi likulu la dziko la Haiti.
M’KANTHAWI kochepa chabe, nyumba za anthu, maofesi a boma, mabanki, zipatala ndi masukulu zinagwa. Anthu oposa 220,000 anafa ndipo ena pafupifupi 300,000 anavulala.
Anthu ambiri amene anapulumuka pa chivomezichi anangokhalakhala pafupi ndi nyumba zawo zogumuka, ali kakasi. Ena ankayesetsa kufukula ndi manja abale awo ndi anthu ena oyandikana nawo nyumba amene anakwiririka ndi nyumba zakugwa. Mapolo a magetsi anagwa ndipo kunali mdima wandiweyani. Choncho, pofufuza anthu amene anakwiririka, ankagwiritsa ntchito matochi ndi makandulo.
Mumzinda wa Jacmel, mnyamata wina wazaka 11, dzina lake Ralphendy, anapsinjika ndi nyumba yosanja imene inagwa mbali imodzi. Kwa maola angapo, gulu lina la mumzindawo lopulumutsa anthu linayesetsa mwakhama kuti limutulutse, koma chifukwa cha zivomezi zing’onozing’ono zimene zinkachitika pambuyo pa chivomezi chachikulu chija, gululo linamusiya. Linkaopa kuti mbali yotsala ya nyumbayo iwagweranso. Koma Philippe, mmishonale wa Mboni za Yehova, sanafune kumusiya. Iye anati: “Sindikanatha kungomusiya Ralphendy akufa.”
Philippe ndi anthu ena atatu anadzipanikiza pakampata kenakake kakang’ono n’kuyamba kuyenda pang’onopang’ono kupita pamene panali Ralphendy. Mapazi a mnyamatayu anali atapsinjidwa ndi zinthu zosiyanasiyana zomwe zinagwa. Kuyambira pakati pa usiku, iwo anayesetsa kuchotsa mosamala zinthu zimene zinamupsinjazo. Pakachitika chivomezi chilichonse chaching’ono, iwo ankamva makoma akusuntha komanso akung’aluka. Pofika 5 koloko m’mawa, patatha maola opitirira 12 kuchokera pamene chivomezichi chinachitika, anakwanitsa kutulutsa Ralphendy.
Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu opulumutsa anzawo sanakwanitse kupulumutsa anthu onse amene anakwiririka. Mwachitsanzo ku Léogâne, mzinda umene unawonongekanso kwambiri ndi chivomezichi, Roger ndi mwana wake wamwamuna wamkulu, Clid, anakwanitsa kuthawa pamene nyumba yawo imagwa. Koma mwana wake wamwamuna wamng’ono, Clarence, analephera kuthawa ndipo anafa. Mkazi wa Roger, Clana, anapsinjika mutu ndi denga koma ankathabe kulankhula. Mkaziyo ankafuula kuti, “Ndithandizeni mwamsanga, ndikufa! Ndikukanika kupuma!” Roger ndi mnzake anayesetsa kwambiri kuti amupulumutse koma analephera. Gulu lopulumutsa anthu linafika pamalopa patapita maola atatu, koma atamutulutsa, anapeza kuti wafa kale.
Lachitatu, January 13
Kunja kutacha m’pamene anthu anaona bwino mmene chivomezichi chinawonongera. Nyumba zambiri za mumzinda wa Port-au-Prince zinali zitagumukiratu. Nkhani ya chivomezichi itayamba kumveka,
mabungwe ndi anthu ena ongodzipereka padziko lonse lapansi anayamba kupita kuti akathandize. Anthu ogwira ntchito pa nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko la Dominican Republic, yomwe ili pa mtunda wa makilomita 300 kuchokera ku Haiti, anamva nthaka ikugwedezeka chifukwa cha chivomezichi. Iwo anauzidwa kuti chivomezichi chawononga kwambiri mumzinda wa Port-au-Prince. Mzindawu uli ndi anthu ambiri, moti pa anthu 9 miliyoni a ku Haiti, 3 miliyoni amakhala mumzinda umenewu. Choncho, Mboni za Yehova za ku Dominican Republic zinayamba kupita kuti zikathandize anthu okhudzidwa ndi chivomezichi.Panali patadutsa zaka 150 kuchokera pamene ku Haiti kunachitika chivomezi chachikulu. Choncho anthu a ku Haiti anali atasiya kumanga nyumba zoti sizingagwe ndi zivomezi, ngakhale kuti zinali zoti zingathe kulimbana ndi mphepo zamkuntho ndi madzi osefukira. Nyumba zambiri zinali za makoma ndi madenga olemera a konkire ndipo n’chifukwa chake zinagwa mosavuta kutachitika chivomezi chachikulu chimenechi. Chivomezichi chinali cha mphamvu zokwana 7.0. Koma nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Haiti, yomwe inamalizidwa mu 1987, inamangidwa moti singagwe wambawamba ndi chivomezi. Ngakhale kuti nthambiyi ili kum’mawa kwenikweni kwa mzinda wa Port-au-Prince, sinawonongeke ndi chivomezichi.
