Buku Limene Mungathe Kulikhulupirira—Gawo 6
Buku Limene Mungathe Kulikhulupirira—Gawo 6
Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Ufumu wa Roma
Ino ndi nkhani ya nambala 6 pa nkhani 7 zotsatizana zimene zikulembedwa m’magazini a “Galamukani!” Nkhanizi zikufotokoza za maufumu 7 otchulidwa m’Baibulo amene analamulirapo dziko lonse. Cholinga cha nkhanizi n’kusonyeza kuti Baibulo ndi lodalirika komanso kuti linauziridwa ndi Mulungu. Cholinga chinanso ndi kusonyeza kuti uthenga wa m’Baibulo umatipatsa chiyembekezo chakuti mavuto onse amene ulamuliro wa anthu wabweretsa, adzatha.
YESU ndi amene anayambitsa Chikhristu, ndipo otsatira ake ndi amene anachifalitsa m’madera ena akutali pa nthawi ya ufumu wa Roma. Ngakhale masiku ano, misewu, ngalande komanso zipilala zimene Aroma anamanga zimapezekabe m’mayiko monga Britain ndi Egypt. Zinthu zimenezi zimasonyeza kuti ufumu wa Roma unakhalapodi. Komanso zimatitsimikizira kuti Yesu ndi atumwi ake anakhalapodi ndiponso kuti nkhani zokhudza zimene anachita komanso kunena n’zenizeni. Mwachitsanzo, ngati mukuyenda mumsewu wa Apiyo umene Aroma anamanga, ndiye kuti mukuyenda mumsewu umene Paulo anadutsa mwina pa ulendo wake wopita ku Roma.—Machitidwe 28:15, 16.
Mbiri Yodalirika
Zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Yesu ndi ophunzira ake, zimaphatikizapo zinthu zambiri zodziwika bwino zimene zinachitika pakati pa chaka cha 1 C.E. ndi 100 C. E. Pa nthawi imeneyi n’kuti ufumu wa Roma ukulamulira. Mutawerenga buku la m’Baibulo la Luka mukhoza kuona kuti analemba zinthu ziwiri zofunika kwambiri zimene zinachitika pa nthawiyo. Zinthu zake ndi utumiki wa Yohane M’batizi komanso kubatizidwa kwa Yesu, komwe kunam’chititsa kuti akhale Khristu kapena kuti Mesiya. Luka analemba kuti zinthu zimenezi zinachitika “m’chaka cha 15 cha ulamuliro wa Kaisara Tiberiyo [29 C.E.].” Analembanso kuti pa nthawiyi “Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya. Herode anali wolamulira chigawo cha Galileya.” (Luka 3:1-3, 21) Luka anatchulanso akuluakulu a boma anayi awa: Filipi (mchimwene wake wa Herode), Lusaniyo, Anasi, ndi Kayafa. Akatswiri a mbiri yakale amanenanso kuti anthu 7 onsewa anakhalapodi. Koma m’nkhaniyi tingokambirana za Tiberiyo, Pilato ndi Herode.
Kaisara Tiberiyo ndi wodziwika kwambiri ndipo pali zithunzi zambiri zojambulidwa mwaluso zimene zimasonyeza mmene ankaonekera. Nyumba ya Malamulo ya ku Roma inamusankha kuti akhale mfumu pa September 15 m’chaka cha 14 C.E., pamene Yesu anali ndi zaka 15.
Pontiyo Pilato. Dzina lake limapezeka pamodzi ndi dzina la Tiberiyo m’nkhani inayake imene inalembedwa pa nthawi imene Baibulo linali litangomalizidwa kulembedwa. Nkhaniyi inalembedwa ndi Tasitasi, yemwe anali katswiri wa mbiri yakale wa ku Roma. Pofotokoza za mawu akuti “Mkhristu,” Tasitasi analemba kuti mawuwa “anachokera ku mawu akuti Khristu. Khristuyo anazunzidwa mpaka imfa pa nthawi ya ulamuliro wa Tiberiyo, movomerezedwa ndi Pontiyo Pilato, mmodzi wa mabwanamkubwa athu.”
