Nyumba za Mbalame za ku Istanbul
Nyumba za Mbalame za ku Istanbul
● Nyumba zamatabwa za mbalame zimapezeka m’madera ambiri padziko lapansi. Nyumbazi ndi malo abwino kwambiri amene mbalame zimadyera, zimakhala zikazizidwa, zimamangapo zisa, kulererapo ana, ndi kubisalapo poopa adani, mvula, mphepo ndi zinthu zina. Mumzinda wa Istanbul, anthu amamanga nyumba za mbalame zooneka ngati nyumba zenizeni. Zina zimaoneka ngati nyumba zikuluzikulu za anthu olemera, zina ngati mizikiti, kapenanso ngati nyumba zachifumu. * Nyumbazi zimadziwika ndi mayina osiyanasiyana.
Nyumba za mbalame zakale kwambiri zinamangidwa cha m’ma 1400, ndipo zinali zokongoletsedwa kwambiri potengera mmene anthu ankamangira nyumba nthawi imeneyo. Pa nthawiyi zinkakhala zing’onozing’ono, koma kuyambira m’zaka za m’ma 1700, anayamba kumanga nyumba zikuluzikulu zokongola kwambiri. Nyumba zina zinkakhala ndi malo oikapo zakudya ndi madzi akumwa, tinjira toyendamo, ndiponso makonde oti mbalamezo zizikhalapo n’kumaona zomwe zikuchitika kunja. Nyumba za mbalamezi ankazimanga kumbali ya nyumba kumene kumafika dzuwa lambiri komanso kumene mphepo siwomba kwambiri. Ankazimanganso patali poti amphaka, agalu komanso anthu sangafikire. Nthawi zina nyumba za mbalamezi ankazimanga mwanjira imeneyi osati n’cholinga chongofuna kuthandiza mbalamezo komanso pofuna kukongoletsa nyumba zimene amangapo nyumba za mbalamezo. Masiku ano mutha kuona nyumba za mbalame pamizikiti ikuluikulu ndi ing’onoing’ono, pamipope ya madzi akumwa, pamalaibulale, pamilatho, ndiponso panyumba za anthu.
Koma n’zomvetsa chisoni kuti zambiri mwa nyumba za mbalamezo zinawonongeka ndi mvula komanso mphepo, ndipo zina zinawonongedwa dala ndi anthu amene sankadziwa kufunika kwake. Choncho nyumbazi zikusowa masiku ano. Ngati mutadzapita ku Istanbul tsiku lina ndipo mumakonda nyumba zakale, mudzayesetse kuyang’anayang’ana m’munsi mwa madenga a nyumba zakale kuti muone nyumba za mbalame zokongolazi. Popeza tsopano mwazidziwa nyumbazi, mukadzaziona mudzasangalala kwambiri.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Ngakhale kuti nyumbazi zimaoneka ngati zenizeni, sizifanana ndendende ndi nyumba zenizeni zimene zilipodi.