ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Zifaniziro
Anthu ambiri amakhala ndi zifaniziro ndipo amaziona kuti n’zofunika kwambiri polambira. Koma kodi Baibulo limavomereza zimenezi? Kodi Mulungu amasangalala nazo?
Kodi Ayuda okhulupirika akale ankagwiritsira ntchito zifaniziro polambira?
“Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cham’madzi a padziko lapansi. Usaziweramire kapena kuzitumikira.”—Ekisodo 20:4, 5.
M’Malemba Achiheberi, omwe ena amati Chipangano Chakale, muli mavesi ambiri amene amaletsa kugwiritsa ntchito zifaniziro polambira.
ZIMENE ANTHU AMANENA
Buku lina la Akatolika limanena kuti Ayuda anali ndi zifaniziro zambiri zimene ankazigwiritsa ntchito polambira ndipo “ankazigwadira komanso ankaziona kuti n’zofunika kwambiri.” (New Catholic Encyclopedia) Bukuli linati chitsanzo cha zimenezi ndi zokongoletsera zomwe zinajambulidwa mochita kugoba pamakoma a kachisi yemwe anali ku Yerusalemu. Zinthu zimenezi ndi monga zithunzi za zipatso, za maluwa komanso za nyama.—1 Mafumu 6:18; 7:36.
ZIMENE MUYENERA KUDZIWA
Zimene bukuli linanenazi si zoona. Ayuda okhulupirika sankagwiritsa ntchito zinthu zogobazi polambira komanso sankazilemekeza mwapadera. Ndipotu palibe vesi lililonse m’Baibulo limene limanena kuti Aisiraeli okhulupirika ankagwiritsa ntchito zifaniziro polambira.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Kudzera mwa mneneri Yesaya, Mulungu anati: “Sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense kapena kupereka ulemerero wanga kwa zifaniziro zogoba.”—Yesaya 42:8.
Kodi Akhristu oyambirira ankagwiritsa ntchito zifaniziro polambira?
“Pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano? . . . Musakhudze chinthu chodetsedwa.”—2 Akorinto 6:16, 17.
Buku lina linati: “Akhristu oyambirira sankagwirizana ndi maganizo oti m’tchalitchi muzikhala zifaniziro. Iwo ankaona kuti kugwadira zinthu zimenezi kapena kuzigwiritsa ntchito popemphera, n’chimodzimodzi kulambira mafano.”—History of the Christian Church.
ZIMENE ANTHU AMANENA
Buku la Akatolika lija linanenso kuti: “Pali umboni wonse woti Akhristu oyambirira ankagwiritsa ntchito zifaniziro polambira. Umboni wa zimenezi ndi mmene manda awo ankaonekera. Mandawa ankakhala ndi zifaniziro za zinthu zosiyanasiyana zopangidwa mwaluso zedi. . . . Ngakhalenso anthu ena otchuka a pa nthawiyo ankakongoletsa nyumba zolambirira komanso manda awo ndi zifaniziro zoterezi. *
ZIMENE MUYENERA KUDZIWA
Manda oyambirira kupezeka ndi zifaniziro anali a m’zaka za m’ma 200 C.E. Apa n’kuti patatha zaka pafupifupi 200 kuchokera pamene Yesu anamwalira. Choncho anthu amene buku la Akatolika lija linanena kuti anali Akhristu oyambirira sanali Akhristu oyambirira enieni a m’nthawi ya atumwi, omwe amatchulidwa m’Malemba Achigiriki chomwe ena amati Chipangano Chatsopano. Kupezeka kwa zifaniziro m’manda akalewo kukungosonyeza kuti pomafika m’zaka za m’ma 200 C.E., Akhristu a mpatuko anali atayamba kutsatira miyambo yachikunja n’kumagwiritsa ntchito zifaniziro. Ankachita zimenezi n’cholinga choti akope anthu kuti alowe m’chipembedzo chawo. *
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Thawani kupembedza mafano.”—1 Akorinto 10:14.
Kodi tizigwiritsa ntchito zifaniziro ngati zotithandiza polambira Mulungu?
“Inu ana okondedwa, pewani mafano.”—1 Yohane 5:21.
Baibulo limaletsa kugwiritsa ntchito zifaniziro polambira. N’chifukwa chake a Mboni za Yehova sagwiritsa ntchito zifaniziro polambira komanso sakhala ndi zinthu zimenezi pamalo awo olambirira kapena m’nyumba mwawo n’cholinga choti azizigwiritsa ntchito polambira.
ZIMENE ANTHU AMANENA
Buku la Akatolika lija linanenanso kuti: “Popeza munthu amagwiritsa ntchito chifaniziro polambira chinthu chimene chifanizirocho chikuimira, n’zothekanso kulambira chifanizirocho m’malo mwa chinthucho.”
ZIMENE MUYENERA KUDZIWA
Pamene Yesu ankaphunzitsa otsatira ake mmene angapempherere, sanawauze kuti azigwiritsa ntchito zifaniziro. Ndipotu palibe vesi lililonse m’Chipangano Chatsopano lomwe limanena kuti tizigwiritsa ntchito zifaniziro polambira.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.”—Mateyu 4:10.
^ ndime 13 Mawu oti zifaniziro akuimira zinthu monga zipirala, zithunzi, mafano komanso zizindikiro zimene anthu amagwiritsa ntchito polambira.
^ ndime 14 Kugwiritsa ntchito zifaniziro polambira kunali kofala pakati pa anthu akale a ku Iguputo, Girisi, India ndi madera ena.