Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Webusaiti Yothandiza Kwambiri

Webusaiti Yothandiza Kwambiri
  • WERENGANI Baibulo m’zinenero pafupifupi 50 komanso werengani mabuku othandiza kuphunzira Baibulo m’zinenero zoposa 500.

  • ONERANI mavidiyo a chinenero chamanja m’zinenero pafupifupi 70.

  • SANKHANI chinenero chimene mukufuna pa zinenero zambirimbiri zimene zikupezeka.

  • MVETSERANI masewero a nkhani za m’Baibulo.

  • ONANI zithunzi zofotokoza nkhani za m’Baibulo n’kuwerenga mawu ake.

  • ONERANI masewero komanso mavidiyo a nkhani za m’Baibulo amene angakuthandizeni kuthana ndi mavuto pa moyo wanu.

  • PANGANI DAWUNILODI mabuku, magazini, nkhani komanso zinthu zomvetsera, ndipo zonsezi ndi zaulere.

  • FUFUZANI nkhani zosiyanasiyana pogwiritsa ntchito LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower. Mungapeze nkhani zambiri zothandiza zomwe zikupezeka m’zinenero pafupifupi 100.

 NDI YOTHANDIZA ANTHU APABANJA

“Ndikufuna kuti banja langa liziyenda bwino. Ine ndi mkazi wanga takhala tisakugwirizana makamaka kuyambira pamene tinayamba kukhala ndi ana. Tikufuna kupeza malangizo amene angatithandize kuti banja lathu liziyenda bwino”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Nzeru zimamanga banja la munthu, ndipo kuzindikira kumachititsa kuti lilimbe kwambiri.”—Miyambo 24:3.

NKHANI ZIMENE MUNGAPEZE PA WEBUSAITIYI

Mbali yakuti “Anthu Apabanja Ndiponso Makolo” ingakuthandizeni pa nkhani ngati izi:

  • Zimene Mungachite Kuti Mukhale Wosangalala M’chaka Choyamba cha Ukwati

  • Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Apongozi Anu

  • Kulangiza Ana

  • Kodi Mungatani Kuti Musamakangane ndi Mwana Wanu?

  • Kugwiritsa Ntchito Ndalama Mwanzeru

(Pitani pamene palembedwa kuti, ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANTHU APABANJA NDIPONSO MAKOLO)

Buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja lili ndi nkhani zosiyanasiyana zokhudza banja, kuyambira pamene munthu akukonzekera kulowa m’banja ndiponso zokhudza kusamalira makolo okalamba.

(Bukuli likupezekanso pa webusaiti ya www.dan124.com/ny. Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > MABUKU)

 NDI YOTHANDIZA KWA MAKOLO

“Ana anga ndi ofunika kwambiri kwa ine kuposa chilichonse. Ndimafuna kuti akule bwino kuti asadzandichititse manyazi”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”—Miyambo 22:6.

NKHANI ZIMENE MUNGAPEZE PA WEBUSAITIYI

Mbali yakuti “Ana” ili ndi zithunzi zofotokoza nkhani za m’Baibulo zimene zikhoza kukuthandizani kuphunzitsa ana anu kuti akhale . . .

  • omvera

  • okoma mtima

  • ogwirizana

  • oyamikira

(Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANA)

Pali buku la mutu wakuti, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndiponso lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Mabukuwa ndi abwino kwambiri kuwerenga limodzi ndi ana anu.

(Mabukuwa akupezekanso pa webusaiti ya www.dan124.com/ny. Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > MABUKU)

NDI YOTHANDIZA ACHINYAMATA

“Ndikufuna nditapeza malangizo othandiza pa nkhani zokhudza sukulu, makolo anga, anzanga komanso atsikana. Si inenso mwana woti ndizingouzidwa zochita”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Sangalala ndi unyamata wako.”—Mlaliki 11:9.

NKHANI ZIMENE MUNGAPEZE PA WEBUSAITIYI

Mbali yakuti “Achinyamata” ili ndi nkhani komanso mavidiyo amene angakuthandizeni ngati . . .

  • mumasowa ocheza nawo

  • mukukumana ndi mavuto kusukulu

  • mwaphwanya malamulo a makolo anu

  • anzanu a kusukulu amakuvutitsani

(Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA)

Buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri lili ndi mayankho a mafunso ambiri amene achinyamata amakhala nawo.

(Bukuli likupezekanso pa webusaiti ya www.dan124.com/ny. Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > MABUKU)

NDI YOTHANDIZA KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUPHUNZIRA BAIBULO

“Ndikufuna nditamvetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa. Kodi ndingayambire pati?”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa.”—2 Timoteyo 3:16.

ZIMENE MUNGAPEZE PA WEBUSAITIYI

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika ndi lolondola komanso ndi losavuta kumva.

(Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > BAIBULO)

Mbali yakuti “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” ili ndi mayankho a mafunso osiyanasiyana.

(Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO)

Mungathe kugwiritsa ntchito mbali yakuti “Pemphani Munthu Woti Aziphunzira Nanu Baibulo Kwaulere” kuti mupemphe munthu wina wa Mboni kuti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere.

(Mukafika patsamba loyamba, pitani pamene palembedwa kuti “Pemphani Munthu Woti Aziphunzira Nanu Baibulo Kwaulere”)

“Ndinasiya kuwerenga Baibulo chifukwa sindinkalimvetsa. Koma nditayamba kuliphunzira pogwiritsa ntchito buku lakuti, ‘Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?’ ndinadabwa kuona kuti Baibulo ndi losavuta kumva.”—Christina.

Tsiku lililonse anthu okwana 700,000 amatsegula webusaiti ya jw.org. Inunso mungathe kuwerenga nkhani zosiyanasiyana pa webusaitiyi.