Herode Antipa amadziwika kuti ndi amene anamanga mzinda wa Tiberiya, m’mphepete mwa nyanja ya Galileya. Iye ankakhalanso mumzinda umenewu ndipo zikuoneka kuti kumeneku n’kumene Herode analamulira kuti Yohane M’batizi adulidwe mutu.
Baibulo limafotokozanso nkhani zina zikuluzikulu zimene zinachitika pa nthawi ya ufumu wa Roma. Ponena za nthawi imene Yesu anabadwa, Baibulo limati: “Tsopano m’masiku amenewo, Kaisara Augusito analamula kuti anthu onse m’dzikolo akalembetse m’kaundula. Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya. Anthu onse anapita kukalembetsa, aliyense kumzinda wakwawo.”—Luka 2:1-3.
Tasitasi ndiponso katswiri wa mbiri ya Chiyuda, Josephus, amatchulanso za Kureniyo. Umboni wakuti kunkakhala kalembera wotereyu umapezeka m’buku linalake limene lili ku malo osungira mabuku a British Library. M’bukuli muli lamulo la bwanamkubwa wa ku Roma, limene limati: “Popeza kuti nthawi yochita kalembera nyumba iliyonse yakwana, m’pofunika kuti tilamule anthu onse amene pa zifukwa zosiyanasiyana sakukhala m’maboma akwawo kuti abwerere kwawo.”
Baibulo limanenanso za “njala yaikulu” imene inachitika “m’nthawi ya [mfumu ya Roma] Kalaudiyo.” (Machitidwe 11:28) Josephus analembanso zinthu zogwirizana ndi zimenezi. Iye anati: “Njala inavuta kwambiri pa nthawi imeneyo ndipo anthu ambiri anafa.”
Komanso, pa Machitidwe 18:2, Baibulo limanena kuti ‘Kalaudiyo analamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma.’ Zimenezi zimagwirizana ndi nkhani yonena za Kalaudiyo imene inalembedwa cha mu 121 C.E. ndi katswiri wa mbiri yakale, dzina lake Suetonius. Iye analemba kuti Kalaudiyo “anathamangitsa Ayuda onse ku Roma.” Analembanso kuti chifukwa chakuti Ayuda ankadana ndi Akhristu “nthawi zonse ankayambitsa zisokonezo.”
Baibulo limafotokoza kuti cha pa nthawi ya njala imene taitchula ija, Herode Agiripa, atavala “zovala zake zachifumu,” analankhula pamaso pa gulu la anthu, omwe ankamugomera kwambiri, n’kumati: “Amenewa ndi mawu a mulungu, osati a munthu ayi!” Kenako Baibulo limanena kuti, Agiripa “anadyedwa ndi mphutsi n’kumwalira.” (Machitidwe 12:21-23) Josephus anafotokozanso za nkhani imeneyo ndipo anawonjezerapo zinthu zina. Iye analemba kuti pa nthawi imene Agiripa ankalankhula, “anavala zovala zopangidwa ndi siliva yekhayekha.” Ananenanso kuti Agiripa ‘anayamba kumva kupweteka m’mimba kwambiri, ndipo zimenezi zinayamba mwamphamvu kwambiri.’ Josephus ananena kuti Agiripa anamwalira patapita masiku asanu.
Ulosi Wodalirika
M’Baibulo mulinso maulosi ofunika kwambiri amene analembedwa ndi kukwaniritsidwa pa nthawi ya ufumu wa Roma. Mwachitsanzo, pamene Yesu ankalowa mu Yerusalemu, analirira mzindawo ndipo analosera kuti asilikali a Roma adzauwononga. Iye ananena kuti: “Masiku adzakufikira pamene adani ako adzamanga mpanda wazisonga kukuzungulira. . . . Ndipo sadzasiya mwala pamwala unzake mwa iwe, chifukwa sunazindikire kuti nthawi yokuyendera inali itakwana.”—Luka 19:41-44.
