Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Cameroon

Dziko la Cameroon

ANTHU oyambirira kukhala ku Cameroon anali amtundu wa Baka omwenso amatchedwa Abathwa. Kenako Apwitikizi anafika m’dzikoli cha m’ma 1500. Patapita zaka zambiri, kunafikanso anthu amtundu wa Fulani, omwe anali Asilamu ndipo anagonjetsa anthu omwe ankakhala kumpoto kwa dziko la Cameroon. Masiku ano ku Cameroon, anthu 40 pa 100 alionse amati ndi Akhristu, 20 pa 100 alionse ndi Asilamu ndipo anthu 40 pa 100 alionse ali m’zipembedzo za makolo.

A Mboni za Yehova amafalitsa mabuku ofotokoza Baibulo m’chinenero cha Chibasa chomwe chimalankhulidwa ku Cameroon

Anthu a ku midzi ya ku Cameroon amadziwa kuchereza alendo. Mlendo akafika amamulowetsa m’nyumba n’kumpatsa moni. Kenako amamupatsa madzi ndi chakudya. Anthuwa amaona kuti kukana chakudya ndi mwano.

Akamacheza ndi mlendo, amayamba kumufunsa za mmene alili komanso za banja lake. Nthawi zina amatha kufunsanso mmene ziweto zawo zilili. Joseph,  yemwe amakhala ku Cameroon, ananena kuti: “Mlendo akatsanzika, timamuperekeza kwinaku tikucheza naye mpaka kukabwerera kunjira, ndipo akapanda kuperekezedwa amaona kuti sanalandiridwe bwino.”

Mu mtsinje wa Sanaga mumadutsa mabwato ambiri. Nsalu zoyendetsera mabwatowa zimapangidwa kuchokera ku zinthu zosiyanasiyana

Nthawi zina anthu amadyera chakudya m’mbale imodzi ndi manja. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti anthuwo ndi ogwirizana. Nthawi zina, kudyera chakudya mbale imodzi kumathandiza kuti anthu omwe anasiya kuchezerana ayambirenso kugwirizana. Akamadyera limodzi amakhala ngati akunena kuti, “Basi takhululukirana.”

A Mboni za Yehova omwe amafalitsa magazini ino, ali m’mipingo yoposa 300 ku Cameroon ndipo akuphunzitsa Baibulo anthu pafupifupi 65,000