Kusamalira Mwapadera Munthu Wodwala Matenda Oti Sachira
Kusamalira Mwapadera Munthu Wodwala Matenda Oti Sachira
“Mayi anga omwe anali ndi zaka 94 anadwala kwambiri moti sankathanso kuyenda. Mtima wawo unkalephera kupopa magazi bwinobwino komanso anali ndi matenda a mu ubongo a “Alzheimer,” amene amachititsa munthu kuiwalaiwala. Nditapita nawo kuchipatala, madokotala anandiuza kuti matendawa akuwachititsa kuti asamazindikire zimene zikuchitika. Iwo ankakana kudya komanso ankangofuna kugona moti ankadana ndi zoti tiziwadzutsa. Ndinasankha kuti ndiziwasamalira kunyumba, koma ndinkafunikira thandizo lapadera.”—Anatero Jeanne.
MUNTHU amene akudwala matenda oti sachira amavutika kwambiri, komanso anthu apabanja pake amavutika nawo. Achibale amafunika kusankha ngati pangafunike kuti moyo wa munthu wodwalayo utalikitsidwe ngakhale kuti munthuyo angamavutike kwambiri ndi matenda akewo. Kapena angasankhe kuti azimupatsa chisamaliro chabwino mpaka pamene adzamwalire.
M’mayiko ena muli pulogalamu yapadera yosamalira odwala amene atsala pang’ono kufa ndipo anthu ambiri amasankha pulogalamu imeneyi. Munthu akalowa m’pulogalamuyi, amatha kulandilira kunyumba chithandizo chonse chimene akanalandira kuchipatala. Madokotala amaonetsetsa kuti wodwalayo akusamalidwa bwino komanso amaonetsetsa kuti achibale ake akucheza naye, kupemphera naye ndi kumulimbikitsa kuti asamade nkhawa kwambiri. Cholinga cha pulogalamu imeneyi ndi kuthandiza wodwalayo kuti asavutike kwambiri ndi matenda ake. Pulogalamuyi ili m’mayiko ambiri, pafupifupi theka la mayiko onse apadziko lapansi, ngakhale kuti m’mayiko ena mulibe zipangizo zokwanira. Mwachitsanzo, chifukwa cha kuchuluka kwa anthu odwala matenda a Edzi ndi khansa m’mayiko a ku Africa, mayiko ambiri ayamba kale kugwiritsa ntchito pulogalamu imeneyi ndipo ena akungoyamba kumene.
Cholinga cha Pulogalamu Imeneyi
Odwala ena akaikidwa m’pulogalamuyi, amakhumudwa chifukwa amaona kuti achibale awo awataya ndipo akungodikirira kuti afe. Ndipo achibale enanso angakhale ndi maganizo ngati amenewa. Komabe cholinga cha pulogalamu imeneyi si chimenecho. Cholinga chake ndikuthandiza kuti wodwala azilemekezedwa, azisangalala pamodzi ndi achibale ake pa nthawi imene ali ndi moyo, komanso kuti asamamve ululu kwambiri. Komanso imapatsa achibale a munthu wodwalayo mpata womulimbikitsa komanso kumuthandiza pa nthawi yonse imene adakali ndi moyo.
Ngakhale kuti wodwalayo sangachiriretu, pulogalamuyi ingathandize kuti mavuto ena ndi ena achepe monga chibayo ndi matenda ena okhudza chikhodzodzo. Wodwalayo akayamba kupezako bwino kapena ngati mankhwala a matendawo apezeka, mungamuchotse m’pulogalamuyo.
Ubwino Wosamalirira Wodwalayo Kunyumba
M’mayiko ena, chithandizo chapadera chimenechi chimapezeka kuchipatala basi. Koma m’mayiko enanso, achibale amatha kusamalira wodwala kunyumba. Ubwino wosamalira wodwalayo kunyumba ndi wakuti amatha kuchita nawo zinthu zina zapabanjapo. Komanso kuthandizira odwala
kunyumba kumagwirizana ndi chikhalidwe cha anthu m’mayiko ambiri. Mwachitsanzo, ku Uganda amaona kuti odwala kapena okalamba ayenera kusamalidwa ndi anthu apabanja pawo kunyumba.Wodwala akaikidwa m’pulogalamu imeneyi n’kumasamalidwa kunyumba, achibale ake amathandizana ndi madokotala, manesi ndi anthu enanso kusamalira munthuyo. Anthu amenewa amatha kuphunzitsa anthu amene akuyang’anira odwalawo mmene angamusamalilire komanso zimene angayembekezere iye akamamwalira. Ndiponso anthu amenewa amapereka chithandizo chogwirizana ndi zimene wodwalayo komanso abale ake akufuna. Mwachitsanzo, potsatira zofuna za achibale a odwalayo, iwo angapewe kumuyeza zinthu zosafunikira kapena kumudyetsa pogwiritsa ntchito paipi, makamaka ngati thupi la wodwalayo silingathe kugaya chakudya.
Azimayi ena awiri, Dolores ndi Jean, amasamalira bambo awo omwe ali ndi zaka 96 kunyumba. Iwo analowetsa bambo awo m’pulogalamu imeneyi ndipo chifukwa chakuti matenda awo akukulirakulira, azimayiwa amayamikira chithandizo chimene amalandira. Dolores anati: “Munthu wina amabwera masiku asanu pa mlungu kudzatithandiza kusambitsa bambo. Iye amasinthanso zofunda zawo komanso kuwathandiza kudzola mafuta ngati pakufunikira kutero. Pamabweranso nesi kamodzi pamlungu amene amadzaona mmene bambo alili komanso kuwapatsa mankhwala awo. Ndipo dokotala amabwera kamodzi pa milungu itatu iliyonse. Koma tikawafuna kwambiri, timatha kuwaitana nthawi ina iliyonse.”
