KUCHEZA NDI | HANS KRISTIAN KOTLAR
Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake
Mu 1978, katswiri wina wasayansi, dzina lake Hans Kristian Kotlar, anayamba ntchito yake pachipatala chinachake ku Norway, ndi kuchita kafukufuku wokhudza matenda a khansa komanso mmene chitetezo cha m’thupi chimagwirira ntchito. Pa nthawi yomweyi anayambanso kufufuza kuti adziwe mmene moyo unayambira. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe zokhudza chikhulupiriro chake.
N’chiyani chinakupangitsani kufuna kudziwa mmene moyo unayambira komanso chifukwa chimene Mulungu anatilengera?
Bambo anga anali Mkatolika pomwe mayi anga anali achipulotesitanti. Zimenezi zikusonyeza kuti iwo sankaganiza zoti chipembedzo choona ndi chiti, ankangoti bola kukhala ndi chipembedzo. Ndili wachinyamata, ndinkadabwa kuti Mulungu anatilengeranji anthufe. Ndinawerenga mabuku achibuda, Chihindu komanso Chisilamu kuti ndipeze yankho la funso limeneli. Pa nthawi ina, mpaka ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kudziwa zoona pa nkhaniyi.
M’ma 1970 asayansi anapeza zinthu zambiri zokhudza zamoyo zing’onozing’ono ndipo ndinayamba kuganiza kuti mwina zimenezi zithandiza kuti ndizindikire kuti moyo unayamba bwanji. Ndinachita chidwi kwambiri ndi tizinthu timene timapezeka muselo, choncho ndinaganiza zophunzira sayansi yogwiritsa ntchito tizinthu timeneti ndi zina popanga zinthu zamakono. Ndipotu aphunzitsi anga ambiri ankanena kuti moyo unayamba ndi kusintha kwa zinthu zachilengedwe, ndipo ine ndinkakhulupirira zimenezi.
N’chiyani chinakuchititsani chidwi ndi Baibulo?
Tsiku lina, azibambo awiri a Mboni za Yehova anafika pakhomo pathu. Ngakhale kuti iwo anali ansangala, ndinawayankha mwamwano kuti sindikufuna kumvetsera zonena zawo. Koma mkazi wanga atamva zimenezi anandiuza kuti: “Bambo, pamenepatu simunachite bwino. Kodi suja munkanena kuti mumafuna mutadziwa mmene moyo unayambira?” Ndinaona kuti mkazi wanga akunena zoona ndipo ndinachita manyazi. Choncho ndinathamangira a Mboni aja. Nditakambirana nawo kwa kanthawi, ndinawafunsa ngati zimene Baibulo limaphunzitsa zimagwirizana ndi sayansi.
Kodi mutawauza zimenezi, a Mboniwo anatani?
Anandisonyeza kuchokera m’Baibulo mfundo yosonyeza kuti mphamvu zonse zimene zili m’chilengedwechi zimachokera kwa Yehova. Vesi limene anawerenga limati: “Kwezani maso anu kumwamba muone. Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo? . . . Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake zoopsa, ndiponso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu, palibe imene imasowa.” * Ndinaonanso kuti n’zodziwikiratu kuti Yehova, mwini mphamvu zonse, ndi amene angachititse kuti zinthu zonse za m’chilengedwe ziziyenda mwadongosolo.
Kodi zimenezi zinakupangitsani kuti musiye kukhulupirira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina?
Ee, chifukwa pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuzindikira kuti mfundo zonse zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, zilibe umboni. Mfundozi zinangokhala zimene akatswiri asayansi anapeka. Iwo anachita zimenezi pofuna kufotokoza mmene zinthu ngati chitetezo cha m’thupi, zimagwirira ntchito ndipo ankati zoterezi zimangochitika zokha. Koma nditaphunzira kwambiri zokhudza chitetezo cha m’thupi, ndinayamba kuona kuti zimene zimachitika n’zodabwitsa kwambiri. Choncho zimene ndinapeza zinandipangitsa kuona kuti amene anayambitsa moyo ndi Mlengi wanzeru kwambiri.
Zimene ndinapeza zinandipangitsa kuona kuti amene anayambitsa moyo ndi Mlengi wanzeru kwambiri
Mungatipatse umboni wosonyeza kuti zamoyo zinachitadi kupangidwa ndi winawake?
