Zimene Zinthu Zakuthambo Zimatiuza
Akatswiri ofufuza zakuthambo amagoma ndi mmene zinthu zilili m’chilengedwechi. Ndipo akupitirizabe kupanga zipangizo zabwino zowathandiza pa ntchito yofufuzayo. Ndiye kodi apeza zotani?
Zinthu zakuthambo zinayalidwa mwadongosolo. Nkhani ina imene inalembedwa m’magazini ina ya sayansi (Astronomy) inanena kuti: “Milalang’amba inayalidwa mwadongosolo kwambiri, sinangomwazikana mwachisawawa.” Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Akatswiri asayansi amakhulupirira kuti zimenezi zinatheka chifukwa cha zinthu zina zosaoneka zimene amazitchula kuti dark matter. Zinthu zimenezi amati “zili ngati akatawala * osaoneka pamene pamatsamira . . . milalang’amba, magulu a milalang’amba komanso magulu akuluakulu a milalang’amba.”
Kodi zinatheka bwanji kuti zinthu zakuthambo ziyalidwe mwadongosolo chonchi? Kodi tingati n’zotheka kuti zinangoyalika zokha popanda winawake wozichititsa? Taonani zimene ananena malemu Allan Sandage, amene ankakhulupirira Mulungu, yemwe anthu amati “anali mmodzi wa akatswiri odziwa bwino kwambiri zinthu zakuthambo amene anakhalapo zaka za m’ma 1900.”
Iye ananena kuti: “Ndimaona kuti n’zovuta kwambiri kuti zinthu zoyalidwa bwino chonchi zingochitika mwangozi. Ziyenera kuti zinayalidwa ndi winawake.”
Zinthu zakuthambo zinakonzedwa m’njira yakuti padzikoli pazikhala zamoyo. Taganizirani mfundo yakuti dzuwa limatentha mokhazikika pa mlingo winawake. Zikanakhala kuti mphamvu imene imachititsa zimenezi inali yofooka, dzuwa silikanapangika n’komwe. Mphamvu imeneyo ikanakhala yochuluka kwambiri, dzuwa likanakhala litatha kalekale.
M’zinthu zakuthambo muli mphamvu zinanso zosiyanasiyana zimene zinachunidwa bwino kuti padziko lapansi pazitha kukhala zamoyo. Wolemba zasayansi wina dzina lake Anil Ananthaswamy, ananena kuti ngakhale imodzi mwamphamvu zimenezi ikanakhala kuti sili mmene ililimu, ndiye kuti “nyenyezi, mapulaneti komanso milalang’amba, sizikanapangika. Zinthu zamoyo sizikanakhalapo n’komwe.”
M’chilengedwechi muli malo abwino kwambiri okhalamo anthu. Dziko lapansi lili ndi mpweya wamlengalenga wokwanira, madzi okwanira komanso mwezi waukulu bwino kuti uzithandiza dziko lapansi kuti lisamasunthe. Magazini ina inanena kuti: “Asayansi anapeza kuti mmene zinthu zopanda moyo komanso zamoyo zilili padzikoli, zimathandiza kuti dzikoli likhale malo okhawo amene anthu angakhalemo.” *—Magazini ya National Geographic.
Wolemba wina ananena kuti dzuwa ndi mapulaneti ake “zili kumbali kwambiri” poyerekezera ndi nyenyezi zina zonse mu mlalang’amba wathuwu. Komatu kutalikirana ndi nyenyezi zina kumeneku, n’kumene kumachititsa kuti padziko lapansi pazitha kukhala zinthu zamoyo. Zikanakhala zoopsa kwambiri kwa zinthu zamoyo zikanakhala kuti tili pafupi kwambiri ndi nyenyezi zina, ngati pakatikati pa mlalang’amba wathuwu kapena kumapeto kwake. Komatu asayansi ena amanena kuti malo amene pali dziko lapansili ndi “okhawo amene pangakhale zamoyo mu mlalang’ambawu.”
Katswiri wina wasayansi dzina lake Paul Davies ananena mawu awa kuchokera pa zimene amadziwa zokhudza zinthu zakuthambo komanso malamulo amene zimayendera: “Sindingakhulupirire kuti zinangochitika mwadzidzidzi kuti tipezeke padzikoli kapena kuti tinangopezekapo mwangozi chabe. . . . Tikuyenera kukhala pano.” Katswiriyu sakhulupirira kuti Mulungu analenga chilengedwechi komanso anthu, koma kodi inuyo mukuganiza bwanji? Zinthu zakuthambo komanso dziko lapansili, zimaoneka kuti zinapangidwa m’njira yoti zizithandiza kuti zamoyo zikhalepo. Kodi n’kutheka kuti zili choncho chifukwa chakuti winawake anachita kuzipanga?
^ ndime 3 Katawala ndi mtundu wina wa makwerero amene amagwiritsidwa ntchito pa zomangamanga pofuna kufika pamwamba.
^ ndime 8 Cholinga cha nkhani ya m’magaziniyi sichinali kufotokoza kuti Mulungu analenga dziko lapansi komanso anthu. Koma inkangofotokoza kuti dzikoli ndi malo abwino kwambiri oti anthu azikhalamo.