NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI ANA A MASIKU ANO SAFUNA KUUZIDWA ZOCHITA?
Kodi Malangizo Abwino Olerera Ana Mungawapeze Kuti?
KUNENA zoona, kulera ana si ntchito yamasewera. Koma kulephera kupereka chilango kwa ana pomwe akufunika chilango, kumangowonjezera mavuto. Zili choncho chifukwa kusalangiza ana kumachititsa kuti ana asamamvere makolo ndipo izi zimapangitsa kuti makolowo azivutika. Kumachititsanso kuti ana asamadziwe zoyenera kuchita, ndipo zimenezi zimawasokoneza.
Koma makolo akamalangiza bwino ana awo, anawo amaona zinthu moyenera komanso amakhala ndi khalidwe labwino. Kulangiza ana kumathandiza kuti anawo aziona kuti ali ndi owayang’anira. Kuwamathandizanso kuti adzakhale anthu odalirika akadzakula. Koma kodi makolo angapeze kuti malangizo abwino olerera ana?
Malangizo Abwino Olerera Ana Amapezeka M’Baibulo
A Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magaziniyi, amakhulupirira kuti Baibulo ndi ‘lopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza.’ (2 Timoteyo 3:16) Baibulo lili ndi mfundo zothandiza kwambiri pa nkhani yolera ana ndipo ndi losiyana kwambiri ndi mabuku a malangizo olerera ana. Taonani zitsanzo zotsatirazi.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.”—Miyambo 22:15.
Ngakhale kuti ana amakhala ndi makhalidwe abwino monga kuganizira ena komanso kukoma mtima, nthawi zambiri amachita zinthu mopanda nzeru. Choncho amafunika kuwalangiza. (Miyambo 13:24) Mukamayesetsa kulangiza ana anu, zingakhale zosavuta kuti mukwaniritse bwino udindo wanu monga kholo.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Usam’mane chilango mwana.”—Miyambo 23:13, mawu a m’munsi.
Musamalephere kulangiza ana kapena kuwapatsa chilango poopa kuti angakhumudwe kapena poganiza kuti akakula angadzayambe kudana nanu. Mukamapereka malangizo oyenera kwa mwana wanu, mwanayo angaphunzire kuti asamakhumudwe anthu akamudzudzula. Zimenezi zingadzamuthandize m’tsogolo.—Aheberi 12:11.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”—Mwachibadwa makolo amafuna kuteteza ana awo. Koma muyenera kusamala. Mwachitsanzo, mwana wanu akachitira zoipa aphunzitsi ake kapena munthu wina, musamamuikire kumbuyo kapena kumuteteza ku zotsatira za khalidwe lake loipa. Kuchita zimenezi n’kumuwononga. Muziona kuti anthu amene akudandaula kuti mwana wanu wawachitira zoipa, akhoza kukuthandizani kudziwa mmene mungamulangizire. Mukamachita zimenezi ndiye kuti mukuthandiza mwanayo kuti azilemekeza anthu amene ali ndi udindo, kuphatikizapo inuyo.—Akolose 3:20.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Mwana womulekerera adzachititsa manyazi mayi ake.”—Miyambo 29:15.
Muzilangiza ana anu mwachikondi, muzichita zimene mwanena komanso muziwapatsa chilango choyenera
N’zoona kuti makolo sayenera kuchitira nkhanza ana awo. Koma sayeneranso kumangolekerera anawo. Buku lina linati: “Ana amene makolo awo amangowalekerera, sazindikira kuti makolo ali ndi udindo wowauza zochita.” (The Price of Privilege) Mukamalephera kuuza mwana wanu zochita, mwanayo amatenga udindowo n’kuyamba kukuuzani zochita. Zimenezi zingabweretse mavuto kwa mwanayo komanso kwa inuyo.—Miyambo 17:25; 29:21.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”—Mateyu 19:5.
Baibulo limanena kuti mwamuna ndi mkazi ayenera kukwatirana asanabereke ana. Ndipotu makolo amakhalabe limodzi ana awowo akakula n’kuchoka panyumba. (Mateyu 19:5, 6) Zimenezi zikusonyeza kuti udindo wolera mwana uyenera kubwera pambuyo pa udindo wanu monga munthu wapabanja. Mukasemphanitsa zinthu n’kuika udindo wosamalira mwana poyamba, mwanayo amayamba kudziona kuti ndi wofunika kwambiri. Amayamba ‘kudziganizira kuposa mmene ayenera kudziganizira.’ (Aroma 12:3) Mwamuna kapena mkazi akamaona kuti ana ndi ofunika kwambiri kuposa mnzakeyo, angachititse kuti chikondi chichepe m’banja lawo.
Mfundo Zothandiza Makolo
Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni polera ana.
Muziwalangiza mwachikondi. “Musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.”—Akolose 3:21.
Muzichita zimene mwanena. “Mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”—Mateyu 5:37.
Muziwapatsa chilango choyenera. “Ndidzakuwongolera pa mlingo woyenera.”—Yeremiya 30:11. *
^ ndime 21 Kuti mudziwe zambiri, pitani pa webusaiti yathu ya jw.org/ny. Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANTHU APABANJA NDIPONSO MAKOLO. Pamenepa mungapezepo nkhani monga yakuti, “Zimene Mungachite Mwana Akayamba Kuvuta” ndi yakuti, “Zimene Mungachite Kuti Mwana Wanu Azikumverani.”