Buluzi wa Diso Logometsa
Kodi Zinangochitika Zokha?
Buluzi wa Diso Logometsa
● Pali mtundu winawake wa buluzi yemwe amati akaduka mchira, miyendo kapena chiwalo china chathupi lake, chimatha kumeranso. Koma kodi chiwalo chimene chameracho chimakhala chofanana ndi chimene chinaduka chija? Akatswiri amene anafufuza za buluziyu ananena kuti chimakhala chofanana. Mwachitsanzo, diso la buluziyu lili ndi kagalasi kamene kamathandiza kuti aziona bwino. Kagalasiko kakachoka, kamameranso kofanana ndendende.
Taganizirani izi: Diso la buluziyu lili ndi minyewa yomwe inazungulira mwana wadiso. Ndiyeno ngati kagalasi kam’diso kaja kachoka, maselo a minyewayi amasintha n’kupanganso kagalasi kena. Asayansi anatha zaka 16 akufufuza abuluzi angapo a ku Japan kuti adziwe mmene zimenezi zimachitikira. Iwo ankati akachotsa kagalasi kam’diso la buluzi, kankameranso, ndipo anachita zimenezi maulendo 18 kwa buluzi aliyense.
Mmene ankamaliza kafukufukuyu, n’kuti buluzi aliyense ali ndi zaka 30. Nthawi zambiri abuluziwa akakhala kutchire amafa ali ndi zaka 25. Koma ngakhale kuti abuluziwa anali ndi zaka zambiri chonchi, kagalasi ka m’diso lawo kankamera mofulumira ngati mmene buluzi wamng’ono amachitira. Akatswiri a pa yunivesite ya Dayton ku Ohio, m’dziko la America, ananena kuti: “Kagalasi kamene kameranso kamakhala kofanana ndendende ndi ka buluzi amene sanachotsedwepo kagalasi chibadwire.” Katswiri wina yemwe anachita nawo kafukufuku uja ananena kuti: “Ndinadabwa kuona kuti kagalasi kamene kameranso sikasiyana chilichonse ndi kagalasi kamene sikanachotsedwepo.”
Asayansi akukhulupirira kuti zimene zimachitika ndi buluziyu ziwathandiza kupeza njira za mmene angathandizire anthu amene maselo a m’thupi lawo awonongeka. Katswiri uja ananenanso kuti: “Zimene zimachitika ndi buluziyu zikhozanso kutithandiza kupeza njira yothandizira anthu okalamba kuti maselo a m’thupi mwawo asamafe.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti kagalasi ka m’diso la buluzi kazimeranso kakachotsedwa, kapena umenewu ndi umboni wakuti pali wina amene anakalenga?
[Chithunzi patsamba 25]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Kagalasi kamene kameranso kamakhala kofanana ndendende ndi kamene sikanachotsedwepo
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Top photo: © Vibe Images/Alamy; middle photo: © Juniors Bildarchiv/Alamy