Alimi Odziwa Kusamalira Nkhalango
ALIMI ambiri amadziwa zoti, kuti akolole zambiri amayenera kudzala pa nthawi yake komanso pamalo oyenera. Koma n’zochititsa chidwi kuti pali alimi ena amene amadzala mbewu zawo usiku ndipo amadzala akuuluka. Alimi amenewa ndi mileme ya m’nkhalango ndipo chifukwa choti imakhala yaikulu ena anaipatsa dzina loti nkhandwe zouluka. *
Mmene Milemeyi Imafesera Mbewu
Mileme imeneyi imakonda kuuluka usiku m’nkhalango n’kumadya zipatso. Imamwanso timadzi totsekemera tam’maluwa. Zitosi za milemeyi zimakhala ndi nthangala za zipatso ndipo milemeyi imagwetsa zitosizi ili m’malere. Nthangalazo zikagwera pansi, zimamera n’kukhala mitengo. Komanso milemeyi ikamamwa madzi a m’maluwa imatenga mungu, kapena kuti poleni, kuchoka m’mitengo ina kupita m’mitengo ina.
Popeza milemeyi imauluka mtunda wautali pofunafuna chakudya, imatha kufesa mbewu m’dera lalikulu. Ndiponso popeza ikamauluka imamwaza zitosi, zitosizi zimathandiza kuti nthaka ikhale yachonde ndipo mbewu zimakula bwino. Choncho kuti mitengo yambiri m’nkhalango imere, ikule bwino komanso ibale zipatso, imadalira milemeyi.
Milemeyi imaona kwambiri ndipo ili ndi luso lotha kudziwa kumene ikupita. Zimenezi n’zimene zimaithandiza kuti izitha kuuluka mtunda wautali m’nkhalango. Ngakhale pamalo a mdima, milemeyi imaona bwino kuposa anthu ndipo imatha kusiyanitsa mitundu ya zinthu. Imathanso kuuluka usiku komanso masana mosavuta.
Mmene Imaswera Komanso Kusamalira Ana
Pali mitundu ina, yomwe imapezeka ku Samoa imene imakwatirana ndipo imakhala limodzi kwa moyo wawo wonse. Kafukufuku wina anasonyeza kuti mileme ina yaikazi imasamalira bwino ana ake. Mwachitsanzo, imawanyamula kulikonse kumene ikupita komanso imawayamwitsa mpaka atakula. Mleme waukazi wa mtundu wina umatha kukhala mzamba, mleme unzake ukamaswa.
Koma chomvetsa chisoni n’chakuti mileme yambiri yamtunduwu ikhoza kutheratu chifukwa anthu akuwononga nkhalango. Izi zingabweretse mavuto akulu. Mwachitsanzo, pazilumba zina za ku South Pacific pali mitengo ina yomwe singabale zipatso popanda milemeyi. Mitengoyi imadalira milemeyi kuti itenge poleni pamaluwa a mtengo wina kupita pamtengo wina. Apatu taona kuti milemeyi ndi yofunika kwambiri chifukwa imathandiza kuti nkhalango zisathe.
^ ndime 2 Milemeyi imapezeka ku Africa, Asia, Australia ndi madera ena kuzilumba za m’nyanja ya Pacific.