Kodi Mungathandize Bwanji Mnzanu Kapena Wachibale Akadwala?
Mayi ena dzina lawo a Maribel ananena kuti: “Bambo anga atatsala pang’ono kutulutsidwa m’chipatala, tinapempha adokotala kuti atiuze zotsatira za magazi awo. Adokotalawo anatiuza kuti, atayeza, sanapeze vuto lililonse. Komabe anaona kuti angowayezanso kuti atsimikizire. Atachita zimenezi, anadabwa kwambiri atapeza matenda moti anapepesa kwambiri n’kuitana dokotala wina wodziwa bwino za matendawo. Panopa bambo anga akupeza bwino. Ndimaona kuti tinachita bwino kukambirana ndi dokotala uja komanso kumufunsa zina ndi zina.”
Anthu ambiri amada nkhawa akauzidwa kuti agonekedwa m’chipatala kapena azipita kukaonana ndi dokotala. Koma monga zinakhalira ndi a Maribel, zimakhala bwino kwambiri wodwalayo akakhala ndi mnzake kapena wachibale woti amuthandize. Ndiye kodi mungathandize bwanji mnzanu kapena wachibale amene akudwala?
Musanakaonane ndi dokotala. Thandizani wodwalayo kulemba mmene akumvera komanso mankhwala amene sagwirizana nawo. Lembaninso mafunso amene mukuona kuti mungakafunse dokotala. Mungachitenso bwino kulemba ngati anadwalapo matendawo m’mbuyomo kapena ngati ali ndi wachibale amene anadwalapo matendawo. Ndi bwino kulemba zinthu ngati zimenezi m’malo moyembekezera kuti dokotalayo akakufunseni kapena kungoganiza kuti akudziwa kale.
Pokambirana ndi dokotala. Muzimvetsera zimene dokotala akukuuzani. Muzifunsa ngati simunamvetse ndipo musamakakamire zimene mukudziwa. Muzimupatsa mpata wodwalayo kuti azilankhulapo komanso kufunsa mafunso. Ndi bwinonso kumvetsera mwatcheru komanso kulemba zimene adokotala akunena. Mungafunsenso njira zimene madokotala amagwiritsa ntchito pothandiza munthu amene ali ndi vuto ngati la wachibale wanuyo. Zingakhalenso bwino kupempha wodwalayo kuti akaonane ndi madokotala ena m’malo mongodalira dokotala mmodzi.
Mukabwerako. Kambiranani ndi wodwalayo zimene dokotala wakuuzani. Onetsetsani kuti akumwa mankhwala motsatira malangizo a dokotala. Ndipo bwereraniko mwamsanga ngati wodwalayo sanagwirizane ndi mankhwalawo. Muzimuthandiza kuti asamangokhalira kudandaula za matenda ake ndipo muzimulimbikitsa kutsatira malangizo omwe wapatsidwa monga kupitanso kuti azikaonana ndi dokotala. Muzimuthandizanso kufufuza kuti adziwe zambiri za vuto lakelo.
Wodwala Akagonekedwa M’chipatala
Muzikhala wodekha komanso wosamala. Wodwala akamapita kuchipatala, amakhala ali ndi nkhawa. Choncho ngati inuyo mutakhala wodekha komanso wosamala, mungathandize kuti zinthu zisasokonekere. Mungachite bwino kuonetsetsa kuti mwalemba molondola mafomu akuchipatala. Muyeneranso kudziwa kuti wodwalayo ali ndi ufulu wosankha chithandizo chimene akufuna. Koma ngati wadwala kwambiri, tsatirani zimene analemberatu kapena zimene munthu amene anamusankha kuti adzamulankhulire akadzadwala, anganene. *
Muzifotokozapo maganizo anu. Muzimasuka kufotokoza maganizo anu komanso kuchita zinthu mwaulemu. Mukamachita zimenezi, ogwira ntchito m’chipatala amasamaliranso bwino wodwalayo komanso kumupatsa chithandizo chimene akufuna. M’zipatala zambiri, odwala amaonedwa ndi madokotala osiyanasiyana. Choncho mukapita kwa dokotala wina mungachite bwino kumufotokozera zimene madokotala ena ananena. Komanso popeza inu ndi amene mukudziwa bwino wodwalayo, mutha kuwafotokozera ngati akupezako bwino kapena ngati sizikusintha.
Muzilemekeza komanso kuyamikira ogwira ntchito m’chipatala. Nthawi zambiri anthu amene amagwira ntchito m’zipatala amapanikizika ndi ntchito. Choncho muzichita zinthu mowaganizira. (Mateyu 7:12) Muziwayamikira komanso muzisonyeza kuti mumawadalira. Zimenezi zingawalimbikitse kuti azigwira ntchito yawo modzipereka.
Popeza zamawa sizidziwika, ndi bwino kuti muzidziwiratu zimene mungachite komanso thandizo limene mnzanu kapena wachibale wanu angafune ngati atadwala. Mukachita zimenezi mudzasonyeza kuti ndinu bwenzi lenileni limene limathandiza pakagwa mavuto.—Miyambo 17:17.
^ ndime 8 Munthu wodwala ali ndi ufulu wosankha chithandizo cha chipatala chimene akufuna. M’mayiko ambiri mumakhala malamulo amene amaonetsetsa kuti ufulu umenewu ukutsatiridwa. Onetsetsani kuti mapepala amene wodwala analembapo zokhudza thandizo la chipatala limene amafuna, ndi olembedwa bwino. Mapepalawo ayeneranso kukhala oti alembedwa chaposachedwapa.