Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Ngati Mumadwala Mutu Waching’alang’ala?

Kodi Mungatani Ngati Mumadwala Mutu Waching’alang’ala?

Kodi Mungatani Ngati Mumadwala Mutu Waching’alang’ala?

Joyce ndi mzimayi wansangala amene amagwira ntchito ya mu ofesi. Iye akuyang’anitsitsa chikalata chimene wanyamula. Mwadzidzidzi, akulephera kuona mbali zina za chikalatacho. Kenako akuyamba kuona timadontho towala tomwe tikukula n’kuyamba kuoneka ngati mizere yokhotakhota yowala ndiponso mabokosimabokosi ooneka mwachilendo. Pomatha mphindi zochepa, Joyce akuona movutikira kwambiri. Atazindikira chimene chikumuchitikira, Joyce akumwa m’bulu umodzi wa mankhwala amene amasunga kuti azimwa zoterezi zikachitika.

JOYCE amadwala mutu waching’alang’ala umene umasiyana ndi mutu wamba m’njira zingapo. Mwachitsanzo, mutu waching’alang’ala umagwira munthu pafupipafupi, pamene mutu wamba umagwira munthu mwa apa ndi apo. Komanso mutu waching’alang’ala ukagwira munthu, amadwala kwambiri ndipo amalephera kugwira ntchito.

Kodi zizindikiro zina za mutu waching’alang’ala n’zotani? Mutuwo ukamapweteka umakhala ngati ukupuma ndipo nthawi zina umawawa mbali imodzi yokha. Nthawi zina munthuyo amachita mseru ndipo amadana ndi kuwala kwambiri. Mutuwo ungathe kupweteka kwa maola angapo kapena masiku angapo.

Ngakhale kuti anthu ambiri amadwala mutu wamba nthawi ndi nthawi, ndi anthu ochepa amene amadwala mutu waching’alang’ala. Pa anthu 10 alionse amene amadwala mutu, ndi munthu mmodzi yekha amene mutuwo umakhala waching’alang’ala. Komanso akazi ndi amene amakonda kudwala mutu waching’alang’ala kuyerekeza ndi amuna. Anthu ena akayamba kudwala mutuwu amavutika kwambiri moti sakwanitsa kupita kuntchito. Nthawi zina zimenezi zimatha kubweretsa umphawi ndi mavuto ena pakhomo. N’chifukwa chake Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena kuti matenda a mutu waching’alang’ala ali pa nambala 20 pa matenda amene amasokoneza kwambiri moyo wa anthu padziko lonse.

Anthu ena akatsala pang’ono kuyamba kudwala mutu waching’alang’ala, manja awo amazizira, thupi lawo lonse limafooka, amamva njala, kapenanso amangoipidwa ndi chilichonse. Kenako, amachita chizungulire, amamva phokoso m’khutu, amamva kubayabaya pakhungu, amaona zinthu ziwiriziwiri, amalephera kulankhula, kapenanso thupi lawo limangoti zii.

Sizikudziwika bwinobwino kuti n’chiyani chimayambitsa matendawa, koma ena akuganiza kuti mwina amayamba chifukwa cha kusagwira bwino ntchito kwa mbali inayake ya ubongo imene imakhudzana ndi mitsempha ya m’mutu. Akuti mwina chimene chimachititsa kuti mutuwo ukamawawa uzikhala ngati ukupuma n’chifukwa chakuti magazi amakhala akudutsa m’mitsempha yotupa. Magazini ina ya zamankhwala inati: “Anthu amene amadwala mutu waching’alang’ala amatengera matendawa kwa makolo awo ndipo mbali inayake ya ubongo wawo sichedwa kusokonezedwa ndi zinthu zosiyanasiyana zimene zimachitika pa moyo wa munthu. Zinthu monga kusagona mokwanira, fungo lamphamvu kwambiri, kuyenda ulendo wautali, kusadya, kupanikizika kwambiri ndi ntchito, komanso kusintha kwa timadzi tinatake ta m’thupi, zikhoza kuchititsa kuti adwale mutuwu.” Anthu amene amadwala mutu waching’alang’ala akhozanso kudwala mosavuta matenda ena monga kupweteka kwa m’mimba, kuda nkhawa kwambiri, komanso kuvutika maganizo.

Mungachepetse Bwanji Vutoli?

Matenda otengera kwa makolo amakhala ovuta kuwathetsa. Komabe pali zimene mungachite kuti mutu waching’alang’ala usamakupwetekeni kawirikawiri. Anthu ena amalemba zinthu zimene zikuwachitikira tsiku ndi tsiku, ndipo mwanjira imeneyi amadziwa zakudya komanso zinthu zina zimene zimachititsa kuti mutu wawo uyambe kuwawa.

Anthu odwala matendawa amasiyanasiyana. Mwachitsanzo, Lorraine anazindikira kuti ankakonda kudwala mutu waching’alang’ala pa nthawi inayake pa mwezi. Iye anati: “Pakamatha milungu iwiri chisambireni, chinthu chilichonse chopitirira malire chimandidwalitsa mutu waching’alang’ala. Mwachitsanzo, ndikagwira ntchito kwambiri, kunja kukatentha kapena kukazizira kwambiri, pakakhala phokoso lambiri, ngakhalenso ndikadya zakudya zatsabola, ndimayamba kudwala mutuwu. Choncho pa nthawi imeneyi ndimayesetsa kuchita zinthu mosamala komanso mosapitirira malire.” Joyce, amene wakhala akudwala mutu waching’alang’ala kwa zaka zoposa 60, anati: “Ndinazindikira kuti ndikangodya malalanje, nanazi, kapena kumwa vinyo wofiira ndimayamba kudwala nthawi yomweyo, choncho ndinayamba kupewa zinthu zimenezi.”

