Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Kafukufuku amene anachitidwa ndi bungwe loona za ngozi zapamsewu kumayiko a Aluya, lomwe likulu lake lili ku Tunisia, anasonyeza kuti kumayiko a Aluya kumachitika ngozi zapamsewu zoposa 500,000 chaka chilichonse, ndipo anthu oposa 36,000 amafa pa ngozi zimenezi.—REUTERS NEWS SERVICE, TUNISIA.

“Kafukufuku wina anasonyeza kuti achinyamata ambiri ku China amaphunzira zambiri zokhudza kugonana kudzera pa Intaneti chifukwa chakuti achinyamatawa saphunzitsidwa mokwanira nkhani zimenezi kusukulu ndi kunyumba.”—CHINA DAILY, CHINA.

Kuona Zinthu za M’makompyuta a Ena Mwakuba

Posachedwapa apolisi ku Germany anagwira munthu wina amene akumuimba mlandu woona zimene zikuchitika m’zipinda za atsikana ambirimbiri pogwiritsa ntchito makamera amene analumikizidwa ku makompyuta a atsikanawo. Akuti munthuyo anakwanitsa kulowa mu kompyuta ya mtsikana mmodzi pogwiritsa ntchito nambala yachinsinsi yomwe inali yosavuta kuitulukira. Atalowa mu kompyuta imeneyi anakwanitsanso kulowa m’makompyuta a atsikana enawo. Akuti anagwiritsanso ntchito adiresi ya mtsikanayo kutumizira atsikana ena mapulogalamu owononga kompyuta amene ankaoneka ngati zithunzi basi. Iye ankatha kuchita zimene akufuna pamakompyuta a atsikana enawo, ngakhalenso kugwiritsa ntchito makamera awo nthawi ina iliyonse. Apolisi atakafufuza kunyumba kwa munthuyo, anapeza kuti anali ndi zithunzi zokwana 3 miliyoni, komanso malinga ndi nyuzipepala ina m’dzikolo, “ankatha kulumikiza kumakompyuta a atsikana 80 n’kumaona zimene iwo akuchita popanda eniakewo kudziwa.”—Aachener Zeitung.

Akatswiri Atulukira Zilankhulo Zina

Akatswiri a zilankhulo amene ankafufuza zilankhulo za Aka ndi Miji, atulukira chilankhulo china chachitatu chotchedwa Koro. Zilankhulo zitatuzi ndi za ku Arunachal Pradesh, lomwe ndi dera lakumpoto chakum’mawa kwa dziko la India, ndipo linachita malire ndi dziko la Bhutan ndi China. Katswiri wina, dzina lake Gregory Anderson, yemwe ndi mkulu wa bungwe lina la zilankhulo, anati: “Anthu ambiri sankadziwa kuti kuli chilankhulo chimenechi chifukwa chakuti palibe mabuku kapena zinthu zina zofotokoza bwinobwino za chilankhulochi.” Komanso chilankhulo cha Koro sichinkadziwika chifukwa chakuti chimalankhulidwa ndi anthu 800 okha amenenso amakhala m’dera lovuta kupitako. M’chaka cha 2009, kudera lina ku China kumene kunkadziwika kuti kuli chilankhulo chimodzi, kunapezeka kuti kuli zilankhulo 24.

Nguluwe za Poizoni

Nyuzipepala ina ya ku Germany inati: “Kuchokera m’chaka cha 2007, ndalama zimene boma limalipira anthu osaka nguluwe [ku Germany] zawonjezereka kuwirikiza kanayi. Boma limalipira anthuwa chifukwa chakuti zina mwa nguluwe zimene amapha zimakhala ndi poizoni.” Alenje ambiri amagulitsa nguluwezi kwa anthu kuti akachite ndiwo, koma boma limaletsa kugulitsa nyama imene ili ndi poizoni wambiri wotchedwa cesium-137. Poizoni ameneyu anafalikira m’derali fakitale yopanga zida za nyukiliya ku Chernobyl itaphulika zaka 25 zapitazo. Nyuzipepalayi inanena kuti nguluwe zimapezeka kwambiri ndi poizoni ameneyu chifukwa chakuti zimakonda kudya bowa ndi zakudya zina zimene zimayamwa poizoni wambiri kuchokera m’nthaka.” Nyuzipepalayi inanenanso kuti: “Boma likulipira ndalama zambiri osati kwenikweni chifukwa chakuti poizoniyi akuwonjezereka, koma chifukwa chakuti nguluwe zikuchulukana kwambiri.” Akatswiri akuti vuto la poizoni ameneyu silitha mpaka zaka 50 kutsogoloku.