Chivomezichi chitangochitika, ntchito zosiyanasiyana zothandiza anthu zinakhazikitsidwa panthambi ya Mboni za Yehova ya ku Haiti. Popeza zinali zovuta kuimba foni kapena kutumiza mauthenga pa Intaneti kunja kwa dzikolo, anthu ogwira ntchito pa nthambiyi anapita kawiri konse pa galimoto kumalire a dzikoli ndi dziko la Dominican Republic kukatumiza uthenga wa momwe zinthu zilili. Pa nthawiyi, anthu ambirimbiri amene anakhudzidwa ndi chivomezichi anadzazana pa ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Haiti. Ena mwa iwo anali ovulala kwambiri. Anthu ambiri ankatengeredwa kuzipatala zomwe zinkagwirabe ntchito m’derali, koma popeza kuti zinalipo zochepa, sizinachedwe kudzaza.
M’zipatala zonsezi munali anthu ovulala atangogonagona pansi, akutuluka magazi komanso akungolira. Mmodzi wa anthuwa anali Marla, yemwe anapsinjidwa ndi nyumba ndipo anafukulidwa patapita maola 8. Iye anavulala kwambiri moti sankatha kusuntha miyendo yake ndipo sankamva chilichonse munthu akaikhudza. Anthu oyandikana nawo ndiwo anamufukula n’kumupititsa kuchipatala, koma bambo ake sanadziwe kuti apita naye kuchipatala chiti. Dokotala wina wa Mboni za Yehova amene anachokera ku Dominican Republic, dzina lake Evan, anamva za Marla ndipo anayamba kumufunafuna, ngakhale kuti ankangodziwa dzina lake lokha.
Apa n’kuti patapita maola oposa 24 chichitikireni chivomezichi, ndipo kunja kunali kutadanso. Evan atafika pachipatala china, anadutsa mitembo ya anthu pofunafuna Marla, ndipo ankapemphera chamumtima kwinaku akuitana Marla. Kenako anamva Marla akuyankha kuti, “Ndine!” Iye ankamwetulira uku akuyang’anitsitsa Evan. Evan anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa Marla kuti: “N’chifukwa chiyani ukumwetulira?” Iye anayankha kuti: “Chifukwa ndapezana ndi m’bale wanga wauzimu.” Evan anakhudzidwa kwambiri moti anagwetsa misozi.
Lachinayi, January 14
Likulu la Mboni za Yehova, lomwe lili ku United States, mogwirizana ndi nthambi ya ku Canada, Dominican Republic, France, Germany, Guadeloupe, Martinique, ndi nthambi zina, inayamba kuyendetsa ntchito yothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi chivomezichi. Zimenezi zinathandiza kuti agwiritse ntchito bwino katundu amene analipo, apeze njira yabwino yomunyamulira, apeze njira zabwino zolankhulirana, komanso agwiritse ntchito bwino ndalama ndi anthu amene anadzipereka kuthandiza. Anthu a Mboni za Yehova odziwa ntchito zachipatala okwana 78, ndi anthu enanso ambiri, ankapita ku Haiti kukathandiza. Pamene nthawi imakwana 2:30 m’bandakucha, galimoto yoyamba yonyamula katundu wothandizira anthu inanyamuka kunthambi ya Mboni za Yehova ya ku Dominican Republic kupita ku Haiti. Galimotoyi inanyamula chakudya, madzi, mankhwala ndi zinthu zina. Katunduyu anali wolemera makilogalamu 6,804.
