Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusamala ndi Zimene Timalankhula?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusamala ndi Zimene Timalankhula?

Zimene Baibulo Limanena

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusamala ndi Zimene Timalankhula?

Nduna yaikulu ya dziko linalake inali itangomaliza kumene kukambirana mwaulemu ndi mayi winawake wachikulire. Kenako atangosiyana, ndunayo inauza antchito ake kuti mayiyo ndi wotopetsa ndipo inawakalipira chifukwa cholola mayiyo kukumana naye. Pa nthawi imene imanena zimenezi, ndunayo sinkadziwa kuti ikumveka pa maikolofoni. Kenako anthu atamva zimene ndunayo inanena anakhumudwa kwambiri. Mbiri yake inaipa ndipo analephera chisankho chimene chinachitika patapita masiku 8 kuchokera tsiku limeneli.

PALIBE munthu amene angathe kulamulira lilime lake nthawi zonse. (Yakobo 3:2) Komabe, nkhani imene tafotokoza pamwambapa ikusonyeza kuti tiyenera kusamala kwambiri ndi zimene timalankhula. Ngati timangolankhula mwachisawawa, tikhoza kuwononga mbiri yathu, kuchotsedwa ntchito komanso kuwononga ubale wathu ndi anthu ena.

Koma si zokhazo. Baibulo limanena kuti zimene timalankhula zimavumbula zimene zili mumtima mwathu. Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.” (Mateyu 12:34) Popeza kuti zimene timalankhula zimasonyeza mmene tikumvera, maganizo athu, komanso umunthu wathu, ndi bwino kuti tiziganizira bwinobwino zimene tikufuna kulankhula. Baibulo lingatithandize kwambiri pa nkhani imeneyi.

Zimene Mungachite Kuti Muzilankhula Zinthu Zabwino

Tisanalankhule timayamba taganiza kaye. Choncho kuti tizilankhula zinthu zabwino, tiyenera kuganiziranso zinthu zabwino. Mawu a Mulungu angatithandize kuti tiziganiza zinthu zabwino, zimene zingachititse kuti tizilankhulanso zinthu zabwino.

Muziganizira zinthu zabwino zokhazokha. Baibulo limatiuza zinthu zabwino zofunika kuziganizira. Limati: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”Afilipi 4:8.

Kuganizira zinthu zabwino zimenezi kungakuthandizeni kuti musamangolankhula chilichonse. Kumbukirani kuti zimene mumaona ndi kuwerenga n’zimene mumakonda kuziganiza. Choncho, kuti musamaganize zinthu zosayenera, muyenera kupewa kuwerenga kapena kuonera zinthu zoipa. Zimenezi zikuphatikizapo zinthu zachiwawa komanso zotukwana. (Salimo 11:5; Aefeso 5:3, 4) M’malomwake muziganizira zinthu zoyera ndi zabwino. Baibulo lingakuthandizeni kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, werengani Miyambo 4:20-27; Aefeso 4:20-32; ndi Yakobo 3:2-12. Onani mmene mfundo za m’malemba amenewa zingakuthandizireni kuti muzilankhula zinthu zabwino. *

Muziganiza kaye musanalankhule. Lemba la Miyambo 12:18 limati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.” Ngati nthawi zambiri mumaona kuti mumalankhula “mawu olasa,” mungachite bwino kuti muziyesetsa kuyamba mwaganiza kaye musanalankhule. Yesetsani kutsatira malangizo abwino kwambiri opezeka pa Miyambo 15:28 omwe amati: “Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe, koma pakamwa pa anthu oipa pamasefukira zoipa.”

Khalani ndi cholinga. Yesetsani kuti mwezi umene ukubwerawo, musalankhule chilichonse chimene changobwera m’maganizo mwanu, makamaka pamene wina wakuputani. M’malomwake tsatirani malemba amene ali mu nkhani ino, ndipo yesetsani kulankhula zinthu zanzeru komanso zachikondi modekha. (Miyambo 15:1-4, 23) Koma pali zinanso zimene mungafunikire kuchita.

Muzipemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni. Munthu wina amene analemba nawo Baibulo anapemphera kuti: “Mawu a pakamwa panga ndi kusinkhasinkha kwa mtima wanga, zikukondweretseni, inu Yehova.” (Salimo 19:14) Muuzeni Yehova Mulungu kuti mukufuna kuti muzilankhula zinthu zomukondweretsa komanso zokondweretsa anthu ena. Lemba la Miyambo 18:21 limati: “Imfa ndiponso moyo zili mu mphamvu ya lilime, ndipo wolikonda adzadya zipatso zake.”

Mawu a Mulungu azikhala ngati galasi lanu. Baibulo lili ngati galasi limene lingakuthandizeni kudziwa mmene mukuonekera. (Yakobo 1:23-25) Mwachitsanzo, mukamaganizira malemba atatu otsatirawa, dzifunseni kuti, ‘Kodi nthawi zambiri ndimalankhula zinthu zotani?’

“Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Kodi mumalankhula modekha? Kodi mumapewa kulankhula mokalipa?

“Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikire, kuti asangalatse owamva.” (Aefeso 4:29) Kodi zimene mumalankhula zimakhala zolimbikitsa?

“Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.” (Akolose 4:6) Ngakhale zinthu zitavuta, kodi mumayesetsa kunena zinthu mokoma mtima n’cholinga choti musakhumudwitse ena?

Mukadziyang’ana pa galasi mumatha kukonza zina ndi zina pa nkhope panu. Mukatero mumaoneka bwino ndipo simuchita manyazi mukakhala pagulu. N’chimodzimodzinso ndi Baibulo. Limakuthandizani kulankhula zinthu zabwino zokhazokha zimene mungapindule nazo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Ngati mumagwiritsa ntchito Intaneti, mukhoza kuwerenga Baibulo pa adiresi iyi: www.dan124.com.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi zolankhula zanu zimasonyeza chiyani?—Luka 6:45.

● Kodi muyenera kulankhula mawu otani?—Aefeso 4:29; Akolose 4:6.

● Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzilankhula zinthu zabwino?—Salimo 19:14; Afilipi 4:8.

[Chithunzi patsamba 11]

Zimene timalankhula zimakhudza mmene anthu amationera