Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu aulemu ali ngati simenti yomangira nyumba, akhoza kulimbitsa banja lanu

MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

3: Kulemekezana

3: Kulemekezana

ZIMENE ZIMACHITIKA

Mwamuna ndi mkazi amene amalemekezana, amakondanabe ngakhale pamene asemphana maganizo. Buku lina linanena kuti: “M’banja lotere palibe amene amakakamira maganizo ake koma amakambirana kuti athetse kusamvana kulikonse komwe kungakhalepo. Wina akamafotokoza maganizo ake, mnzakeyo amamvetsera mwaulemu n’kupeza njira yabwino yothetsera nkhaniyo.”​—Ten Lessons to Transform Your Marriage.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.”​—1 Akorinto 13:4, 5.

A Micah ananena kuti: “Ndimaona kuti kulemekeza mkazi wanga kumatanthauza kuti ndizimuona kuti ndi wofunika. Ndipo ndimapewa kuchita chilichonse chomwe chingamukhumudwitse komanso kusokoneza banja lathu.”

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Ngati mwamuna ndi mkazi wake salemekezana, amangokhalira kuimbana milandu, kunyozana kapena kulankhulana mawu achipongwe. Ndipotu akatswiri anapeza kuti zimenezi ndi zizindikiro zosonyeza kuti banjalo likhoza kutha.

A Brian ananena kuti: “Kulankhula monyoza, mawu achipongwe kapena nthabwala zosafunika, zingachititse kuti mkazi wanu asiye kukudalirani komanso kukukhulupirirani. Ndipo pamapeto pake banjalo limasokonezeka.”

ZIMENE MUNGACHITE

YESANI KUCHITA IZI

Kwa mlungu umodzi, ganizirani zimene mwalankhula komanso kuchita. Kenako mudzifunse kuti:

  • Kodi mwamuna kapena mkazi wanga ndamuyamikirako kangati mlungu uno? Nanga ndi kangati kamene sindinamulankhule bwino?

  • Kodi ndachitapo zotani posonyeza kulemekeza mwamuna kapena mkazi wanga?

ZOTI MUKAMBIRANE

  • Kodi mungakonde kuti mnzanuyo achite zotani kapena kukulankhulani mawu otani kuti mumve kuti wakupatsani ulemu?

  • Kodi mumaona kuti mnzanuyo sanakulemekezeni akachita zinthu zotani kapena akakulankhulani mawu otani?

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI

  • Lembani zinthu zitatu zomwe mungafune kuti mnzanuyo akuchitireni kuti mumve kuti wakulemekezani. Ndipo nayenso alembe zimene angakonde. Kenako sinthanani zomwe mwalembazo ndipo aliyense aziyesetsa kuchita zimene mnzakeyo akufuna.

  • Lembani makhalidwe abwino a mnzanuyo omwe amakuchititsani chidwi. Ndipo muuzeni mmene mumamvera akamasonyeza makhalidwewo.

A Megan ananena kuti: “Ndimasonyeza kuti ndimalemekeza mwamuna wanga ndi zimene ndimamuchitira ndipo ndimafuna kuti azisangalala. Sizichita kufuna kuti umuchitire chinthu chachikulu kuti adziwe zoti umamulemekeza. Ngakhale tinthu ting’onoting’ono timakhala tokwanira.”

Apa tingati mfundo ndi yoti, mwamuna kapena mkazi wanu aziona yekha kuti mumamulemekeza, osati mmene inuyo mukumvera kuti mumamulemekeza.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.”​—Akolose 3:12.