Katunduyo atafika panthambi ya Mboni za Yehova ya ku Haiti m’mawa wa tsiku limenelo, anthu ogwira ntchito pa ofesiyi anayamba kukonza zoti zinthuzi zigawidwe. Pofuna kuti anthu asabe zinthuzi, iwo anazilongedza m’njira yoti munthu sangadziwe kuti muli chiyani. Anthuwa anagwira ntchitoyi usana ndi usiku. Iwo ankalongedza zakudya ndi zinthu zina m’mapaketi ang’onoang’ono oti akaperekedwe ku mabanja ndi kwa munthu mmodzimmodzi. M’miyezi yotsatira, Mboni za Yehova zinapereka kwaulere zinthu zoposa makilogalamu 450,000, kuphatikizapo mapaketi a zakudya oposa 400,000.
Lachisanu, January 15
Pamene nthawi inkakwana 12 koloko masana, madokotala, manesi ndi anthu ena ogwira ntchito zachipatala a Mboni za Yehova okwana 19 anafika ku Haiti kuchokera ku Dominican Republic ndi ku Guadeloupe. Posakhalitsa, iwo anakhazikitsa chipatala chaching’ono chothandizira anthu ovulala. Ena mwa anthu amene anathandizidwa pachipatalachi anali ana ambirimbiri amene ankakhala pamalo ena apafupi osungira ana amasiye. Mboni za Yehova zinaperekanso chakudya ndi matenti kumalo osungira ana amasiyewo. Mkulu woyang’anira malowo, dzina lake Étienne, anati: “Ndikuyamikira kwambiri Mboni za Yehova. Sindikudziwa kuti tikanatani iwo akanapanda kutithandiza.”
Anasowa Koma Kenako Anapezeka
Pa nthawi imene chivomezichi chinkachitika, mtsikana wina wa zaka 7, dzina lake Islande, atasuzumira pawindo anaona mapolo a magetsi akuthyoka ndiponso moto wa magetsi ukuthetheka. Kenako makoma a nyumba yawo anayamba kugwa, ndipo zidutswa zina zikuluzikulu zinamugwera. Iye anathyoka mwendo ndipo anavulala kwambiri. Anthu atamusolola, bambo ake, a Johnny, anapita naye kuchipatala m’dziko la Dominican Republic, m’malire ndi dziko la Haiti. Kuchokera kumeneku, Islande anatengedwa pa ndege kupita kuchipatala china kulikulu la dzikoli, ku Santo Domingo. Koma Johnny ataimbako foni, anapeza kuti Islande kulibe.
Kwa masiku awiri, Johnny anafufuza Islande kulikonse, koma sanamupeze, chifukwa anali atamupititsa kuchipatala china. Kumeneko, munthu wina wogwira ntchito mongodzipereka pachipatalapo anamumva akupemphera kwa Yehova. (Salimo 83:18) Munthuyo anamufunsa kuti: “Kodi umakonda Yehova?” Islande anayankha akulira kuti: “Inde.” Kenako munthuyo anamulimbitsa mtima pomuuza kuti: “Usadandaule. Yehova akuthandiza.”
Johnny anapempha nthambi ya ku Dominican Republic ya Mboni za Yehova kuti imuthandize kufufuza mwanayo. Mayi wina wa Mboni za Yehova, dzina lake Melanie, anadzipereka kuti amuthandiza. Atapita pachipatala china kukafufuza, munthu amene anamva
Islande akupemphera uja anamva Melanie akufunsafunsa ndipo anamulozera pomwe mwanayo anali. Pasanapite nthawi yaitali, Islande anakamupereka kwa makolo ake.Kuthandiza Anthu Ovulala
Anthu ambiri ovulala amene ankabwera pachipatala chimene Mboni za Yehova zinakhazikitsa panthambi ya ku Haiti anali oti sanalandire chithandizo chilichonse chivulalireni, kapena anangolandira chithandizo chochepa kwambiri, ndipo ziwalo zawo zinali zitayamba kuwonongeka. Choncho ambiri mwa iwo anangofunika kuwadula ziwalozo kuti akhale ndi moyo. Pa masiku oyambirira chivomezichi chitangochitika, zipangizo zopangira opaleshoni, mankhwala opha ululu pochita opaleshoni ndi mankhwala ena, zinali zochepa kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti ngakhale madokotalawo azimva chisoni kwambiri. Dokotala wina anati: “Ndinaona ndi kumva zinthu zambiri zoopsa zimene ndimalakalaka Mulungu atazifufuta m’maganizo mwanga.”
