Mulungu Akulonjeza Kuti Dzikoli Lidzakhalanso Bwino
“Dzikoli ndi lopirira kwambiri kuposa mmene timaganizira.”
Zimenezi ndi zimene kagulu kena ka anthu ochita kafukufuku kanapeza pa nkhani yokhudza kusintha kwa nyengo. Ngati mumakhulupirira kuti kuli mlengi amene amakonda anthu, ndiye kuti zimene akatswiriwa ananenazi zakukumbutsani njira zambiri za mmene Mulungu anakonzera dzikoli kuti lizidzikonza lokha anthu akaliwononga.
Komabe tikaganizira mmene anthu awonongera dzikoli, njira zachilengedwezi pazokha si zokwanira kuti dzikoli likhalenso bwino. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti Mulungu achitapo kanthu?
Taonani malemba omwe ali m’musiwa amene akutitsimikizira kuti dzikoli lidzakhalanso bwino ndipo lidzakhalapo mpaka kalekale.
Dzikoli linalengedwa ndi Mulungu. “Pachiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1
Mulungu ndiye mwiniwake wa dziko. “Dziko lapansi ndiponso zonse zimene zili mmenemo ndi za Yehova. a”—Salimo 24:1
Mulungu anakonza dzikoli kuti lidzakhalepo mpaka kalekale. “Iye wakhazikitsa dziko lapansi pamaziko ake. Silidzasunthidwa pamalo ake mpaka kalekale.”—Salimo 104:5
Mulungu akulonjeza kuti zamoyo zimene zili m’dzikoli zidzakhalapo mpaka kalekale. “Mulungu woona, amene anaumba dziko lapansi, . . . sanalilenge popanda cholinga, koma analiumba kuti anthu akhalemo.” —Yesaya 45:18
Mulungu akulonjeza kuti anthu adzakhala padzikoli mpaka kalekale. “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.”—Salimo 37:29
Mulungu anakonza dzikoli kuti anthu azisangalala ndi moyo popanda kuliwononga. Baibulo linaneneratu kuti pa nthawi yake, Yehova Mulungu adzawononga anthu onse odzikonda amene akuwononga dzikoli.—Chivumbulutso 11:18
Baibulo limalonjeza kuti pambuyo pa zimenezi, Mulungu adzakonza dzikoli kuti likhale paradaiso wokongola kwambiri “n’kukwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse.”—Salimo 145:16
a Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.