Chitetezo cha m’thupi la munthu chimapangidwa ndi zinthu zinazake zomwe zimagwira ntchito ngati asilikali kuteteza thupi ku tizilombo toyambitsa matenda, monga mabakiteriya ndi mavailasi. Koma asilikali a m’thupi amenewa tingawagawe m’magulu awiri. Gulu loyamba, ndi la asilikali amene amateteza thupi ku tizilombo toyambitsa matenda pakangotha maola ochepa tizilomboti titalowa m’thupi. Gulu lachiwiri limayamba kulimbana ndi tizilombo patatha masiku angapo kuchokera pamene talowa m’thupi. Koma asilikali a m’gulu limeneli ndi amphamvu kwambiri ndipo amalimbana ndi kachilombo kenikeniko. Gulu lachiwiriri limathanso kukumbukira tizilombo tomwe tinalowapo m’thupi moti tizilomboti tikalowanso m’thupi, gululi limalimbana nato nthawi yomweyo. Chitetezo cha m’thupi chimagwira ntchito mogometsa kwambiri moti nthawi zambiri sitizindikira n’komwe kuti tinatenga matenda ndipo chitetezo cha m’thupi lathu chatiteteza kuti tisadwale. Chinthu chinanso chodabwitsa kwambiri ndi choti, chitetezo cha m’thupi chimatha kusiyanitsa pakati pa zinthu zoyambitsa matenda m’thupi ndi mitundu yosiyanasiyana ya maselo amene amapanga thupi lathu.
Tatiuzeni, kodi chimachitika n’chiyani tizilombo toyambitsa matenda tikalowa m’thupi mwathu?
Tizilombo toyambitsa matenda timalowa m’thupi lathu kudzera mu mpweya, chakudya, khungu komanso njira zina. Chitetezo cha m’thupi chikazindikira kuti m’thupi mwalowa tizilombo toyambitsa matenda, chimakonzekera njira zosiyanasiyana zolimbanirana ndi tizilomboto. Njira ina ikalephera kuthana ndi tizilomboto, imapangitsa kuti njira yotsatira iyambenso kulimbana nato. Mmene zimenezi zimachitikira n’zogometsa kwambiri.
Kodi tingati zimene munaphunzira pa ntchito yanu zakuthandizani kuti muzikhulupirira kwambiri Mulungu?
Ee, zandithandiza kwambiri. Mmene chitetezo cha m’thupi chimagwirira ntchito, zimachita kusonyezeratu kuti kuli Mlengi wanzeru kwambiri. Ndinganenenso kuti zimene ndaphunzira zokhudza sayansi ya zachipatala zachititsa kuti ndizikhulupirira kwambiri Baibulo. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 17:22 limati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.” Akatswiri anapeza kuti munthu akakhala kuti alibe nkhawa, chitetezo cha m’thupi mwake chimakhala chokwera. Koma akakhala kuti akuvutika maganizo ndi zinazake, chitetezo cha m’thupi mwake chimatsika.
Asayansi anzanu sakhulupirira kuti kuli Mulungu, n’chifukwa chiyani?
Pali zifukwa zosiyanasiyana. Ena, ngati mmene zinalili ndi ineyo, amachita zimenezi chifukwa choti anaphunzitsidwa kuti kulibe Mulungu. Mwina amaganiza kuti pali umboni wasayansi wosonyeza kuti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina. Koma ena sakhulupirira kuti kuli Mulungu chifukwa choti saganizira kwambiri mmene moyo unayambira. Zimenezi n’zomvetsa chisoni kwabasi. Koma zingakhale bwino ataifufuza bwinobwino nkhaniyi chifukwa zingathandize kuti adziwe zoona.
N’chiyani chinakupangitsani kuti mukhale wa Mboni za Yehova?
Ndinachita chidwi kwambiri kuona kuti a Mboni ndi anthu ansangala. * Ndinachitanso chidwi ndi zimene amakhulupirira zokhudza lonjezo la Mlengi lonena za dziko laparadaiso. Zimene amakhulupirirazi si zabodza kapena nkhambakamwa chabe, koma zili ndi umboni. *