Patapita milungu iwiri chichitikireni chivomezicho, madokotala a Mboni za Yehova a ku Ulaya amene anali akatswiri a maopaleshoni ovuta kwambiri komanso ofunika kuchitidwa mwamsanga, anayamba kufika ndipo anabweretsanso zipangizo zofunika pochita maopaleshoni oterewa. Madokotalawa anachita maopaleshoni okwana 53 ndipo anaperekanso chithandizo china cha mankhwala kwa anthu ambirimbiri. Mtsikana wina wazaka 23, dzina lake Wideline, anafika mumzinda wa Port-au-Prince kutatsala tsiku limodzi kuti chivomezi chija chichitike. Iye anavulala kwambiri ndi chivomezichi moti dzanja lake lamanja linaphwanyika ndipo analidula kuchipatala. Kenako achibale ake anamutengera kuchipatala china chakufupi ndi kumudzi
kwawo ku Port-de-Paix, chomwe chinali pa mtunda woyenda maola 7 kuchokera ku Port-au-Prince. Koma matenda a Wideline ankangokulirakulira, ndipo madokotala a pachipatalacho anasiya kumupatsa chithandizo poganiza kuti sachira.Madokotala ena a Mboni za Yehova atamva za Wideline, anachoka ku Port-au-Prince kuti akamupatse chithandizo komanso kuti akamutenge n’kubwera naye kuti azidzamusamalirira pafupi. Odwala ena ataona kuti abale ake auzimu abwera kudzamutenga, anasangalala kwambiri ndipo anawombera m’manja. Anthu a m’banja la Wideline komanso a mumpingo wakwawo amuthandiza kwambiri.
Ku Dominican Republic, Mboni za Yehova zinapanga lendi nyumba zina n’cholinga choti azisamaliramo odwala amene anatumizidwa m’dzikoli. Madokotala, manesi, ndi anthu ena osamalira odwala, omwe anali a Mboni za Yehova, ankasinthana posamalira odwala m’nyumbazi. Iwo ankasamalira odwalawa mosangalala mpaka pomwe anayamba kupeza bwino.
Kulalikira Kunalimbitsa Chikhulupiriro, Chiyembekezo, ndi Chikondi
Pa Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova zokwana 56 zimene zili m’dera lomwe munachitika chivomezichi, 6 zokha n’zimene zinawonongeka kwambiri. Mboni za Yehova zambiri zimene nyumba zawo zinawonongeka zinayamba kukhala m’Nyumba za Ufumu zosawonongekazo, kapena m’malo ena panja. Mboni za Yehovazi zinazolowera kale kusonkhana pamodzi pa misonkhano yawo ikuluikulu, choncho zinkangokhala ngati zili pa msonkhano.
