Kodi Nyamakazi ya M’mafupa Imayamba Bwanji?
Kodi Nyamakazi ya M’mafupa Imayamba Bwanji?
NYAMAKAZI ya m’mafupa ndi imodzi mwa nthenda zopweteka komanso zimene zimagwira anthu ambiri. Buku lina linanena kuti: “Nyamakazi ya m’mafupa imayamba chifukwa chakuti thupi lalephera kugaya bwinobwino mchere winawake wa m’thupi. Munthu amayamba kudwala ngati timibulu ta michere imeneyi taunjikana molumikizana mafupa, . . . makamaka pachala chachikulu chakuphazi.”
Thupi lathu linapangidwa kuti likagaya zakudya, lizichotsa zinthu zina zosafunikira monga michere yomwe imapezeka m’magazi. Mwachitsanzo thupi likalephera kuchotsa michereyi, imapanga timibulu tobaya tomwe timakaunjikana molumikizana mafupa. Nthawi zambiri imakaunjikana pachala chachikulu chakuphazi, koma ikhoza kuunjikana paliponse pamene mafupa analumikizana. Zimenezi zikachitika, polumikizirana mafupapo pamatupa, kuotcha komanso kupweteka kwambiri. * Munthu wina amene amadwala nthendayi, dzina lake Alfred, ananena kuti: “Kungokhudzapo pang’ono pokha umakhala ngati akubaya ndipo umamva kupweteka kwambiri.”
Bungwe lina la ku Australia, loona za nthenda ya nyamakazi, linanena kuti: “Munthu amene amadwala nthendayi amatha kumva kupweteka kwambiri kwa mlungu umodzi ngati sanamwe mankhwala. Zikatero pakhoza kutenga miyezi kapenanso zaka kuti adzayambenso kumva kupweteka. Koma ngati munthu sanalandire chithandizo, akhoza kumamva kupweteka kwambiri komanso pafupipafupi zomwe zingachititse kuti mafupa ake asamagwire ntchito bwinobwino. Anthu ena amafika podwala nthendayi tsiku lililonse.”
Koma chosangalatsa n’chakuti nyamakazi ya m’mafupi ndi imodzi mwa nthenda zimene zikhoza kuchizidwa. Mwachitsanzo munthu wodwala nthendayi amapatsidwa mankhwala othandiza kuti molumikizira mafupa musatupe. Koma amene akudwala kwambiri matendawa amawapatsa mankhwala oti
michere isamaunjikane molumikizira mafupa. Kwa munthu woti ali ndi matendawa, kodi pali zimene angachite kuti asamadwaledwale? Inde zilipo, makamaka ngati munthuyo akudziwa zimene zimachititsa kuti azidwaladwala.Zimene Zimachititsa
Anthu ambiri amadwaladwala matendawa chifukwa cha ukalamba, kutengera kwa makolo awo komanso ngati ndi aamuna. Akatswiri ena amanena kuti pa anthu 100 alionse amene amadwala nthendayi, anthu oposa 50 amakhala kuti anatengera kwa makolo awo. Mwachitsanzo, Alfred amene tamutchula poyamba uja, ananena kuti: “Bambo anga komanso agogo anga aamuna ankadwala nthendayi.” Nthawi zambiri matendawa amagwira anthu aamuna, makamaka amene ali ndi zaka pakati pa 40 ndi 50. Ndi azimayi ochepa amene amadwala matendawa ndipo amadwala asanafike zaka zosiya kusamba. Komanso munthu angadwale pa zifukwa zotsatirazi:
Zakudya komanso kunenepa kwambiri: Buku lina linanena kuti: “Pofuna kuthandiza anthu kuti asamadwaledwale, poyamba anthu odwala matendawa ankaletsedwa zakudya zina, zomwe madokotala ankaganiza kuti zimachititsa kuti munthu adwale. Koma masiku ano madokotala akulimbikitsa anthu kuti azipewa kunenepa kwambiri komanso akumawapatsa mankhwala amene amachotsa zinthu zosafunikira m’thupi, zimene zingayambitse matendawa.”—Encyclopedia of Human Nutrition
Komabe madokotala ena amalimbikitsa anthu kuti azipewa kudya nsomba zamitundu ina, nyama komanso zakudya zimene athira yisiti. *
Mowa: Munthu akamamwa mowa kwambiri thupi lake limalephera kuchotsa michere yosafunikira m’thupi. Zikatero michereyo imakaunjikana molumikizira mafupa.
