Kodi Mungafufuze Bwanji?
“Zinthu za m’chilengedwe zinangokhalapo zokha.”—Anatero akatswiri a sayansi Stephen Hawking ndi Leonard Mlodinow, mu 2010.
“Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Limatero Baibulo pa Genesis 1:1.
Kodi chilengedwechi komanso zamoyo, zinachita kulengedwa ndi Mulungu kapena zinangokhalapo zokha? Mawu ali pamwambawa a akatswiri awiri asayansi komanso mawu oyambirira a m’Baibulo, akusonyeza kuti funsoli lili ndi mayankho awiri osiyana kwambiri. Yankho lililonse lili ndi anthu amene amaliikira kumbuyo. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri sadziwa zimene ayenera kukhulupirira. Anthu akhala akupereka maganizo osiyanasiyana kudzera m’mabuku otchuka komanso mitsutso.
N’kutheka kuti aphunzitsi anu anakutsimikizirani kuti zinthu zonse m’chilengedwechi, zinangokhalapo zokha ndipo sizinachite kulengedwa. Koma kodi aphunzitsi anuwo anaperekadi umboni wosonyeza kuti kulibe Mlengi? Komanso n’kutheka kuti munamvapo atsogoleri a chipembedzo akunena kuti kuli Mlengi, koma kodi anakupatsani umboni wa zimene ankanenazo? Kapena anangokuuzani kuti muzikhulupirira chifukwa chakuti ndi zimene amaphunzitsa?
N’zosakayikitsa kuti munadzifunsapo funso limeneli ndipo mwina mumaona kuti palibe amene anganene motsimikiza kuti kuli Mlengi. N’kutheka kuti mumakhalanso ndi funso lina lakuti: Kodi kupeza yankho lake n’kofunikiradi?
Magazini ya Galamukani! ino, ifotokoza zimene zachititsa anthu ambiri kukhulupirira kuti kuli Mlengi. Ifotokozanso chifukwa chake n’zofunika kudziwa yankho la funso lakuti, kodi moyo unayamba bwanji padziko lapansili?