Munthu wina yemwe ndi mkulu mumpingo wina wa Mboni za Yehova m’deralo, dzina lake Jean-Claude, anati: “Tinapitirizabe kuchita zinthu zauzimu zimene timachita nthawi zonse pampingo pathu. Zimenezi zinathandiza kuti ana ndi akulu omwe asataye mtima kwambiri.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Munthu wina yemwe si wa Mboni anati: “Ndikusangalala kuona
inu Mboni za Yehova mukupitirizabe kulalikira. Tikanapanda kukuonani, bwenzi tikuganiza kuti zinthu zafika poipa kwambiri.”Mboni za Yehova zinkayesetsa kulimbikitsa anthu. Munthu wina wa Mboni za Yehova anati: “Pafupifupi aliyense amene tikukumana naye, akukhulupirira kuti chivomezichi ndi chilango chochokera kwa Mulungu. Koma ife tikuwatsimikizira kuti chivomezicho ndi tsoka lachilengedwe chabe osati chilango chochokera kwa Mulungu. Tikumawawerengera lemba la Genesis 18:25. Palembali, Abulahamu anasonyeza kuti n’zosatheka kuti Mulungu awononge anthu oipa pamodzi ndi abwino. Tikumawawerengeranso lemba la Luka 21:11. Palembali, Yesu ananena kuti masiku athu ano kudzachitika zivomezi zamphamvu, ndiponso tikuwauza kuti iye posachedwapa adzaukitsa akufa komanso kuthetsa mavuto onse. Anthu ambiri akuthokoza kwambiri tikamawauza zinthu ngati zimenezi.” *
Komabe mavuto adakalipo. Jean-Emmanuel, yemwe ndi dokotala komanso ndi wa Mboni za Yehova, anati: “Vuto loyamba linali chivomezi, koma chatsala n’chakuti tilimbane ndi mavuto omwe chivomezicho chatibweretsera. Kupatula pa matenda omwe amabwera chifukwa chakuti anthu ambiri akukhala malo osasamalika komanso onyowa, anthu ambiri akuvutikabe maganizo akaganizira zimene zinachitikazo. Iwo akuyesetsa kuti asasonyeze zimenezi koma sizikutheka.”
Patapita milungu ingapo kuchokera pamene chivomezichi chinachitika, munthu wina wa Mboni za Yehova anabwera pachipatala chimene a Mboni za Yehova anakhazikitsa, akudandaula kuti mutu wake wakhala ukupweteka ndipo sukusiya komanso akulephera kugona. Nthawi zambiri zimenezi zimachitikira anthu omwe akumana ndi tsoka. Nesi wina wa Mboni, anamufunsa kuti: “Kodi pali chinachake chinakumenyani m’mutu?” Iye anayankha molimba mtima kuti, “Ayi, palibe. Kungoti mkazi wanga yemwe ndakhala naye zaka 17 anafa ndi chivomezi. Koma tiyenera kuyembekezera zinthu zimenezi kuchitika chifukwa ndi zimene Yesu ananena.”
Nesiyo anazindikira kuti mwina mavutowo ayamba chifukwa chakuti munthuyo sakufuna kusonyeza kuti ali ndi chisoni. Choncho, anamuuza kuti: “N’zopweteka kuona mkazi wanu wokondedwa, amene mwakhala naye zaka zambiri, atamwalira. Zoterezi zikachitika ndi bwino kulira. Ngakhale Yesu analira mnzake Lazaro atamwalira.” Nesiyo atangonena zimenezo, munthuyo anayamba kulira kwambiri.
Kudera kumene kunachitikira chivomezichi kuli Mboni zopitirira 10,000, ndipo zimene zinafa zinalipo zokwana 154. Pafupifupi munthu aliyense wokhala mumzinda wa Port-au-Prince, wachibale wake kapena mnzake mmodzi kapena angapo anafa ndi chivomezichi. Mboni za Yehova zakhala zikuyendera mobwerezabwereza anthu amene ali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha imfa ya abale awo. Mbonizo zimapereka mpata kwa anthuwo kuti afotokoze mmene akumvera ndipo akafotokoza, Mbonizo zimalimbikitsa anthuwo. Ngakhale kuti a Mboni amene abale awo anafa amadziwa kale lonjezo la m’Baibulo lakuti akufa adzauka komanso lakuti kudzakhala dziko latsopano, ankafunikabe kufotokozera a Mboni anzawo mmene akumvera, n’cholinga choti awalimbikitse.
Kupirira Mavuto Panopa Komanso Kukhala ndi Chiyembekezo
Mtumwi Paulo analemba kuti: “Patsala zitatu izi: Chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.” (1 Akorinto 13:13) Zinthu zitatu zimenezi n’zimene zikuthandiza Mboni za Yehova za ku Haiti kuti zipirire mavuto awo panopa, kuti zikhale ndi chiyembekezo, komanso kuti zizilimbikitsa ena. Ntchito yomwe Mboni za Yehova zochokera m’mayiko osiyanasiyana zikugwira yothandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi chivomezichi ikuyenda bwino kwambiri chifukwa chakuti anthu amene akuigwira ali ndi chikhulupiriro chenicheni, amachita zinthu mogwirizana komanso ndi achikondi. Dokotala wa Mboni za Yehova, yemwe anabwera kudzathandiza kuchokera ku Germany, dzina lake Petra, anati: “Sindinaonepo anthu akusonyezana chikondi ngati chimenechi. Nthawi zambiri ndakhala ndikutulutsa misozi, osati chifukwa cha chisoni koma chifukwa cha chisangalalo.”
