Kulera Ana Kuti Akule Bwino
Kulera Ana Kuti Akule Bwino
Makolo akamayang’ana mwana wawo wongobadwa kumene amasangalala kwambiri. Pa nthawi imeneyi, iwo saganizira kwenikweni kuti mwanayo tsiku lina adzachoka pakhomo pawo n’kukakhala payekha. Koma zoona zake n’zakuti iye akadzakula adzachitadi zimenezi. Mmenemu ndi mmene Mulungu anakonzera kuyambira pachiyambi, chifukwa Baibulo limanena kuti “mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake.” (Genesis 2:24) Mofanana ndi mwana wamwamuna, nayenso mwana wamkazi akakula amasiya makolo ake.
Komabe, nthawi ikafika yakuti mwana achoke panyumba n’kumakakhala payekha, makolo amada nkhawa kwambiri. Makolo ambiri amadzifunsa kuti: ‘Kodi tamulera bwino mwana wathuyu?’ ‘Kodi akakwanitsa kukhala bwino ndi anthu kuntchito, kusamalira nyumba yake komanso kusamala ndalama?’ Funso linanso lofunika kwambiri limene makolo amadzifunsa ndi lakuti: ‘Kodi mwana wathuyu akapitiriza kutsatira mfundo zimene tinamuphunzitsa?’—Miyambo 22:6; 2 Timoteyo 3:15.
Galamukani! yapaderayi ifotokoza malangizo a m’Baibulo amene angathandize makolo kuti alere bwino ana awo, kuyambira pamene angobadwa mpaka pamene adzachoke pakhomo.