Ubwino wa pulogalamu imeneyi ndi wakuti mukhoza kuitana anthu odziwa zachipatala, amene angaonetsetse kuti munthuyo akupatsidwa mankhwala oyenerera komanso sakumva ululu kwambiri. Nthawi zinanso amatha kumuika wodwalayo pa okosijeni. Chithandizo chimene akatswiri amenewa amapereka chimachititsa kuti wodwala komanso amene akumuyang’anira achotse mantha oti iye azimva ululu kwambiri kapena mantha oti pakhala mavuto ena wodwalayo akamamwalira.
Amafunika Kuwasamalira Mwachikondi
Anthu ogwira ntchito m’pulogalamu imeneyi amafunika kuonetsetsa kuti sakuchita zinthu zomuchotsera ulemu wodwalayo ndipo amamulemekeza pa nthawi yonse imene akumusamalira. Mwachitsanzo, Martha, amene wakhala akugwira
ntchitoyi kwa zaka zoposa 20, anati: “Ndinafika powadziwa bwino odwala amene ndinkawayang’anira. Ndinkadziwa zinthu zimene ankakonda komanso zimene ankadana nazo, ndipo ndinkawathandiza kuti azikhala osangalala mmene angathere pa nthawi yotsala ya moyo wawo. Nthawi zambiri ndinkazolowerana nawo moti ena tinkakondana kwambiri. N’zoona kuti anthu ena odwala matenda makamaka okhudzana ndi ubongo ankavuta kwambiri mpaka kufika pondimenya kapena kufuna kundiluma pamene ndikuwathandiza. Komabe, ndinkayesetsa kukumbukira kuti vuto si iwowo koma matenda awowo.”Ponena za mmene ankamvera pothandizana ndi anthu osamalira odwala, Martha anati: “Chisamaliro chimene ndinkapereka chinkawathandiza kuti asamadandaule kwambiri akamasamalira wodwalawo. Iwo ankatonthozedwa kungodziwa kuti anthu ogwira ntchito m’pulogalamuyi akuwathandiza kusamalira odwala awo.”
Ngati pulogalamu imeneyi imapezekanso kumene mumakhala, dziwani kuti ndi yabwino kwambiri chifukwa mumangoitana madokotala ndi manesi, m’malo mopititsa m’bale wanuyo kuchipatala kapena kukamusiya kumalo osamalira okalamba. Jeanne, yemwe tinamutchula poyamba uja, akusangalala chifukwa chakuti anaika mayi ake m’pulogalamu imeneyi. Iye anati: “Amayi anapitirizabe kukhala kunyumba pamodzi ndi ifeyo, ndipo tinkawapatsa chithandizo chilichonse chimene ankafunikira. Komanso madokotala ndi manesi ankabwera kudzawapatsa mankhwala ndi kuwalimbikitsa. Kunena zoona, aliyense ankayesetsa kusamalira mayi anga mwachikondi ndipo malangizo amene ankapereka anali othandiza kwambiri. Ndikukhulupirira kuti chisamaliro chimenechi ndi chimene mayi ankafunikira kwambiri.”
[Mawu Otsindika patsamba 17]
Ngati mukusamalira wodwala kunyumba, ndi bwino kwambiri kukhala ndi dokotala amene mungamuitane
[Bokosi/Chithunzi patsamba 16]
“Tinali Nawo Limodzi Kunyumba”
Mayi wina wa ku Mexico, dzina lake Isabel, yemwe mayi ake anavutika ndi khansa kwa zaka 16 mpaka pamene anafika poti sachiranso, anati: “Ine ndi abale anga tinali ndi nkhawa yoti mayi athu avutika kwambiri. Tinkangopemphera kuti iwo asavutike ndi ululu umene anthu ambiri odwala khansa amavutika nawo asanafe. Dokotala wina wa ku Mexico kuno, amene ndi katswiri wa mankhwala opha ululu ndi amene anatithandiza kwambiri. Iye ankabwera kamodzi pa mlungu kudzapereka mankhwala opha ululu komanso kudzatipatsa malangizo osavuta kutsatira a mmene tingagwiritsire ntchito mankhwalawo ndi mmene tingasamalilire amayi. Zinali zolimbikitsa kudziwa kuti dokotala akhoza kubwera nthawi iliyonse imene tamuitana, ngakhale usiku kwambiri. Zinali zotonthoza kuona kuti mayi athu sakumva ululu kwambiri masiku awo omaliza, komanso kuti ukawapatsa chakudya ankakwanitsa kudyako pang’ono. Tinali nawo limodzi kunyumba mpaka pamene anafera kutulo.”
[Bokosi patsamba 17]
Zimene Mungachite Wodwala Akamamalizika
Muzionetsetsa kuti zofunda n’zoyera, n’zouma komanso n’zosakwinyikakwinyika. Nthawi ndi nthawi muzimutembenuza wodwalayo komanso kumusintha zovala zamkati makamaka ngati akungodziipitsira. Zimenezi zingathandize kuti asatuluke zilonda. Ngati wodwala akukanika kuchita chimbudzi, mungamupatse mankhwala amene angamuthandize. Chakudya ndi madzi n’zosafunika kwenikweni ngati munthu akumalizika. Muzimuika thonje lonyowa kapena ayisi mkamwa komanso kumupaka mafuta m’milomo. Kugwira dzanja la wodwalayo kumakhala kotonthoza kwambiri kwa iye ndipo kumbukirani kuti akhoza kumamvabe zimene zikuchitika mpaka pamene wamwalira.