Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Matenda a Muubongo

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Matenda a Muubongo

Mayi wina wa ku South Africa, dzina lake Claudia yemwe anamupeza ndi matenda a muubongo, anati: “Atangondiuza kuti ndili ndi matendawa, ndinkangoona ngati ndifa basi. Ndinkada nkhawa kwambiri ndikaganizira zoti anthu odwala matendawa amasalidwa.”

Mark, yemwe ndi mwamuna wa Claudia, anati: “Zinanditengera nthawi kuti ndivomereze zoti mkazi wanga wapezeka ndi matenda a muubongo. Koma kenako ndinazindikira kuti chofunika kwambiri ndi kumuthandiza komanso kumusamalira.”

KODI mungamve bwanji inuyo kapena munthu amene mumam’konda atapezeka ndi matenda a muubongo? N’zodziwikiratu kuti zingakhale zowawa kwambiri. Koma ubwino wake ndi woti matendawa ali ndi mankhwala. Tiyeni tione zinthu zingapo zomwe zingakuthandizeni kudziwa zambiri za matendawa.

Dziwani Zambiri za Matendawa

Bungwe loona za umoyo padziko lonse linati: “Matenda a muubongo amagwira anthu ambirimbiri padziko lonse ndipo amene amavutika si wodwala yekhayo. Achibale ndi anzake a wodwalayo amavutikanso. Munthu mmodzi pa anthu 4 alionse amadwala matendawa. Kuvutika maganizo ndi amodzi mwa matenda a muubongo omwe anthu ambiri amadwala padziko lonse. Ena mwa matenda a muubongowa, omwenso ndi oopsa kwambiri, ndi monga kusokonezeka maganizo komanso misala. . . . Ngakhale kuti matenda a muubongo ndi ofala, anthu ambiri odwala matendawa sadziwa, salandira thandizo loyenera ndipo ena amasalidwa.”

Bungwe loona za umoyo padziko lonse linanenanso kuti, anthu ambiri omwe ali ndi matenda a muubongo sapita kuchipatala kukalandira thandizo chifukwa choopa kuti anthu akadziwa kuti ali ndi matendawa, aziwasala.

Ngakhale kuti matenda a muubongo ali ndi mankhwala, bungwe lina loona za matendawa linati, ku United States anthu 60 pa 100 alionse komanso ana 50 pa 100 alionse azaka za pakati pa 8 ndi 15, sanalandire mankhwala a matendawa chaka chatha.

Kumvetsa Zimene Zimachitikira Odwala Matendawa N’kothandiza

Akatswiri odziwa za matenda a muubongo amati, matendawa amapangitsa kuti munthu asamaganize bwino komanso kuti azilankhula kapena kuchita chilichonse chomwe wafuna, popanda kudziletsa. Nthawi zambiri matendawa amalepheretsa munthu kuti azimvana ndi anzake komanso amapangitsa kuti munthu azichita zosalongosoka.

Matenda a muubongo sayamba chifukwa choti munthu ali ndi vuto kapena khalidwe linalake loipa

Zizindikiro za matenda a muubongo zimasiyanasiyana potengera mmene munthu alili, vuto la munthuyo komanso mmene zinthu zilili pa moyo wake. Matendawa saona nkhope. Amagwira aliyense mosatengera zaka, chikhalidwe, mtundu, chipembedzo, maphunziro, kulemera, kusauka kapenanso kuti ndi mwamuna kapena mkazi. Matenda a muubongo sayamba chifukwa choti munthu ali ndi vuto kapena khalidwe linalake loipa. Komatu munthu wodwala matendawa akalandira thandizo akhoza kuchira bwinobwino.

Mankhwala Ake

Madokotala odziwa bwino za matenda a muubongo amatha kuthandiza anthu odwala matendawa, n’kuchira bwinobwino. Koma kuti anthu oterewa akuthandizeni muyenera kupita kuchipatala kuti akakuuzeni zambiri zokhudza matenda anuwo komanso zomwe muyenera kuchita.

Munthu wodwala matendawa angachire pokhapokha ngati atatsatira malangizo omwe wapatsidwa. Nthawi zina kuti athe kuchita zimenezi ayenera kukhala womasuka kufotokozera ena za matenda akewo. Zimenezi zingathandize kuti athe kufotokozera dokotala mmene akumvera komanso zonse zomwe zikumuchitikira. Izi zingachititse kuti dokotalayo amuthandize kumvetsa bwino zokhudza matendawo. Angamuuzenso zimene ayenera kuchita komanso kumulimbikitsa kuti asasiye kulandira thandizo. Pokaonana ndi dokotalayo ndi bwino kupita ndi mnzake kapena wachibale kuti azimuthandiza komanso kumulimbikitsa.

Anthu ambiri odwala matenda a muubongo akamvetsa bwino zokhudza matendawa komanso akatsatira malangizo onse amene dokotala wawapatsa, amachira. Mark yemwe tamutchula koyamba uja anati: “Mkazi wanga asanamupeze ndi matenda a muubongo, sitinkadziwa zambiri za matendawa. Koma atamupeza nawo, tinamvetsa bwino zokhudza matendawa. Tinazindikiranso kuti tisamadere nkhawa kwambiri za mawa, koma tizingoyesetsa kuthana ndi vuto lomwe lilipo pa nthawiyo. Madokotala, anzathu komanso achibale atithandiza kwambiri.”

Muyenera kupita kuchipatala kukaonana ndi dokotala wodziwa bwino za matenda anuwo kuti akakuuzeni zambiri zokhudza matendawo komanso zomwe muyenera kuchita

Claudia nayenso anati: “Atandiuza kuti andipeza ndi matendawa, ndinangomva ngati ndalandidwa ufulu wonse. Koma patapita nthawi ndinasiya kukhala ndi maganizo amenewa. Ngakhale kuti matendawa amapangitsa kuti tisamakwanitse kuchita zinthu zina, taona kuti n’zotheka kuthetsa mavuto ena omwe poyamba tinkaona ngati ndi osatheka kuwathetsa. Chinanso chomwe chimatithandiza n’choti, timayesetsa kutsatira malangizo omwe madokotala amatipatsa, timayesetsa kumacheza ndi anthu ena komanso kuti tisamangokhalira kudera nkhawa za matendawa.”

Kupeza Nthawi Yochita Zinthu Zauzimu N’kothandiza

Baibulo silinena kuti kuchita zinthu zauzimu kungapangitse kuti munthu achire matenda ake. Komabe pali anthu ambiri omwe amalimbikitsidwa ndi zimene Baibulo limanena. Mwachitsanzo, limatiuza kuti Mlengi wathu wachikondi amafunitsitsa kuthandiza anthu “a mtima wosweka” komanso ‘a mtima wachisoni.’—Salimo 34:18.

Ngakhale kuti Baibulo si buku la zaumoyo, lili ndi malangizo omwe angatithandize kuchepetsa nkhawa komanso kudziwa zochita tikadwala. Lingatithandizenso kukhala ndi chiyembekezo choti m’tsogolomu padzikoli sipadzakhalanso matenda kapena mavuto alionse. Baibulo limati: “Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva. Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.”—Yesaya 35:5, 6.

 

^ ndime 32 Galamukani! sisankhira anthu mankhwala. Mkhristu aliyense ali ndi udindo woonetsetsa kuti chithandizo cha mankhwala chomwe walandira si chotsutsana ndi mfundo za m’Baibulo.

^ ndime 40 Malangizo ena othandiza mungawapeze m’nkhani yakuti, “Kodi Mungatani Ngati Mukuvutika Maganizo?” mu Galamukani! ya May 2014.