MUNGATANI KUTI MUZIKHALA WOSANGALALA?
Chikondi
ALIYENSE AMAFUNA KUKONDEDWA. Popanda chikondi, anthu sangakwatirane, mabanja sangalimbe komanso sitingakhale ndi anzathu. Choncho m’pomveka kuti chikondi chimathandiza kuti munthu akhale wosangalala komanso wathanzi. Koma kodi “chikondi” n’chiyani?
Chikondi chomwe tikufuna kukambirana si chapakati pa mwamuna ndi mkazi ngakhale kuti chikondi chimenechinso ndi chofunika kwambiri. Koma tikambirana za chikondi chimene chimachititsa munthu kuchita chidwi komanso kukhudzidwa ndi mmene zinthu zikuyendera pa moyo wa munthu wina. Ndipo munthu wotereyu amaika patsogolo zofuna za anthu ena m’malo mwa zofuna zake. Amasonyeza chikondichi chifukwa chotsatira mfundo m’Baibulo ndipo amakonda anthu ena kuchokera mumtima.
Mawu ochititsa chidwi ofotokoza za chikondi amati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse,. . . chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha.”—1 Akorinto 13:4-8.
Chikondi chimenechi “sichitha” chifukwa chidzakhalapo mpaka kalekale. Nthawi ikamapita, chikondichi chimathanso kulimba. Popeza kuti chimachititsa anthu kukhala oleza mtima, achifundo komanso okhululuka, tinganene kuti chikondicho “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akolose 3:14) Ndipo anthu amene amasonyezana chikondi chimenechi amakhala osangalala ndipo ubwenzi wawo umakhala wokhalitsa ngakhale kuti nthawi zina amalakwirana. Mwachitsanzo tiyeni tikambirane zokhudza banja.
CHIKONDI “CHIMAGWIRIZANITSA ANTHU MWAMPHAMVU KWAMBIRI”
Yesu Khristu anaphunzitsa mfundo zofunika kwambiri zokhudza banja. Mwachitsanzo iye ananena kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi. . . Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mateyu 19:5, 6) Tsopano tiyeni tikambirane mfundo ziwiri zimene Yesu anazitchulazi.
“AWIRIWO ADZAKHALA THUPI LIMODZI.” Banja ndi mgwirizano umene anthu amapanga chifukwa cha chikondi. Mwamuna ndi mkazi omwe amakondanadi amayesetsa kukhala okhulupirika ndipo sangalole kukhala “thupi limodzi” ndi mwamuna kapena mkazi wina. (1 Akorinto 6:16; Aheberi 13:4) Anthu okwatirana amayamba kukayikirana ngati wina ndi wosakhulupirika ndipo banja lotere silingalimbe. Ngati ali ndi ana, anawo amasokonezeka kwambiri ndipo amadziona kuti alibe tsogolo, sakukondedwa komanso sakhala osangalala.
“CHIMENE MULUNGU WACHIMANGA PAMODZI.” Ukwati ndi wopatulika chifukwa anauyambitsa ndi Mulungu. Anthu okwatirana omwe amazindikira mfundo imeneyi amayesetsa kulimbitsa ukwati wawo. Akakumana ndi mavuto saona kuti njira yabwino ndi kungothetsa banjalo. M’malomwake amakondana kwambiri komanso amakhala opirira. Chikondi chotere “chimakwirira zinthu zonse,” komanso chimathandiza pothetsa mavuto. Zimenezi zimathandiza kuti okwatiranawo azikhala mogwirizana komanso mwamtendere.
Makolo akamakondana, zimathandizanso kuti ana azikhala osangalala. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Jessica anati: “Makolo anga amakondana komanso kulemekezana kwambiri. Ndikaona mmene mayi anga amasonyezera ulemu kwa bambo anga, zimandisangalatsa moti ndimafuna nditakhala ngati iwowo.”
Chikondi ndi khalidwe lalikulu la Mulungu. Ndipo Baibulo limanena kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Choncho n’zosadabwitsa kuti Yehova amatchedwanso kuti ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Nafenso tingakhale osangalala tikamayesetsa kutsanzira makhalidwe a Mlengi wathu makamaka posonyezana chikondi. Lemba la Aefeso 5:1, 2 limanena kuti: “Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo yendanibe m’chikondi.”