Zimene Asayansi Sangatiuze
Zikuoneka kuti asayansi anaphunzira zambiri zokhudza chilengedwechi. Komabe, pali mafunso ambiri ofunika omwe sangakwanitse kuyankha.
Kodi asayansi amafotokoza mmene chilengedwe komanso zamoyo zinayambira? Yankho lachidule ndi lakuti ayi. Anthu ena amanena kuti asayansi omwe anaphunzira zakuthambo ndi amene angafotokoze mmene chilengedwechi chinayambira. Komabe pulofesa wina wa ku koleji ya Dartmouth dzina lake Marcelo Gleiser, yemwe amakayikira kuti kuli Mulungu, ananena kuti: “Sitinakwanitsepo kufotokoza mmene chilengedwe chinayambira.”
Komanso pofotokoza mmene moyo unayambira, nkhani ina ya m’magazini ya sayansi (Science News) inanena kuti: “N’zosatheka kudziwa zoona zake za mmene moyo unayambira padzikoli. Miyala komanso zinthu zina zakale zimene zinakwiririka munthaka zomwe zikanasonyeza mmene zinthu zinalili m’masiku oyambirira a dzikoli, zinasiya kupezeka.” Zimenezi zikusonyeza kuti pofika pano sayansi yalephera kupeza yankho la funso lakuti, Kodi chilengedwe komanso zamoyo zinayamba bwanji?
Koma mwina mukhoza kudabwa kuti, ‘Ngati zamoyo zinachita kulengedwa, ndiye ndi ndani amene anazilenga?’ Mwinanso munadzifunsapo mafunso awa: ‘Ngati kulidi Mlengi yemwe ndi wanzeru komanso wachikondi, n’chifukwa chiyani amalola kuti anthu omwe anawalenga yekha azivutika? N’chifukwa chiyani amalola kuti anthu azilambira m’njira zosiyanasiyana? N’chifukwa chiyani amalola kuti anthu ena amene amati amamulambira azichita zinthu zoipa zambiri?’
Sayansi singathe kupeza mayankho a mafunso amenewa. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti simungapeze mayankho omveka bwino. Ndipotu anthu ambiri anapeza mayankho m’Baibulo amene anawafika pamtima.
Ngati mungakonde kudziwa chifukwa chake asayansi ena omwe anaphunzira Baibulo amakhulupirira kuti kuli Mlengi, pitani pa jw.org. Fufuzani mawu akuti “zokhudza mmene moyo unayambira.”