Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
“Anthu oposa theka la anthu onse a ku Russia amaganiza kuti munthu afunika kupereka ziphuphu kwa anthu audindo kuti zinthu zimuyendere bwino.’”—REUTERS NEWS SERVICE, RUSSIA.
“Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu pafupifupi 18 pa 100 aliwonse achikulire ku China, akudwala matenda osokonekera maganizo . . . Akazi ndi amene amavutika kwambiri ndi matenda a maganizo kuposa amuna.”—CHINA DAILY, CHINA.
“Malinga ndi lipoti lotulutsidwa ndi bungwe loona zopewa ngozi za pamsewu, ngozi zoposa 28 pa ngozi 100 zilizonse (zomwe ndi ngozi 1.6 miliyoni pa chaka) zimene zimachitika ku U. S. A., zimachitika chifukwa chakuti oyendetsawo amalankhula pa foni kapena kutumiza ndi kuwerenga mauthenga pa foni.”—UC BERKELEY WELLNESS LETTER, U.S.A.
“Mbiri Yochititsa Manyazi”
Nyuzipepala ya Irish Times, inati: “Lipoti lofufuza nkhani yochitira nkhanza ana lasonyeza kuti tchalitchi cha Katolika ku Ireland chili ndi “mbiri yochititsa manyazi.” Malinga ndi zimene nyuzipepalayi inanena, lipoti limeneli likusonyeza kuti tchalitchichi chili ndi mbiri yoipa, kuyambira pa “kumenya ana omwe apezeka ndi nsabwe,” mpaka pa kuchita nawo zachiwerewere. Nyuzipepalayi inanena kuti, milanduyi yakhala ikunyalanyazidwa chifukwa chokhulupirira kuti “tchalitchi cha Katolika chili ndi mphamvu zopanda malire,” ndipo ayenera kumangochigonjera pa chilichonse. Pogwira mawu a munthu wina amene ankamvera chisoni anthu ochitidwa nkhanzawo, nyuzipepala ya Times ija inali ndi mutu wakuti: “Aboma ndi Atchalitchi, Chitani Manyazi.”
Asayansi Apeza Madzi Pamwezi
Asayansi anatumiza chombo chokhala ndi mainjini awiri kuti chikamenye pamwezi, n’cholinga choti aone ngati fumbi limene lingatuluke pamweziwo lili ndi madzi. Iwo anaunika fumbilo ndi zipangizo zawo zimene zimathandiza kuti aone mmene zinthu zapangidwira. Michael Wargo, yemwe ndi mkulu wa dipatimenti yoona za mwezi kulikulu la bungwe la NASA, ku Washington, D.C., anati: “Cholinga chathu ndi kuphunzira zinthu zambiri zatsopano zokhudza mwezi komanso mapulaneti ena amene atiyandikira.” Chaposachedwapa, makina ounikira a setilaiti asonyeza kuti kumpoto kwa mwezi kuli madzi ambirimbiri.
Anthu Akumagula Golide pa Makina
M’madera ambiri padzikoli, golide wayamba kupezeka m’gulu la malonda ogulitsidwa pa makina ogulitsira zinthu. Mwachitsanzo, hotela ina ya ku Abu Dhabi, m’dziko la United Arab Emirates, yayamba kugwiritsa ntchito makina amene amagulitsa okha zinthu zosiyanasiyana zokwana 320. Zina mwa zinthuzi ndi golide wolemera magalamu 10 komanso ndalama zagolide zopangidwa mwapadera. Mitengo ya golideyu imasintha pa mphindi 10 zilizonse, potengera mmene mtengo wa golide ulili pa msika wapadziko lonse. Poyamba makinawa ankangolola ndalama za m’dzikolo basi, koma panopa anthu amatha kugula golide pogwiritsa ntchito makadi otengera ndalama. Nkhani ina imene inatulutsidwa ndi bungwe lofalitsa nkhani la Reuters, inanena kuti anthu anaganiza zoika makinawa ku Abu Dhabi “chifukwa chakuti kuli anthu ambiri amene amafuna kugula golide.”