Dzira
Kodi Zinangochitika Zokha?
Dzira
● Anthu amanena kuti dzira la nkhuku kapena la mbalame linapangidwa modabwitsa kwambiri. N’chifukwa chiyani amatero?
Taganizirani izi: Ngakhale kuti chakunja cha dzira la nkhuku chimaoneka cholimba, chimakhala ndi timabowo tosaoneka tokwana pafupifupi 8,000. Mabowo amenewa amachititsa kuti mpweya wabwino uzitha kulowa komanso mpweya woipa uzitha kutuluka m’dziramo. Zimenezi zimathandiza kuti kamwana ka nkhuku mkatimo kakhale ndi moyo. Koma chochititsa chidwi n’chakuti mabakiteriya sangathe kulowa mkati kudzera m’timabowo timeneti, chifukwa amatchingidwa ndi chakunjachi komanso tizikopa tina mkatimo. Timadzi timene timapezeka m’dzira timachititsa kuti dziralo likakhutchumuka, kamwana mkatimo kasavulale.
Potengera mmene dzira linapangidwira, asayansi akuganiza zopanga zovala ndi zipewa zoti munthu asamavulale kwambiri akachita ngozi, komanso akuganiza zopanga timapepala tapulasitiki tokutirira zipatso, toteteza kuti tizilombo tisadye zipatsozo. Komabe katswiri wina, dzina lake Marianne Botta Diener, analemba kuti: “Kutengera zinthu zam’chilengedwe n’kovuta kwambiri.” Malinga ndi zimene mayiyu ananena, zinthu zimene asayansi akugwiritsa ntchito poyesa kupanga zinthu zimenezi, zikuwononganso chilengedwe.
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti dzira lipangidwe ndi zinthu zogometsa chonchi, kapena ndi umboni wakuti alipo analipanga?
[Chithunzi patsamba 28]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
MKATI MWA DZIRA
Chakunja cha dzira
Chamkati mwa dzira
Cholumikizira
Kachikopa kakunja
Kachikopa kamkati
Pamene kamwana kamayambira
Timadzi
Timadzi tolimbirako
Danga la mpweya