Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Abusa a Nkhosa a ku Wales Amachita Chaka Chonse

Zimene Abusa a Nkhosa a ku Wales Amachita Chaka Chonse

Zimene Abusa a Nkhosa a ku Wales Amachita Chaka Chonse

PADZIKO lonse pali nkhosa zoposa 1 biliyoni ndipo abusa amagwira ntchito yotamandika kwambiri yosamalira nkhosa zimenezi. Nyengo iliyonse pa chaka imakhala ndi ntchito yapadera imene abusa a nkhosawa amagwira. Tinacheza ndi Gerwyn, Ioan ndi Rhian, omwe ndi abusa a nkhosa kumapiri a ku Wales, kuti atiuze zambiri zokhudza ntchito yosamalira nkhosa. Ku Wales kuli nkhosa zambiri, moti chiwerengero cha nkhosa n’chochuluka kuwirikiza katatu kuposa chiwerengero cha anthu.

Ntchito Yobereketsa

Nyengo yobereketsa ikafika, abusa amagwira ntchito usana ndi usiku kuti athandize nkhosa zazikazi.

Gerwyn: “Ngakhale kuti nthawi yobereketsa ndi yotopetsa kuposa nthawi ina iliyonse pa chaka, imakhala yosangalatsa kwambiri. Kukhala ndi galu wophunzitsidwa bwino pa nthawi imeneyi kumathandiza kwambiri. Nkhosa ikamavutika kubereka, galu wanga amapita kukaigwira n’kuikhazika pansi bwinobwino kuti ndiithandize kubereka.”

Ioan: “Ngakhale kuti ndakhala ndikuthandiza nkhosa zambirimbiri kubereka, nthawi zonse ndimasangalala kwambiri ndikaona kamwana kankhosa kongobadwa kumene.”

Ntchito Yometa Nkhosa Ubweya

M’nyengo yachilimwe, abusa amakhala ndi ntchito yometa ubweya wa nkhosa. Nkhosa imodzi imatha kutulutsa ubweya wokwana makilogalamu 10. M’busa mmodzi amatha kumeta nkhosa zokwana 250 pa tsiku.

Rhian: “Ndisanayambe kumeta nkhosa ubweya, ndimachotsa kaye ubweya wothimbirira kumchira kwa nkhosayo. M’busa waluso amatha kumaliza kumeta nkhosa imodzi m’mphindi ziwiri zokha pogwiritsa ntchito malezala amagetsi. Inenso ndimathandiza nawo ntchitoyi, ndipo ndikatero ndimapindapinda ubweyawo ngati mphasa n’kuuika m’matumba kuti ukagulitsidwe.”

Abusa amachoka m’mapiri n’kupita kumalo otsika kukamweta udzu wopangira chakudya cha nkhosa. Iwo amakakhala kumeneko milungu iwiri. Chakudya chimene amapanga chimakhala chabwino kwambiri ndipo n’chimene amadyetsa nkhosa m’nyengo yonse yozizira. Achibale komanso anthu ena amathandiza kutenga chakudyacho n’kupita nacho kumapiri.

Ioan: “Nthawi inanso imene ndimasangalala kwambiri ndi pamene ndadzuka m’mawa n’kumayendayenda m’munda pambuyo poti tamweta udzu wonse.”

Ntchito Yosonkhanitsa Nkhosa

Kuti abusa alekanitse nkhosa zazikazi ndi ana awo, amatenga nkhosazo n’kutsika nazo kuchoka m’mapiri muja.

Ioan: “Ngakhale mutapanda kuzilowetsa m’khola kapena kuzimangira mpanda, nkhosa sizisochera wamba kapena kumangoyenda chisawawa mpaka kukalowa m’munda wa eniake. Pamalo athu owetera nkhosa, nkhosa iliyonse yaikazi imadziwa malire a malowo. Iyo imaphunzira zimenezi kuchokera kwa mayi ake kapena m’busa, ndipo nkhosayo imadzaphunzitsanso ana ake aakazi. Komabe nthawi zina nkhosa zina zimasochera ndipo timatha maola ambiri kapena masiku angapo tikuzifunafuna.”

Abusa amafufuzanso nkhosa zamphongo zabwino pa nkhosa zimene ali nazo kapena kukagula n’kukaziika pamodzi ndi zazikazi. Zimenezi zimathandiza kuti nkhosa zizichulukana. Pamafunika nkhosa imodzi yaimuna pa nkhosa zazikazi 25 kapena 50 zilizonse.

Pambuyo pa milungu 10 kapena 12 kuchokera pamene nkhosa zamphongo zakhalira pamodzi ndi nkhosa zazikazi, abusa amagwiritsa ntchito makina enaake kuti aone nkhosa zimene zili ndi bere komanso kuti adziwe kuti zidzabereka ana angati. Nkhosa zosabereka zimagulitsidwa. Zimene zidzabereke mwana mmodzi zimaikidwa pagulu limodzi, ndipo zimene zidzabereke ana awiri kapena atatu, zimasamalidwa mwapadera komanso kupatsidwa chakudya chambiri.

Ntchito Yodyetsa Nkhosa M’nyengo Yozizira

Ntchito yaikulu imene abusa amagwira m’nyengo yozizira ndi kudyetsa nkhosa zabere, moti abusa amathera nthawi yawo yonse masana akudyetsa nkhosazo. Kaya kunja kwacha bwanji, nthawi zonse m’busa satalikirana ndi nkhosa zake ndipo amaonetsetsa kuti zili ndi chakudya chokwanira.

Gerwyn: “M’nyengo yotereyi, nkhosa zimafuna kusamalidwa kwambiri ndipo m’busa amafunikira kuzipatsa chakudya chokwanira komanso kuziteteza.”

Rhian: “Ndimasangalala kwambiri ndi ntchito yosamalira nkhosa chifukwa ndimakhala panja chaka chonse n’kumaona nyama zakuthengo komanso zomera zosiyanasiyana zikusintha mogwirizana ndi nyengo.”

[Mapu patsamba 12]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

NORTHERN IRELAND

IRELAND

SCOTLAND

WALES

ENGLAND

[Chithunzi patsamba 14]

Ioan akufufuza nkhosa yaimuna yoyenera

[Chithunzi patsamba 14]

Gerwyn ndi galu wophunzitsidwa bwino