Kudziwa chinthu chenicheni chimene chimachititsa kuti mutu uyambe kuwawa n’kovuta chifukwa nthawi zambiri pamakhala zinthu zingapo zimene zimayambitsa. Mwachitsanzo, pa nthawi ina mukhoza kudya chokoleti osadwala, koma pa nthawi ina chokoleti chomwecho chikhoza kukudwalitsani, mwina chifukwa chakuti pali chinthu chinanso chimene chinachitika.

Ngakhale ngati simungathe kudziwa kapena kupewa zinthu zimene zimachititsa kuti mutu uyambe kukupwetekani, pali njira zina zimene zingakuthandizeni kuti musamadwale pafupipafupi. Akatswiri a matendawa amati ndi bwino kusasinthasintha nthawi imene mumagona ndi kudzuka tsiku lililonse. Ngati mukufuna kugona kwa nthawi yaitali Loweruka kapena Lamlungu, ndi bwino kudzuka pa nthawi imene mumadzuka tsiku lililonse, n’kuchita zinthu zinazake kwa mphindi zochepa, kenako n’kukagonanso. Kumwa khofi, tiyi kapena cocacola wambiri kungayambitse matendawa, choncho musamamwe khofi kapena tiyi wopitirira makapu awiri pa tsiku, kapena cocacola wosapitirira mabotolo awiri pa tsiku. Nthawi ya chakudya ikakwana, muzidya, chifukwa njala imachititsa kuti mutu uyambe kuwawa. Mutu waching’alang’ala umayambanso chifukwa cha nkhawa. Ngakhale kuti n’zosatheka kupeweratu nkhawa, muziyesetsa kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kuichepetsa, monga kusintha ndandanda yanu, kuwerenga Baibulo kapena kumvetsera nyimbo zabwino zapansipansi.

Kodi Pali Mankhwala a Mutu Waching’alang’ala?

Pali zinthu zambiri zimene anthu odwala matendawa angachite. * Mwachitsanzo, kugona mokwanira kumathandiza kwambiri. Palinso mankhwala opha ululu amene munthu angamwe n’kuyamba kumva bwino.

M’chaka cha 1993, kunabwera mankhwala atsopano a mutu waching’alang’ala otchedwa triptan. Pofotokoza za mankhwalawa, magazini ina ya zachipatala inanena kuti “mankhwalawa ndi umboni wakuti chithandizo cha anthu odwala mutu waching’alang’ala chapita patsogolo kwambiri.” Inanenanso kuti “kubwera kwa mankhwala a triptan . . . kwathandiza kwambiri anthu odwala mutu waching’alang’ala ngati mmene kubwera kwa mankhwala a penisilini kunathandizira anthu odwala matenda oyambitsidwa ndi bakiteriya.”—The Medical Journal of Australia.

Mutu waching’alang’ala si matenda akupha. Koma mankhwala ake, mosiyana ndi mankhwala a matenda oyamba chifukwa cha bakiteriya, sachiziratu. Komabe, mankhwalawa athandiza kwambiri anthu ena omwe akhala akuvutika ndi mutu waching’alang’ala. Anthu odwala mutu waching’alang’ala amafunikabe kugona mokwanira ndi kuchita zinthu zina zimene tafotokoza kale zija. Ngakhale zili choncho, anthu ena odwala matendawa anena kuti moyo wawo wasintha kwambiri chifukwa cha mankhwalawa.

Koma mankhwala alionse amakhala ndi ubwino komanso kuipa kwake. Kodi kuipa kwa mankhwala a triptan n’kotani? Choyamba, mankhwalawa ndi odula kwambiri, choncho amangoperekedwa kwa anthu amene mutu waching’alang’ala umawavutitsa kwambiri. Chinanso, mankhwalawa sathandiza munthu aliyense, ndipo anthu ena sangamwe mankhwalawa chifukwa cha matenda ena amene ali nawo. Panopa palibe mankhwala ochiritsira mutu waching’alang’ala, womwe munthu amachita kutengera kwa makolo ake. Komabe, magazini ina ya zachipatala inati: “Chifukwa cha mankhwala a mutu waching’alang’ala amene alipo masiku ano, palibe chifukwa choti anthu odwala matendawa azivutika nawo kwambiri.”—Emergency Medicine.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Magazini ya Galamukani! silimbikitsa anthu kusankha mtundu winawake wa mankhwala. Munthu aliyense ayenera kuganizira bwinobwino ubwino ndiponso kuipa kwa mankhwalawo asanayambe kuwagwiritsira ntchito.

[Chithunzi patsamba 23]

Ena amalemba zimene zikuchitika pa moyo wawo tsiku lililonse ndipo zimenezi zimawathandiza kudziwa zakudya kapena zinthu zina zimene zimachititsa kuti mutu uyambe kuwapweteka

[Chithunzi patsamba 23]

Kumvetsera nyimbo zabwino zapansipansi kungachepetseko nkhawa, imene nthawi zambiri imayambitsa mutu waching’alang’ala

[Chithunzi patsamba 23]

Munthu amatengera matenda a mutu waching’alang’ala kwa makolo ake. Matendawa ndi ovutitsa kwambiri komabe nthawi zambiri madokotala amathandiza