Matenda ena: Madokotala a pachipatala cha Mayo ku United States, ananena kuti munthu akhoza kuyamba kudwala matendawa ngati “sakulandira chithandizo cha mankhwala a nthenda yothamanga magazi. Akhozanso kudwala ngati amadwala matenda a shuga, ngati ali ndi mafuta ambiri m’thupi komanso ngati mitsempha yodutsa magazi yayamba kutsekeka.” Munthu akhozanso kudwala nthendayi ngati “wadwala mwadzidzidzi, wavulala komanso ngati wakhala nthawi yaitali akungogona chifukwa cha matenda.” Akhozanso kudwala ngati ali ndi vuto la impso. Nthawi zambiri michereyi imakonda kuunjikana pachala chachikulu chakuphazi chifukwa chakuti magazi safikako mokwanira komanso chifukwa chakuti mapazi amakhala ozizira.
Mankhwala: Ena mwa mankhwala amene angachititse kuti munthu adwale matendawa ndi mankhwala a khansa, asipulini, mankhwala a matenda othamanga magazi omwe amathandiza kuchotsa madzi m’thupi, komanso mankhwala amene amapatsa munthu yemwe amuchita opaleshoni yoika chiwalo china.
Zimene Mungachite Kuti Musadwalenso
Popeza kuti anthu ambiri amadwala nthendayi chifukwa cha zimene amadya kapena kumwa, malangizo otsatirawa angathandize anthuwa kuti asamadwaledwale. *
1. Nthenda ya nyamakazi imayamba thupi likalephera kugaya bwinobwino zakudya. Choncho munthu amene ali nayo kale ayenera kupewa kudya zakudya zonenepetsa. Komanso munthu wonenepa kwambiri akhoza kudwala mosavuta chifukwa mafupa ake amalemedwa.
2. Musamadzimane zakudya zopatsa thanzi n’cholinga choti muchepe thupi mwachangu. Kuchita zimenezi kungawonjezere mchere m’magazi mwanu.
3. Musamadye nyama kwambiri. Ena amati ndi bwino kuti patsiku munthu azidya nyama yochepa yopanda mafuta ambiri, kuphatikizapo nsomba ndi nkhuku.
4. Musamamwe mowa mopitirira malire ndipo ngati mukudwala matendawa mungachite bwino kusiyiratu.
5. Muzimwa madzi ambiri ndi zakumwa zina zosaledzeretsa chifukwa zimathandiza kusungunula komanso kuchotsa mchere m’thupi. *
Mfundo zimene takambirana mu nkhani ino zikutikumbutsa malangizo ochokera m’Baibulo akuti tisamachite “zinthu mopitirira malire” komanso kuti tisamakonde “kumwa vinyo wambiri.” (1 Timoteyo 3:2, 8, 11) Kunena zoona, Mlengi wathu amadziwa bwino kwambiri zimene zili zoyenera komanso zosayenera kwa ife.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Palinso nthenda ina yomwe zizindikiro zake zimafanana ndi za nyamakazi ya m’mafupa. Koma munthu akadwala nthenda imeneyi amafunika chithandizo chosiyana ndi cha nyamakazi ya m’mafupa.
^ ndime 9 Magazini ina inanena kuti ngakhale kuti zakudya monga bowa, nyemba, mphodza, nsawawa, spinachi ndi ndiwo zina zamasamba zili ndi michere yambiri imene ingayambitse nyamakazi ya m’mafupa, “palibe umboni wosonyeza kuti zakudyazi zimayambitsadi matendawa.”
^ ndime 14 Cholinga cha nkhani ino sikusankhira anthu zochita pa nkhani ya mankhwala. Aliyense ayenera kulandira chithandizo cha mankhwala mogwirizana ndi vuto lake. Choncho simuyenera kusiya kumwa mankhwala amene adokotala anakupatsani kapena kusintha zakudya zimene mumadya musanakambirane ndi adokotala.
^ ndime 19 Malangizowa achokera ku bungwe la Mayo Foundation for Medical Education and Research.
[Chithunzi patsamba 24]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Polumikizirana mafupa patatupa
Kamnofu koteteza kuti mafupa asamakhulane
[Chithunzi]
Michere itaunjikana