Koma Yesu anasonyeza kuti otsatira ake adzakhala ndi mpata wothawa. Kodi iwo akanadzathawa bwanji? Yesu anawapatsa malangizo atsatanetsatane nthawi idakalipo. Iye anawachenjeza kuti: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu, mudzadziwe kuti chiwonongeko chake chayandikira. Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo [Yerusalemu] adzatulukemo.” (Luka 21:20, 21) Mwina otsatira a Yesu ankadzifunsanso kuti, ‘Tidzatha bwanji kuthawa mumzinda woti wazunguliridwa ndi adani?’
Josephus analemba zimene zinachitika pa nthawi imeneyo. Mu 66 C.E., bwanamkubwa wa Roma analowa m’chipinda chosungira chuma cha pakachisi n’kutengamo ndalama, chifukwa Ayuda anali ndi ngongole kwa Aroma ya msonkho. Ayuda ena anakwiya nazo kwambiri zimenezi ndipo anapha asilikali a Aroma, ndipo sankamveranso ulamuliro wa Aroma. Kenako m’chaka chomwecho, Seshasi Galasi, yemwe anali bwanamkubwa wa Aroma ku Siriya, analowera kum’mwera ndi asilikali okwana 30,000 n’kukafika ku Yerusalemu, pa nthawi ya chikondwerero chinachake chachipembedzo. Galasi ndi asilikali ake analowa m’midzi ya ku Yerusalemu ndipo kenako anayamba kugumula mpanda wa kachisi, kumene Ayuda oukira aja ankabisala. Kenako, pa chifukwa chosadziwika bwino, Galasi ndi asilikali ake anabwerera. Poona zimenezi, Ayuda ena anasangalala kwambiri ndipo anawatsatira asilikaliwo n’kukamenyana nawo.
Akhristu okhulupirika sanapusitsidwe ndi kubwerera kwa asilikaliwo. Iwo anazindikira kuti ulosi wochititsa chidwi umene Yesu ananena, wakuti mzinda wa Yerusalemu udzazunguliridwa ndi asilikali, wakwaniritsidwa. Tsopano popeza kuti asilikaliwo anali atabwerera, Akhristuwo anaona kuti ndi mpata wawo woti athawe mumzindawo. Ambiri anathawira ku Pela, mzinda womwe unali kumapiri a kutsidya lina la Yorodano. Mumzindawu munkakhala anthu omwe sanali Ayuda, amene sankakhudzidwa ndi mkangano wa pakati pa Ayuda ndi Aroma.
Kodi kenako mzinda wa Yerusalemu unakumana ndi zotani? Asilikali a Roma anabwereranso ndipo pa nthawiyi ankatsogoleredwa ndi Vasipashani ndi mwana wake Tito. Iwo anali ndi asilikali okwana 60,000. Asilikaliwo analowa mumzindawo chikondwerero cha Pasika cha mu 70 C.E. chitatsala pang’ono kuyamba, ndipo anatsekereza anthu okhala mumzindawo komanso alendo amene anabwera kudzachita nawo chikondwererochi. Asilikali a Roma anagwetsa mitengo yambiri mumzindawo n’kumanga mpanda wazisonga, monga mmene Yesu ananenera. Patadutsa miyezi pafupifupi isanu, Aroma anagonjetsa mzindawo.