Nyuzipepala ina (The Wall Street Journal) inanena kuti chivomezi chomwe chinachitika ku Haiti m’chaka cha 2010 “mwina tingati chinali tsoka lachilengedwe lowononga kwambiri kuposa tsoka lililonse limene linachitikapo m’dziko limodzi.” Komabe, kuyambira pamene chivomezi cha ku Haiti chinachitika, padzikoli pachitikanso masoka ena oopsa kwambiri, ena achilengedwe ndipo ena oyambitsidwa ndi anthu. Kodi zinthu zimenezi zidzatha? Mboni za Yehova za ku Haiti komanso za padziko lonse sizikayikira kuti posachedwapa Mulungu adzakwaniritsa zimene analonjeza m’Baibulo kuti “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 31 Onani mutu 11 wakuti “N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?” m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 15]
“Sindikanatha kungomusiya Ralphendy akufa”
[Mawu Otsindika patsamba 19]
“Ndikusangalala kuona inu Mboni za Yehova mukupitirizabe kulalikira”
[Bokosi/Zithunzi patsamba 17]
KUMANGIRA NYUMBA ANTHU OSOWA POKHALA
Patapita mwezi umodzi kuchokera pamene chivomezichi chinachitika, akatswiri a zomangamanga a Mboni za Yehova anayamba kuyendera nyumba kuti aone zimene sizinawonongeke kwambiri zoti eni ake akhoza kubwereramo. Anthu ambiri amene nyumba zawo zinawonongeka ankafunika kupeza pokhala pongoyembekezera, podikirira kupeza nyumba ina.
John, amene amagwira ntchito pa ofesi ya Mboni za Yehova ku Haiti, anati: “Potengera luso la mabungwe amene amathandiza anthu padziko lonse pakagwa tsoka, tinamanga nyumba zosalira ndalama zambiri komanso zosavuta kumanga. Nyumbazi zinali zazikulu mofanana ndi nyumba zimene anthu ambiri amakhala chivomezicho chisanachitike. Nyumbazi zikuthandiza anthu kuti asavutike ndi mvula kapena mphepo, komanso ngati kutachitika chivomezi china, sizingawagwere.” Patangotha milungu itatu yokha chichitikireni chivomezicho, gulu la anthu ongodzipereka a ku Haiti komweko komanso ochokera m’mayiko ena anayamba kumanga nyumba zoti anthu azikhalamo mongoyembekezera.
Magalimoto onyamula mbali zina za nyumbazi, zimene anali atazipangiratu kale, akamadutsa m’misewu, anthu ankafuula mokondwera ndi kuwombera m’manja. Pamene ankapereka chilolezo choti katundu womangira nyumbazi alowe m’dziko la Haiti, munthu wina amene amagwira ntchito yoona zinthu zolowa ndi zotuluka m’dzikolo, anati: “A Mboni za Yehova anali m’gulu la anthu oyambirira amene anabwera m’dziko muno kudzathandiza anthu. Iwo samangonena zothandiza anthu, koma amathandizadi.” Pomatha miyezi yochepa chivomezichi chitachitika, Mboni za Yehova zinali zitamanga nyumba zokwana 1,500, kuti anthu amene nyumba zawo zinawonongeka azikhalamo.
[Mapu patsamba 14]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
HAITI
PORT-AU-PRINCE
Léogâne
Epicenter
Jacmel
DOMINICAN REPUBLIC
[Chithunzi patsamba 16]
Marla
[Chithunzi patsamba 16]
Islande
[Chithunzi patsamba 16]
Wideline
[Chithunzi patsamba 18]
Mboni za Yehova za ku Haiti zikupita kukalimbikitsa anthu amene anakhudzidwa ndi chivomezi
[Chithunzi patsamba 18]
Dokotala akuthandiza mwana wovulala pachipatala chokhazikitsidwa ndi Mboni za Yehova