Kodi Tizitchula Zinthu Ziti Tikamapemphera kwa Mulungu?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Tizitchula Zinthu Ziti Tikamapemphera kwa Mulungu?
KULANKHULA ndi Wamphamvu yonse komanso kumuuza zakukhosi kwathu ndi mwayi waukulu. Komabe, anthu ena sadziwa zimene ayenera kutchula popemphera ndipo ena amafuna atadziwa zimene angatchule popemphera kuti azipereka mapemphero abwino. Zikuoneka kuti otsatira ena a Yesu Khristu oyambirira ankafuna kuti adziwe bwino mmene angamapempherere. Mmodzi wa iwo anapempha Yesu kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera.” (Luka 11:1) Poyankha, Yesu anawapatsa chitsanzo cha mmene angapempherere. Pemphero limeneli limadziwika kuti Pemphero la Ambuye kapena kuti Pemphero la Atate. Pemphero limeneli lili ndi mfundo zabwino komanso ndi lalifupi ndipo limatithandiza kudziwa mmene tingalankhulire ndi Mulungu m’njira yoyenera. Pempheroli limatithandizanso kumvetsa mfundo yaikulu ya Baibulo.
Pemphero la Yesu la Chitsanzo
Yesu ananena kuti: “Koma inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Mutikhululukire zolakwa zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira. Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.’”—Mateyu 6:9-13.
Onani kuti Yesu ananena kuti: “Muzipemphera motere.” N’chifukwa chiyani Yesu ananena zimenezi? Yesu sankafuna kuti otsatira ake azingobwereza zimene iye wanena kapena kuziloweza pamtima, ndipotu anali atangowaletsa kumene kuchita zimenezi. (Mateyu 6:7) M’malomwake, pemphero lakeli limatithandiza kudziwa kuti zinthu zofunika kwambiri ndi zokhudza Mulungu osati zokhudza ifeyo basi. Kuti tidziwe zinthu zofunika zimenezi, tifunika kumvetsa tanthauzo la mawu a Yesu. Tiyeni tione mfundo zimene Yesu anatchula m’pemphero lakeli, iliyonse payokha.
Zimene Pemphero la Chitsanzo Limatanthauza
“Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” Yesu anatchula Mulungu kuti “Atate” ndipo mpake kumutchula choncho chifukwa amatikonda ndiponso kutisamalira ngati mmene bambo wabwino amachitira ndi ana ake. Mulungu ali ndi dzina lake lenileni lomwe ndi Yehova. Dzina limeneli si lofanana ndi mayina ake audindo monga Wamphamvuyonse, Mulungu ndi Ambuye. * (Salimo 83:18) Nangano n’chifukwa chiyani dzina la Mulungu, lomwenso limafotokoza za khalidwe lake, likufunikira kuyeretsedwa? Chifukwa chakuti dzinali lakhala likunyozedwa komanso kuneneredwa zinthu zambiri zabodza.
Anthu ena amaimba Mulungu mlandu kuti ndi amene amachititsa mavuto, pamene mavuto awowo amabwera chifukwa cha anthu ena kapena chifukwa chakuti iwowo anali pamalo olakwika panthawi yolakwikanso. (Miyambo 19:3; Mlaliki 9:11) Enanso amaimba Mulungu mlandu kuti ndiye amachititsa masoka achilengedwe. Koma Baibulo limatiuza kuti: “Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobo 1:13) Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti Mulungu amalanga anthu oipa powawotcha ndi moto kwamuyaya. Chiphunzitso chimenechi sichigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu ndi wachikondi. (Yeremiya 19:5; 1 Yohane 4:8) Lemba la Aroma 6:23 limanena kuti “malipiro a uchimo ndi imfa,” osati kuwotchedwa ndi moto kwamuyaya. *
“Ufumu wanu ubwere.” Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni ndipo Mfumu yake ndi Yesu Khristu. Danieli 7:14 limanena kuti “anamupatsa ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu.” Ufumu wa Mulungu ‘udzabwera’ kuti uphwanye maboma onse a anthu n’kuyamba kulamulira dziko lonse.—Danieli 2:44.