Tito analamula kuti kachisi asagwetsedwe koma msilikali wina anatentha kachisiyo ndipo kenako kachisiyo anagwetsedwa yense, osasiya ngakhale mwala umodzi pa unzake. Zimenezi zinakwaniritsa ndendende zimene Yesu ananena. Malinga ndi zimene Josephus ananena, anthu okwana 1,100,000, omwe anali Ayuda ndi anthu otembenukira ku Chiyuda, anafa. Ambiri a iwo anafa chifukwa cha njala ndi miliri. Ena okwana 97,000 anagwidwa ukapolo. Ambiri anatumizidwa ku Roma kuti akakhale
akapolo kumeneko. Ngati mutapita ku Roma panopa, mukhoza kukaona chinyumba chotchuka kwambiri chotchedwa Colosseum, chomwe kalelo ankachitiramo masewera osiyanasiyana. Chinyumbachi chinamalizidwa kumangidwa ndi Tito. Mukhozanso kukaona chipilala cha Tito, chomwe chinamangidwa pokumbukira kugonjetsedwa kwa mzinda wa Yerusalemu. Zimenezi zikusonyeza kuti ulosi wa m’Baibulo ndi wodalirika kwambiri. Choncho tiyenera kulabadira zimene Baibulo limalosera kuti zidzachitika m’tsogolo.Chiyembekezo Chodalirika
Yesu atakaonekera pamaso pa bwanamkubwa Pontiyo Pilato, anafotokoza za boma, kapena kuti Ufumu, umene “si wochokera pansi pano.” (Yohane 18:36) Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipempherera boma labwino kwambiri limeneli. Iye anati: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Onani kuti Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti chifuniro cha Mulungu, osati cha anthu onyada ndi ongofuna kulamulira anzawo, chichitike padziko lapansi.
Yesu ndiye wolamulira wa Ufumu wakumwamba umenewu. Ndipo mogwirizana ndi cholinga choyambirira cha Mulungu, Yesu adzachititsa kuti dziko lapansi likhale paradaiso.—Luka 23:43.
Kodi ndi liti pamene Ufumu wa Mulungu udzayambe kulamulira padziko lapansi? Yesu ataukitsidwa n’kupita kumwamba, anasonyeza nthawi imene zimenezi zidzachitike pamene analankhula ndi mtumwi Yohane, yemwe pa nthawiyo anali atamangidwa pa chilumba cha Patimo. Iye anamangidwa pa nthawi imene Domitian, mchimwene wake wa Tito, anali mfumu ya Roma. Yesu anati: “Palinso mafumu 7. Asanu agwa, imodzi ilipo, inayo sinafikebe. Koma ikafika, ikufunika kudzakhala kanthawi kochepa.”—Chivumbulutso 17:10.
Pa nthawi imene Yohane ankalemba mawu amenewa, n’kuti “mafumu” kapena kuti maufumu asanu atagwa. Maufumuwa anali: Ufumu wa Iguputo, Asuri, Babulo, Mediya ndi Perisiya, ndi ufumu wa Girisi. Ufumu umene ‘unalipo’ pa nthawi imene mtumwi Yohane ankalemba zimenezi, unali wa Roma. Zimenezi zikusonyeza kuti panali patatsala ufumu umodzi: Ufumu umene Baibulo limanena kuti udzakhala womaliza kulamulira dziko lonse lapansi. Kodi ufumu umenewu ndi uti? Kodi udzalamulira kwa nthawi yaitali bwanji? Mafunso amenewa adzayankhidwa mu Galamukani! yotsatira.
[Chithunzi patsamba 10]
Paulo anayendapo mumsewu wa Apiyo umenewu
[Chithunzi patsamba 10]
Kaisara Tiberiyo ndi mmodzi mwa akuluakulu a boma la Roma amene anatchulidwa mu Uthenga Wabwino wa Luka
[Chithunzi patsamba 11]
Mwala umene analembapo dzina la Pontiyo Pilato
[Chithunzi pamasamba 12, 13]
Dzina la Tito, mwana wa Vasipashani, linalembedwa pa ndalama iyi
[Mawu a Chithunzi]
Musée de Normandie, Caen, France
[Chithunzi patsamba 13]
Chipilala cha Tito ku Rome chinamangidwa pokumbukira kugonjetsedwa kwa mzinda wa Yerusalemu mu 70 C.E.
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
Top, time line: Egyptian wall relief and bust of Nero: Photograph taken by courtesy of the British Museum; Persian wall relief: Musée du Louvre, Paris; bottom, bust of Tiberius Caesar: Photograph taken by courtesy of the British Museum