ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Ufumu wa Mulungu
Kodi Ufumu wa Mulungu umakhala mumtima mwa munthu?
“Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.”
—Maliko 12:34.
ZIMENE ANTHU AMANENA
Anthu ambiri amakhulupirira zimene chipembedzo china chimaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu “umakhala mumtima mwa munthu ndipo umalamulira moyo komanso zochita za munthuyo.”
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni ndipo n’zosiyana ndi zimene anthu amakhulupirira kuti munthu akamamvera malamulo a Mulungu mumtima mwake, ndiye kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira mumtimamo. Baibulo limasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu udzalamulira padziko lonse lapansi.—Salimo 72:8; Danieli 7:14.
Nanga Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti “Ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu”? (Luka 17:21, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Pamenepa sikuti Yesu ankatanthauza kuti ufumu wa Mulungu unali m’mitima ya anthu amene ankamumvetserawo. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti ankalankhula mawu amenewa kwa Afarisi. Yesu ananena kuti Afarisi sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu chifukwa kulambira kwawo kunali kwachinyengo komanso kosavomerezeka kwa Mulungu. (Mateyu 23:13) Choncho, Yesu sankalakwitsa pouza Afarisi kuti Ufumu wa Mulungu uli “mkati mwa inu” kapena kuti “uli pakati panu,” mogwirizana ndi Baibulo la Dziko Latsopano. Zili choncho chifukwa Yesu yemwe anali kudzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu anali pakati pawo.—Luka 17:21.
Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?
“Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.”—Mateyu 6:10.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni limene Mulungu analikhazikitsa ndipo Yesu Khristu ndi Wolamulira wake. (Mateyu 28:18; 1 Timoteyo 6:14, 15) Cholinga cha ufumu umenewu ndi kukwaniritsa chifuniro cha Mulungu kumwamba ndi padziko lapansi. (Mateyu 6:10) Mulungu adzagwiritsa ntchito ufumuwu kuthetsa mavuto onse. Ufumuwu udzachita zimene maboma a anthu alephera.
Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, anthu adzakhala pa mtendere ndipo azidzasangalala m’paradaiso padziko lapansi. (Salimo 46:9; Yesaya 35:1; Mika 4:4) Palibe amene azidzadwala kapena kumwalira ndipo matenda adzatheratu. (Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:4) Anthu okalamba adzakhalanso anyamata. Baibulo linalosereratu kuti: “Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata. Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.”—Yobu 33:25.
ZIMENE MUNGACHITE
Kaya munabadwira kuti kapena banja liti, mukhoza kukhala nzika ya Ufumu wa Mulungu ngati mutamachita zimene Mulungu amafuna. Baibulo limanena kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Machitidwe 10:34, 35.
Kodi anthu ndi amene adzabweretse Ufumu wa Mulungu?
“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.”
—Danieli 2:44.
ZIMENE ANTHU AMANENA
Ena amakhulupirira kuti anthu ndi amene adzabweretse Ufumu wa Mulungu, ndipo adzachita zimenezo pokopa anthu kuti alowe m’chipembedzo chawo kapena kukhazikitsa mtendere ndi mgwirizano padziko lonse.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Mulungu ndi amene adzabweretse Ufumu umenewu osati anthu. (Danieli 2:44) Pa nthawi imene ankakhazikitsa Ufumuwo, Mulungu anati: “Inetu ndakhazika mfumu yanga.” (Salimo 2:6) Choncho anthu sangabweretse Ufumu wa Mulungu ndipo sangasokoneze cholinga cha Ufumuwo chifukwa likulu lake lili kumwamba ndipo udzalamulira dziko lonse.—Mateyu 4:17.
ZIMENE MUNGACHITE
Sizolakwika kulakalaka anthu atakhala pa mtendere komanso ali ogwirizana. Mwina mungayesetse kuchita zinthu zoti padziko lapansi pakhale mtendere ndi mgwirizano koma mungakhumudwe kwambiri kuona kuti zimenezi sizikutheka. Kudziwa mfundo yakuti Mulungu ndi amene adzakhazikitse Ufumuwu padziko lapansi kungakuthandizeni kuchita zonse zomwe mungathe kuti mukhale nzika ya ufumu wa Mulungu.