Iye posachedwapa adzayamba kulamulira dziko lonse lapansi. Lemba la“Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira, anthu onse azidzachita chifuniro cha Mulungu. Ndipo chifukwa cha zimenezi, padziko lonse padzakhala mtendere ndipo anthu onse azidzalambira Mulungu m’njira yoyenera. Zinthu zimene zimachititsa anthu kuti asamagwirizane, monga ndale ndi chipembedzo chonyenga, sizidzakhalaponso. Lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 limanena mophiphiritsa kuti “Chihema cha Mulungu” chidzakhala “pakati pa anthu.” Lembali limapitiriza kuti: “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”
“Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.” Atatchula zinthu zofunika kwambiri zokhudza dzina la Mulungu komanso Ufumu wake, Yesu anayamba kutchula zinthu zofunika pa moyo wathu. Mawu ake amasonyeza kuti tiyenera kupewa kufuna zinthu zambiri kuposa zimene timafunikira pa tsiku. M’malomwake, tiyenera kutsatira zimene lemba la Miyambo 30:8 limanena kuti: “Musandipatse umphawi kapena chuma. Ndidye chakudya chimene ndikufunika kudya.”
“Mutikhululukire zolakwa zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira.” Zolakwa zathu zili ngati ngongole imene timabweza tikamamvera Mulungu. Choncho tikachimwa timakhala ngati tikudziunjikira ngongoleyo. Koma Yehova amatikhululukira ngati nafenso takhululukira anzathu.—Mateyu 18:21-35.
“Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.” “Woipa” amene akutchulidwa palembali ndi Satana Mdyerekezi, yemwe amadziwikanso kuti “Woyesayo.” (Mateyu 4:3) Chifukwa cha kupanda kwathu ungwiro, timafunika kuti Mulungu atithandize kulimbana ndi Satana komanso anthu amene amachita zofuna zake.—Maliko 14:38.
Tikukhulupirira kuti pemphero la Yesu la chitsanzo likuthandizani kudziwa mmene mungapempherere komanso kudziwa zinthu zofunika kwambiri kuzitchula m’pemphero. Koma kodi pemphero limeneli limatithandiza kudziwa bwanji mfundo yaikulu ya m’Baibulo? Mogwirizana ndi mawu a Yesu, mfundo yaikulu ya m’Baibulo ndi kuyeretsedwa kwa dzina lopatulika la Mulungu, kuchotsedwa kwa zinthu zonse zoipa komanso kubwera kwa Ufumu wa Mulungu umene udzabweretsa mtendere pa dziko lapansi. Choncho, Yesu anafotokozadi mfundo zofunika kwambiri m’pemphero lake lachitsanzo.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 M’zilankhulo zoyambirira zimene anagwiritsa ntchito polemba Baibulo, makamaka Chiheberi ndi Chigiriki, dzinali limapezeka nthawi pafupifupi 7,000. Koma n’zomvetsa chisoni kuti Mabaibulo ambiri masiku ano anachotsamo dzina lakuti Yehova n’kuikamo mayina ake audindo.
^ ndime 9 Anthu akufa sakhala ndi moyo kwinakwake. Koma ali “m’tulo” kapena kuti “sadziwa chilichonse,” ndipo akungoyembekezera kudzaukitsidwa.—Yohane 5:28, 29; 11:11-13; Mlaliki 9:5.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
● Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Muzipemphera motere”?—Mateyu 6:9.
● Kodi nthawi zonse tikafuna kupemphera, ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuzitchula poyamba?—Mateyu 6:9, 10.
● N’chifukwa chiyani tiyenera kukhululukira anthu amene amatilakwira?—Mateyu 6:12.
[Chithunzi patsamba 13]
Pemphero lachitsanzo la Yesu limatithandiza kudziwa kuti zinthu zofunika kwambiri ndi zokhudza Mulungu osati zokhudza ifeyo basi